1 Mbi. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Maina a makolo kuyambira Adamu kufikira Abrahamu(Gen. 5.1-32; 10.1-32; 11.10-26)

1Adamu adabereka Seti, Seti adabereka Enosi, Enosi adabereka Kenani,

2Kenani adabereka Mahalalele, Mahalalele adabereka Yaredi,

3Yaredi adabereka Enoki, Enoki adabereka Metusela, Metusela adabereka Lameki,

4Lameki adabereka Nowa, Nowa adabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.

5Ana a Yafeti naŵa: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Meseki ndi Tirasi.

6Ana a Gomeri naŵa: Asikenazi, Rifati ndi Togarima.

7Ana a Yavani naŵa: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.

8Ana a Hamu naŵa: Kusi, Ejipito, Puti ndi Kanani.

9Ana a Kusi naŵa: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana a Raama naŵa: Sheba ndi Dedani.

10Kusi adabereka Nimirodi. Iyeyu ndiye adayamba kukhala munthu wamphamvu pa dziko lonse lapansi.

11Ejipito adabereka Ludimu, Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,

12Patirusimu, Kasiluhimu (kholo la Afilisti) ndi Kafitorimu.

13Kanani adabereka Sidoni mwana wake wachisamba ndi Heti.

14Kanani analinso kholo la Ayebusi, Aamori, Agirigasi,

15Ahivi, Aariki, Asini,

16Arivadi, Azemari ndi Ahamati.

17Ana a Semu naŵa: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi, Aramu, Uzi, Huli, Getere ndi Meseki.

18Aripakisadi adabereka Sela. Sela adabereka Ebere.

19Ebere adabereka ana aamuna aŵiri. Mwana wina anali Pelegi (pakuti anthu adaagaŵikana pa nthaŵi yake), ndipo mbale wake anali Yokotani.

20Yokotani adabereka Alimodadi, Selefi, Hazara-Maveti, Yera,

21Hadoramu, Uzali, Dikila,

22Ebala, Abimaele, Sheba,

23Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onseŵa anali ana a Yokotani.

24A m'banja la Semu anali aŵa: Aripakisadi, Sela,

25Ebere, Pelegi, Reu,

26Serugi, Nahori, Tera,

27ndi Abramu, ndiye kuti Abrahamu.

Zidzukulu za Ismaele(Gen. 25.12-16)

28Ana a Abrahamu naŵa: Isaki ndi Ismaele.

29Mibadwo yao nayi: mwana wachisamba wa Ismaele anali Nebayoti. Panalinso Kedara, Adibeele, Mibisamu,

30Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema,

31Yeturi, Nafisi ndi Kedema.

32Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu naŵa: Zimirani, Yokosamu, Medani, Midiyani, Isibaki, ndiponso Suwa. Ana a Yokosamu naŵa: Sheba ndi Dedani.

33Ana a Midiyani naŵa: Efa, Efere, Hanoki, Abida ndi Elida. Onseŵa anali zidzukulu za Ketura.

Zidzukulu za Esau(Gen. 36.1-19)

34Abrahamu adabereka Isaki. Ana a Isaki naŵa: Esau ndi Israele.

35Ana a Esau naŵa: Elifazi, Reuele, Yeusi, Yalamu ndi Kora.

36Ana a Elifazi naŵa: Temani, Omara, Zefi, Gatamu, Kenazi, Timna ndi Amaleke.

37Ana a Reuele naŵa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza.

Nzika zoyambirira za ku Edomu(Gen. 36.20-30)

38Ana a Seiri naŵa: Lotani, Sobala, Zibiyoni, Ana, Disoni, Ezere ndi Disani.

39Ana a Lotani naŵa: Hori ndi Honamu. Mlongo wake wa Lotani anali Timna.

40Ana a Sobala naŵa: Aliyani, Manahati, Ebala, Sefi ndi Onamu. Ana a Zibiyoni naŵa: Aiya ndi Ana.

41Mwana wa Ana anali Disoni. Ana a Disoni naŵa: Hamurani, Esibani, Itirani, ndi Kerani.

42Ana a Ezere naŵa: Bilihani, Zaavani ndi Yaakani. Ana a Disani naŵa: Uzi ndi Arani.

Mafumu a ku Edomu(Gen. 36.31-43)

43Naŵa mafumu amene ankalamulira ku dziko la Edomu, Aisraele adakalibe mfumu iliyonse: Bela mwana wa Beori, ndipo mzinda wake unali Dinaba.

44Bela atafa, Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira, adaloŵa ufumu m'malo mwake.

45Yobabu atafa, Husamu wa ku dziko la Temani adaloŵa ufumu m'malo mwake.

46Husamu atafa, Hadadi mwana wa Bedadi, amene adagonjetsa Amidiyani ku dziko la Mowabu, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Mzinda wake ankautchula kuti Aviti.

47Hadadi atafa, Samila wa ku Masireka adaloŵa ufumu m'malo mwake.

48Samila atafa, Shaulo wa ku Rehoboti ku Yufurate, adaloŵa ufumu m'malo mwake.

49Shaulo atafa, Baala-Hanani mwana wa Akibori adaloŵa ufumu m'malo mwake.

50Baala-Hanani atafa, Hadadi adaloŵa ufumu m'malo mwake. Mzinda wake ankautchula kuti Pai. Mkazi wake anali Metabele mwana wa Materedi, mwana wa Mezahabu.

51Hadadi nayenso nkufa.

Mafumu a ku Edomu anali aŵa: Timna, Aliva, Yeteti,

52Oholibama, Ela, Pinoni,

53Kenazi, Temani, Mibizara,

54Magadiele ndi Iramu. Ameneŵa ndiwo mafumu a ku Edomu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help