2 Pet. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Lonjezo la kubweranso kwa Ambuye

1Inu okondedwa, kalata ndikukulemberaniyi ndi yachiŵiri. M'makalata aŵiri onseŵa ndafuna kuutsa mitima yanu kuti mukhale ndi maganizo oona.

2Kumbukirani mau amene aneneri oyera adanena kale, ndiponso lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu limene atumwi adakupatsani.

3Yuda 1.18Choyamba mumvetse izi: pa masiku otsiriza kudzafika anthu olalata, otsata zilakolako zao zoipa.

4Azidzalalata nkumanena kuti, “Kodi suja Ambuye adalonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nkale adamwalira makolo athu, koma zonse zili monga momwe Mulungu adazilengera poyamba paja.”

5Gen. 1.6-9Apa akuiŵala dala kuti kalelo Mulungu atanena mau, zakuthambo zidalengedwa, ndipo dziko lapansi lidapangidwa ndi madzi kufumira m'madzi.

6Gen. 7.11 Ndipo ndi madzi okhaokhawo dziko lapansi la masiku amenewo lidamizidwa ndi kuwonongedwa.

7Koma Mulungu ndi mau omwe aja adasunga zakuthambo ndi dziko lapansi la masiku ano kuti adzazitenthe ndi moto. Akuzisunga kufikira tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osasamala za Iye.

8 Mas. 90.4 Koma inu okondedwa, chinthu chimodzi musaiŵale, kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka chikwi chimodzi, ndipo zaka chikwi chimodzi zili ngati tsiku limodzi.

9Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.

10 Mt. 24.43; Lk. 12.39; 1Ate. 5.2; Chiv. 16.15 Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikulo zakumwamba zidzatha ndi phokoso loopsa. Zinthu zonse zidzayaka moto nkusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili m'menemo zidzapseratu.

11Popeza kuti zonsezi zidzasungunuka motero, nanga simuyenera kukhala anthu angwiro m'makhalidwe anu ndiponso osamala za Mulungu?

12Muziyembekeza tsiku la Ambuye ndi kugwira ntchito zofulumizitsa kudza kwake. Pa tsikulo zakumwamba zidzayaka moto ndi kusungunuka, ndipo zinthu zonse nazonso zidzasungunukira m'motomo.

13Yes. 65.17; 66.22; Chiv. 21.1Koma potsata lonjezo la Mulungu, tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, m'mene chilungamo chizidzakhalamo.

14Choncho inu okondedwa, popeza kuti mukudikira zimenezi, muzichita changu kuti Ambuye adzakupezeni muli opanda banga kapena chilema ndiponso muli pa mtendere ndi Ambuyewo.

15Zindikirani kuti Ambuye athu akukulezerani mtima kuti mupulumuke. Paulo, mbale wathu wokondedwa uja, nayenso adakulemberani za zimenezi ndi nzeru zimene Mulungu adampatsa.

16Paja amanena chimodzimodzi m'makalata ake onse polemba za zimenezi. M'makalatamo muli zina zapatali kuzimvetsa, ndipo anthu osaphunzira ndi a nzeru zosakhazikika amazipotoza, monga amapotozeranso Malembo ena. Pakutero akungodziwononga okha.

17Tsono inu okondedwa, popeza kuti mwazidziŵiratu zimenezi, chenjerani kuti zolakwa za anthu ochimwa zingakusokeretseni ndipo mungagwedezeke kenaka nkugwa.

18Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help