1“Pofuna kumpatula Aroni ndi ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira, uchite izi: Utenge ng'ombe yamphongo ndi nkhosa zamphongo ziŵiri zopanda chilema.
2Utengenso buledi wosafufumitsa, makeke osatupitsa, osakaniza ndi mafuta, ndiponso mitanda ya buledi yopsapsalala yopaka mafuta. Zimenezi uzipange ndi ufa wosalala watirigu.
3Uziike m'lichero, ndipo ubwere nazo kwa Ine, pamene ukupereka nsembe ng'ombe yamphongo ija ndi nkhosa zija.
4Ubwere naye Aroni ku khomo la chihema chamsonkhano, pamodzi ndi ana ake aamuna, ndipo onsewo uŵayeretse m'madzi.
5Tsono utenge zovala zija ndi kumuveka Aroni mwinjiro ndi mkanjo wautali wovala pamwamba pa efodi, ndiponso chovala chapachifuwa. Ndipo umange lamba woluka mwaluso uja m'chiwuno mwake.
6Umuveke nduŵira kumutu kwake, ndi duŵa lopatulika lija panduŵirapo.
7Tsono utenge mafuta odzozera aja ndi kuŵatsanyulira kumutu kwake kuti umdzoze.
8Kenaka ubwere ndi ana ake aamuna, ndipo uŵaveke miinjiro.
9Uŵavekenso lamba m'chiwuno mwao ndi nduŵira. Motero iwoŵa adzakhala ansembe anga potsata lamulo langa losatha. Umu ndimo m'mene umdzozere Aroni ndi ana ake aamuna.
10“Pambuyo pake ubwere ndi ng'ombe yamphongo pakhomo pa chihema chamsonkhano. Tsono Aroni ndi ana ake asanjike manja ao pamutu pa ng'ombeyo.
11Kenaka muiphe ng'ombeyo pamaso pa Chauta, pa khomo la chihema chamsonkhano.
12Utengeko magazi a ng'ombeyo, ndipo uŵapake ndi chala chako pa nyanga za guwa. Tsono magazi otsalawo uŵatsanyulire patsinde pa guwalo.
13Pambuyo pake utenge mafuta onse okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ndiponso imso ziŵiri, pamodzi ndi mafuta ozikuta. Zonsezi uzipereke, ndipo uzitenthere pa guwalo.
14Koma nyama yake, chikumba chake ndi ndoŵe zake, ukazitenthere kunja kwa mahema. Chopereka chimenechi ndicho cha nsembe yopepesera machimo.
15“Utenge imodzi mwa nkhosa ziŵiri zamphongo zija, ndipo Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo.
16Tsono uiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza pa mbali zonse za guwa.
17Nkhosayo uiduledule, ndipo utatsuka matumbo ndi miyendo yake, uziike mosanjikiza pamwamba pa nthuli zake ndi mutu.
18Aef. 5.2; Afi. 4.18 Ndipo upsereze nkhosa yonseyo paguwapo. Imeneyo idzakhala nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta. Idzakhala nsembe ya fungo lokoma yopereka pa moto kwa Chauta.
19“Tsono utenge nkhosa yamphongo inayo. Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo.
20Muiphe, ndipo mutengeko magazi ake ndi kupaka pa khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa khutu la ku dzanja lamanja la ana ake aamuna. Upakenso pa chala chao chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja. Magazi ena uwaze pa mbali zonse za guwa.
21Utengeko magazi otsalira pa guwa ndiponso mafuta ena odzozera, uwaze Aroni ndi zovala zake. Uwazenso ana ake ndi zovala zao. Tsono iyeyo ndi ana ake adzakhala opatulika, pamodzi ndi zovala zomwezo.
22“Nkhosa yamphongo ija utengeko mafuta ake, mchira wake wamafuta, mafuta okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ozikutawo, ndiponso ntchafu ya ku dzanja lamanja, chifukwa nkhosa imeneyi ndi nsembe ya pa mwambo wodzozera.
23M'lichero limene lili m'Nyumba ya Chauta utengeko buledi mmodzi wosafufumitsa, keke imodzi yosakaniza ndi mafuta, ndiponso buledi mmodzi wopsapsalala.
24Chakudya chonsechi uchiike m'manja mwa Aroni ndi mwa ana ake, ndipo iwowo achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa ine.
25Kenaka uchotse zonsezo m'manja mwao, ndipo uzipsereze pa guwa, pamwamba penipeni pa zopereka zija kuti zipereke fungo lokondweretsa Chauta. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza kwa Chauta.
26“Utenge nganga ya nkhosa yamphongo imene adaipha podzoza Aroni, ndipo uiweyule kuti ikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Imeneyi ndiyo idzakhala gawo lako.
27Pambuyo pake upatule zigawo za nkhosa yopereka pa mwambo wodzozera Aroni ndi ana ake, ndiye kuti nganga yoperekedwa ngati chopereka choweyula ija, ndiponso ntchafu yoperekedwa ngati chopereka choweyula ija.
28Pa zimene Aisraele azipereka, zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake nthaŵi zonse. Alandire ndiwo ansembe zonsezi zochokera pa zopereka zamtendere za Aisraele pakuti ndizo mphatso zao za Aisraele kwa Chauta.
29“Zovala za Aroni zaunsembe zidzakhale za ana ake aamuna iyeyo atafa, kuti anawo azivala zimenezo pamene akudzozedwa ndi kulandira udindo wao.
30Mwana wa Aroni womloŵera m'malo kuti akhale wansembe, azidzavala zimenezi masiku asanu ndi aŵiri, pamene akuloŵa m'chihema chamsonkhano kukatumikira m'malo oyera.
31“Tsono utenge nkhosa yamphongo yophera mwambo woloŵera unsembe, uiphike m'malo oyera.
32Ndipo Aroni ndi ana akewo adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, pamodzi ndi buledi wam'lichero uja pakhomo pa chihema chamsonkhano.
33Adzadye zonse zimene adazipereka kwa Chauta pa mwambo wopepesera machimo poŵadzoza ndi kuŵapatula. Munthu wamba asadyeko, chifukwa nzoyera.
34Nyama ikatsalako, kapena buledi akatsalako mpaka m'maŵa, utenthe. Asadye zimenezo chifukwa nzoyera.
35“Zonse zimene ndakulamulazi umchitire Aroni ndi ana ake aamuna omwe. Udzachite mwambo wakuŵapatula pa masiku asanu ndi aŵiri.
36Tsiku ndi tsiku uzipereka ng'ombe yamphongo yopepesera machimo, kuti machimowo akhululukidwe. Uyeretse guwalo pakuliperekera nsembe yopepesera machimo. Kenaka ulidzoze kuti likhale lopatulika.
37Pa masiku asanu ndi aŵiri uzipereka nsembe zoyeretsera guwalo, ndipo uzilipatula. Pambuyo pake guwalo lidzakhala loyera kwathunthu, ndipo chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.
Zopereka za tsiku lililonse(Num. 28.1-8)38“Pa guwa lansembe uziperekapo izi: nthaŵi zonse tsiku ndi tsiku, uzipereka anaankhosa aŵiri a chaka chimodzi.
39Mwanawankhosa wina uzimpereka m'maŵa, wina madzulo.
40Pamodzi ndi mwanawankhosa woyambayo, uzipereka kilogaramu limodzi la ufa wosalala watirigu wosakaniza ndi lita limodzi la mafuta abwino, ndiponso lita limodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.
41Tsono uzipereka mwanawankhosa wachiŵiriyo madzulo ndithu. Pamodzi ndi mwanawankhosayo, uziperekanso chopereka chachakudya ndi cha chakumwa, monga zam'maŵa zija, kuti zipereke fungo lokoma ndipo zikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta.
42Zopereka zopsereza zimenezi ziziperekedwa nthaŵi zonse pa mibadwo yonse. Muzizipereka pamaso pa Ine Chauta pa chipata choloŵera m'chihema chamsonkhano, kumene ndizidzakumana ndi anthu anga ndi kulankhula nawo.
43Kumeneko ndiko ndizidzakumana ndi Aisraele, ndipo malo amenewo azidzakhala oyeretsedwa chifukwa cha ulemerero wanga.
44Chihema chamsonkhanocho ndidzachisandutsa kuti chikhale chopatulika, pamodzi ndi guwa lomwe. Ndipo Aroni ndidzampatula pamodzi ndi ana ake aamuna, kuti akhale ansembe anga onditumikira.
45Ndidzakhala pakati pa anthu anga Aisraele, ndipo ndidzakhala Mulungu wao.
46Adzandidziŵa Ine Chauta amene ndidaŵatulutsa ku Ejipito kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Chauta, Mulungu wao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.