Aef. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za ntchito ya Paulo pakati pa anthu osakhala Ayuda

1Nchifukwa chake ine Paulo ndimakupemphererani. Ndine womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Khristu ndi kugwirira ntchito inu amene simuli Ayuda.

2Kumva mudamva za ntchito imene mwa ufulu wake Mulungu adandipatsa, yolalika pakati panu za kukoma mtima kwake.

3Adandiwululira chinsinsi chake, monga ndidakulemberani mwachidule posachedwapa.

4Akol. 1.26, 27Pamene muŵerenga zimenezi, mungathe kuwona kuti ndikumvetsetsadi chinsinsi chonena za Khristu.

5Chinsinsi chimenechi anthu a mibadwo yakale sadachidziŵe, koma Mulungu wachiwulula tsopano mwa Mzimu Woyera kwa atumwi ake oyera mtima, ndiponso kwa aneneri ake.

6Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.

7Mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandisandutsa wolalika Uthenga Wabwino umenewu, ndipo pakutero adaonetsapo mphamvu yake.

8Pakati pa anthu onse a Mulungu ine ndine wamng'ono koposa, komabe Mulungu adandipatsa ineyo ntchito iyi, yakuti ndilalikire anthu a mitundu ina za chuma chopanda malire, chimene Mulungu amatipatsa mwa Khristu.

9Adandipatsanso ntchito yofotokozera anthu onse za m'mene Mulungu adzachitira zonse zimene Iye adakonzeratu mwa chinsinsi chake. Mulungu amene adalenga zonse, adasunga chinsinsichi chikhalire, nthaŵi isanayambe.

10Tsopano afuna kuti kudzera mwa Mpingo, mafumu ndi aulamuliro onse a Kumwamba adziŵe nzeru za Mulungu zamitundumitundu.

11Mulungu adachita zimenezi kuti zichitikedi zimene Iye adakonzeratu mwa Khristu Yesu Ambuye athu chikhalire, nthaŵi isanayambe.

12Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse.

13Ndikukupemphani tsono kuti musataye mtima chifukwa chakuti ndikukusaukirani. Kwenikweni muyenera kunyadira chifukwa cha kusauka kwangaku.

Paulo apemphera kuti Aefeso adziŵe chikondi cha Khristu

14Nchifukwa chake tsono ndikugwadira Atate,

15amene banja lililonse Kumwamba ndi pansi pano limatchulidwa ndi dzina lao.

16Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu.

17Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.

18Mphu. 1.3Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu.

19Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.

20Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.

21Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help