1Nawu uthenga umene Yeremiya adalandira wonena za Ayuda amene ankakhala ku dziko la Ejipito ku Migidoli, ku Tapanesi, ku Memfisi ndi ku dziko la Patirosi:
2“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Mwaziwona zoopsa zimene ndidagwetsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya ku Yuda. Tsopano yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda anthu okhalamo.
3Zonsezi zidachitika chifukwa cha machimo a anthu amene adaputa mkwiyo wanga, pofukizira lubani milungu ina ndi kumaitumikira, milungu imene sadaidziŵe iwowo kapena inu kapenanso makolo anu.
4Komabe ine ndidakhala ndikutuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Musamachita zoipa zimene Ine ndimadana nazo.’
5Koma makolo anuwo sadamvere, sadasamaleko nkomwe. Sadaleke kuchita zoipa zao, sadasiye kuifukizira lubani milungu ina.
6Motero ukali wa mkwiyo wanga udayaka ngati moto m'mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Mizindayo idasanduka mabwinja osiyidwa, monga m'mene iliri leromu.
7“Ndiye tsopano Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, Chifukwa chiyani mukuti mudziwononge chotero? Chifukwa chiyani mukufuna kuphetsa Ayuda amuna ndi akazi, ana ndi makanda, osakutsalirani ndi mmodzi yemwe pa mtundu wanu?
8Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga pochita zoipa ndi manja anu ndiponso pomafukizira lubani milungu ina m'dziko la Ejipito m'mene mukukhala? Mudziwononga nokha, ndipo musanduka chinthu chomachiseka ndi chonyozeka m'maso mwa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
9Kodi mwaiŵala zoipa zonse zimene adachita makolo anu, mafumu a ku Yuda ndi akazi ao, ndiponso inuyo ndi akazi anu, ku dziko la Yuda ndiponso pa miseu ya mu Yerusalemu?
10Mpaka lero lino simudalape, simudachite mantha, simudatsate malamulo anga amene ndidakuikirani inuyo ndi makolo anu.
11“Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndatsimikiza zoti ndiŵakhaulitse ndi kuŵatheratu anthu a ku Yuda.
12Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene adatsimikiza zopita ku Ejipito kukakhala kumeneko, onsewo adzatheratu. Adzaphedwa m'dziko la Ejipito, ena adzafa pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe adzafadi pa nkhondo kapena kufa ndi njala. Ndipo adzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chinthu chomachiseka ndi chonyozeka.
13Ndidzalanga Ayuda okhala ku Ejipito monga momwe ndidalangira a ku Yerusalemu. Ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri.
14Motero mwa anthu otsala ku Yuda, amene adapita nakakhala ku Ejipito, palibe amene adzapulumuke, kapena kukhala moyo, kapena kubwerera ndi kukakhalanso ku Yuda komwe ankalakalaka. Palibe amene adzabwerere, kungopatula ena othaŵa nkhondo.”
15Tsono amuna onse amene adadziŵa kuti akazi ao ankafukizira lubani milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, anthu ochuluka ndithu, kudzanso anthu onse amene ankakhala ku Patirosi m'dziko la Ejipito, adayankha Yeremiya kuti,
16“Ife sitidzamvera zimene watiwuza m'dzina la Chauta.
17Koma tidzachitadi zonse zimene tidalumbira. Tidzaifukizira ndithu lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa, monga tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo tinali ndi chakudya chambiri, ndipo tinkakhuta, osapeza zovuta.
18Koma kuchokera nthaŵi imene tidaleka kuifukizira lubani mfumukazi yakumwamba, ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, takhala tikusoŵa zonse, ndipo taonongeka ndi nkhondo ndi njala.”
19Akaziwo adapitirira ponena kuti, “Pamene tinkaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza m'mene tinkapangira mfumukaziyo makeke abwino olembapo chithunzi chake, ndiponso m'mene tinkaiperekera nsembe zazakumwa?”
20Atalimva yankho la anthu onsewo, amuna ndi akazi omwe, Yeremiya adati,
21“Za lubani amene munkafukiza inuyo, makolo anu, mafumu anu, akalonga anu ndi anthu am'dzikomo, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu, kodi muyesa kuti Chauta adaziiŵala? Kodi nkupanda kuzikumbukira mumtima mwake?
22Nchifukwa chake Chauta sadathenso kupirira ntchito zanu zoipa ndi zonyansa zimene munkachita. Choncho dziko lanu lidasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa, dziko lopanda anthu, monga liliri leromu.
23Tsoka limeneli lakugwerani chifukwa choti munkafukiza lubani, ndipo munkachimwira Chauta pokana kumvera mau ake ndi posatsata malamulo ndi malangizo ake.”
24Yeremiya adauzanso anthu onse, makamaka akazi, kuti, “Mverani mau a Chauta inu nonse ochokera ku Yuda amene mukukhala ku Ejipito.
25Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, Inu ndi akazi anu mudalonjeza ndi pakamwa panupa ndipo mudazichitadi ndi manja anu. Inu mudanena kuti, ‘Tidzachita zimene talumbira. Tidzaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa.’ Chabwino, tsimikizani lonjezo lanuli, ndi kuchitadi zimene mudalumbirazo.
26Koma tsono imvani mau a Chauta, inu nonse ochokera ku Yuda amene mumakhala ku Ejipito. Chauta akuti, Ndalumbira m'dzina langa lopambana kuti mwa anthu a ku Yuda palibe ndi mmodzi yemwe wodzatchulanso dzina limeneli m'dziko lino la Ejipito kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’
27Panopo ndikuŵazonda kuti ndiŵachite zoipa osati zabwino. Anthu onse a ku Yuda amene ali ku Ejipito adzaphedwa pa nkhondo, ena adzafa ndi njala, mpaka nditaŵatheratu.
28Opulumuka ku nkhondo, amene adzabwerera ku Yuda kuchokera ku Ejipito, ndi oŵerengeka okha. Choncho otsala onse a ku Yuda amene adapita kukakhala ku Ejipito adzadziŵa kuti zoona nziti, zaozo kapena zangazi.
29Ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano, kuti choncho mudziŵe kuti mau anga oti ndidzakulangani ndi oonadi.
302Maf. 25.1-7Chizindikirocho ndi ichi: Farao Hofira, mfumu ya ku Ejipito, ndidzampereka kwa adani ake, ndi kwa anthu ofuna kumupha, monga ndidamchitira Zedekiya mfumu ya ku Yuda: iyenso ndidampereka kwa mdani wake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, amene ankafuna kumupha.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.