Yow. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu adzaweruza mitundu ya anthu

1“Nthaŵi imeneyo itafika, masiku amene ndidzakwezanso anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu,

2ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yonse, ndipo ndidzaŵatengera ku chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzaŵaweruza chifukwa cha zimene adachitira Aisraele, osankhidwa anga, pakuti adaŵamwaza m'maiko ao onse, nagaŵana dziko langa.

3Adagaŵana anthu anga pochita maere, mnyamata adamsinthitsa ndi mkazi wadama, mtsikana nkumsinthitsa ndi vinyo, kenaka adamumwa vinyoyo.

4 Yes. 23.1-18; Ezek. 26.1—28.26; Amo. 1.9, 10; Zek. 9.1-4; Mt. 11.21, 22; Lk. 10.13, 14 Yes. 14.29-31; Yer. 47.1-7; Ezek. 25.15-17; Amo. 1.6-8; Zef. 2.4-7; Zek. 9.5-7 “Kodi inu a ku Tiro, a ku Sidoni ndi a ku madera a Filistiya, mukuti mundichite chiyani? Kodi mumati mundilipsirire chifukwa cha zina zimene ine ndakuchitani? Ngati pali kanthu koti mundilipsirire, ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu mofulumira.

5Inu mudatenga siliva ndi golide wanga ndi zinthu zanga zina zamtengowapatali, kupita nazo ku nyumba za milungu yanu.

6Mudakagulitsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kwa Agriki, kuti mupite nawo kutali ndi malire a dziko lao.

7Koma ndidzaŵadzutsa kuti achoke kumalo kumene mudaŵagulitsa. Kenaka ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu.

8Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzaŵagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali aja. Ndatero Ine Chauta.

9“Mulengeze pakati pa anthu

a mitundu ina kuti,

‘Konzekerani nkhondo,

itanani ankhondo amphamvu.

Asilikali onse afike pafupi,

ayambe nkhondo.

10 Yes. 2.4; Mik. 4.3 Sulani makasu anu kuti akhale malupanga.

Sulani migwandali yanu kuti ikhale mikondo.

Ngakhale wofooka anene kuti, Ndalimba mtima.

11“ ‘Fulumirani, bwerani,

inu anthu a mitundu yonse yozungulira,

ndipo musonkhane kumeneko.’ ”

Inu Chauta, tumizani ankhondo anu.

12“Anthu a mitundu yonse akonzeke

ndipo abwere ku chigwa cha Yehosafati.

Pakuti kumeneko ndidzaweruza

anthu a mitundu yonse,

ochokera ku mbali zonse.

13 Chiv. 14.14-16; Chiv. 14.19, 20; 19.15 “Samulani zenga wodulira tirigu,

pakuti mbeu zacha kale kudikira kholola.

Bwerani, dzapondeni mphesa,

poti mopondera mphesa mwadzaza,

ndipo mbiya zikusefukira.

Chonchonso zolakwa za mitundu ina ya

anthu zachuluka zedi.”

14Makamu ndi makamu a anthu

ali m'Chigwa cha Chiweruzo.

Ndithu tsiku la Chauta layandikira

m'Chigwa cha Chiweruzo.

15Dzuŵa ndi mwezi zada,

ndipo nyenyezi zaleka kuŵala.

Chauta adzadalitsa anthu ake

16 Amo. 1.2 Chauta akukhuluma ku Ziyoni,

mau ake amveka ngati bingu

kuchokera ku Yerusalemu.

Ndipo thambo ndi dziko lapansi zikugwedezeka.

Koma Chauta ndiye pothaŵirapo anthu ake,

ndiye linga lotetezera a ku Israele.

17“Motero mudzadziŵa kuti ndine Chauta,

Mulungu wanu,

amene ndimakhala ku Ziyoni,

ku phiri langa loyera.

Yerusalemu adzakhala woyera

ndipo alendo sadzamthiranso nkhondo.

18“Nthaŵi imeneyo ikadzafika,

mapiri adzakhetsa vinyo watsopano,

ndipo kuzitunda kudzayenderera mkaka.

Mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi.

Kasupe adzatumphuka ku Nyumba ya Chauta

ndi kuthirira chigwa cha Sitimu.

19“Koma Ejipito adzasanduka chipululu,

ndipo Edomu adzakhala bwinja lopanda anthu,

chifukwa cha nkhondo imene adathira pa anthu

a ku Yuda ndiponso chifukwa cha kukhetsa

magazi a anthu osalakwa ku dziko lao.

20Koma ku Yudako kudzakhala anthu mpaka muyaya,

ndipo ku Yerusalemu sikudzatha anthu pa mibadwo yonse.

21Ndidzalipsira magazi a ophedwawo,

sindidzalekerera tchimo la olakwawo.

Ine Chauta ndimakhala ku Ziyoni.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help