Mphu. 32 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za madyerero

1Ngati akusankha kuti ukhale woyang'anira

pa phwando, usapupulume.

Khala monga ena onse,

usamale za iwo poyamba, kenaka ukhale pansi.

2Utatsiriza ntchito zako zonse,

ukakhale pamalo pako.

Motero udzakondwa poona chimwemwe chao,

ndipo iwowo adzakuyamika chifukwa cha

makhalidwe ako abwino.

3Ngati ndiwe nkhalamba ulankhule,

chifukwa ndi chinthu chokuyenerera.

Koma polankhula uzilankhula zomveka,

ndipo usadule zoimbaimba.

4Ngati pali zoimbaimba, usalankhulelankhule,

si nthaŵi yodziwonetsa kuti ndiwe munthu wanzeru.

5Monga momwe umakhalira mwala wa rubi pa

mphete yagolide,

ndi m'menenso liliri gulu la anthu oimba

pa phwando.

6Monga momwe umakhalira mwala wa emeradi

pa mphete yagolide,

ndi m'menenso iliri nyimbo yokoma

pakumwa vinyo wabwino.

7Ngati ndiwe mnyamata,

ulankhule ngati nkofunika.

Koma usalankhule kopitirira kaŵiri

ndipo pokhapokha atakupempha.

8Ukambe mwachidule,

unene zambiri ndi mau ochepa,

uwoneke kuti ndiwe wodziŵa,

koma wosafuna kulankhula.

9Pakati pa anthu otchuka

usakhale ngati uli ndi anzako

olingana nawo,

ndipo pamene wina akulankhula,

iwe usaikepo mau achibwana.

10Monga mphezi imayamba kung'anima bingu lisanagunde,

momwemonso mbiri ya munthu wabwino imamveka,

iye tisanamuwone.

11Pa phwando uzichoka nthaŵi yabwino,

usamakhala wotsirizira.

Ulunjike ku nyumba, osaimaimanso ai.

12Kumeneko ungathe kudzisangalatsa,

ungathe kuchita zomwe ukufuna,

koma usachimwe polankhula zodzikuza.

13Tsono pa zonsezi usaiŵale kuthokoza Mlengi wako

amene amakupatsa madalitso ochuluka.

Za kuwopa Mulungu

14Munthu woopa Ambuye amalandira malango ake.

Anthu odzuka m'maŵa kuti achite kufuna kwa Ambuye,

Mulungu amaŵakomera mtima.

15Munthu wokonda Malamulo adzapezamo chakudya

choti nkukhuta,

koma munthu wachiphamaso amaphunthwa nawo Malamulowo.

16Munthu woopa Ambuye adzadziŵa chilungamo

ndipo ntchito zake zidzaŵala ngati nyale.

17Munthu wochimwa amakana kumdzudzula,

amafunafuna zifukwa zopitirizira mkhalidwe wake.

18Munthu wanzeru sanyozera malangizo a anzake,

koma munthu wamwano ndi wodzikuza alibe mantha konse.

19Usachite zinthu usanaganize,

ndipo pambuyo pake sudzadandaula.

20Usayende pa njira yoipa,

ndipo sudzakhumudwa pa mwala.

21Usamayende mosachenjera

pa njira yosalala,

22uzipenyetsetsa kumene ukupita.

23Uzisamala bwino pa zonse zimene uchita

chifukwa kutero ndiye kutsata Malamulo.

24Munthu wokhulupirira Malamulo amamvera mau ake.

Munthu wokhulupirira Ambuye sadzaona zomupweteka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help