2 Mbi. 33 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Manase aononga ntchito za Hezekiya(2 Maf. 21.1-9)

1Manase anali wa zaka khumi ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 55 ku Yerusalemu.

2Yer. 15.4 Iyeyu adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata ntchito zonyansa za anthu a mitundu ina, amene Chauta adaaŵapirikitsa pofika Aisraele.

3Adayambitsanso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaŵaononga. Adapanganso maguwa a Abaala ndiponso mafano, namapembedza zinthu zonse zamumlengalenga, ndi kumazitumikira.

42Mbi. 6.6 Adamanga maguwa achikunja m'Nyumba ya Chauta imene Chauta mwini wake anali atanena kuti, “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka muyaya.”

5Adamanga maguwa m'mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta, kumangira zolengedwa zonse zamumlengalenga.

6Ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza. Adachita zimenezi ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo ankachita zobwebwetetsa, namasamala zamalodza ndi zanyanga, nkumamvana ndi anthu olankhula ndi mizimu ndi anthu amatsenga. Adachita zoipa zambiri pamaso pa Chauta, naputa mkwiyo wake.

71Maf. 9.3-5; 2Mbi. 7.12-18 Tsono m'Nyumba ya Chauta adaikamo fano lopanga iyeyo, Nyumba imene Mulungu adaauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba imeneyi, mu Yerusalemu muno, malo amene ndaŵasankhula pakati pa mafuko onse a Aisraele, ndimo m'mene adzatamandira dzina langa mpaka muyaya.

8Ndipo sindidzachotsa phazi la Israele m'dziko limene ndidapatsa makolo anu, pokhapokha akamasamala ndi kuchita zonse zimene ndidaŵauza pakumvera malamulo ndi malangizo onse amene ndidaŵapatsa kudzera mwa Mose.”

9Manase adachimwitsa anthu a ku Yuda pamodzi ndi anthu okhala mu Yerusalemu. Ankachita zoipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵaononga pofika Aisraele.

Kulapa kwa Manase

10Chauta adalankhula ndi Manase ndiponso ndi anthu ake, koma iwo sadasamaleko.

11Nchifukwa chake Chautayo adaŵatumira atsogoleri ankhondo a mfumu ya ku Asiriya kudzamenyana naye Manase. Adamkoka ndi ngowe zachitsulo nammanga ndi maunyolo amkuŵa, nkupita naye ku Babiloni.

12Ndiye pamene anali pa mavuto, adapempha kuti Chauta, Mulungu wake, amkomere mtima, ndipo adadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.

13Atapemphera kwa Iye, Mulungu adamva kupempha kwake ndi kupemba kwake, ndipo adambwezanso ku Yerusalemu mu ufumu wake. Motero Manase adadziŵa kuti Chauta ndi Mulungu.

14Pambuyo pake adamanga khoma la kunja kwa mzinda wa Davide kuzambwe kwake kwa Gihoni, kuchokera ku chigwa mpaka poloŵera ku Chipata cha Nsomba. Ndipo adamanga khomalo kuzungulira Ofele nalikweza kwambiri. Adaikanso atsogoleri ankhondo ku mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda.

15Adachotsa milungu yachilendo ndiponso fano m'Nyumba ya Mulungu. Adachotsa maguwa onse achikunja amene anali ataŵamanga pa phiri la Chauta ku Yerusalemu. Ndipo adaŵataya kunja kwa mzinda.

16Adamanganso guwa la Chauta, namaperekerapo nsembe zachiyanjano ndiponso nsembe zothokozera. Tsono adalamula anthu a ku Yuda kuti azitumikira Chauta Mulungu wa Israele.

17Anthuwo ankaperekabe nsembe ku akachisi, koma kwa Chauta, Mulungu wao yekha.

Kutha kwa ufumu wa Manase(2 Maf. 21.17-18)

18Tsono ntchito zina zonse za Manase, pamodzi ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndiponso mau a aneneri amene adalankhula naye m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mafumu a ku Israele.

19Ndipo pemphero lake ndi m'mene Mulungu adalilandirira pemphero lakelo, machimo ake onse, kusakhulupirika kwake, akachisi amene adayambitsa, m'mene adakhazikitsira mafano ndi zithunzi zina, asanadzichepetse paja, zonsezi zidalembedwa m'buku la mbiri ya aneneri.

20Choncho Manase adamwalira, naikidwa m'nyumba mwake. Tsono Amoni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Amoni mfumu ya ku Yuda(2 Maf. 21.19-26)

21Amoni anali wa zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka ziŵiri ku Yerusalemu.

22Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene ankachitira Manase bambo wake. Amoniyo ankapereka nsembe kwa mafano onse amene bambo wake adaŵapanga, ndipo ankaŵatumikira.

23Sadadzichepetse pamaso pa Chauta monga momwe Manase bambo wake adadzichepetsera. Koma Amoniyu ankadzipereka ku machimo kosalekeza.

24Tsono anyamata ake adamchita chiwembu, namupha m'nyumba mwake.

25Koma anthu am'dzikomo adapha onse aja amene adamchita chiwembu Amoniyo. Kenaka anthuwo adalonga Yosiya mwana wake kuti akhale mfumu m'malo mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help