1Zitatha izi, ndidaona mngelo wina akutsika kuchokera Kumwamba. Anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo pa dziko lonse lapansi padayera chifukwa cha kuŵala kwake.
2Yes. 21.9; Yer. 51.8; Chiv. 14.8; Yes. 13.21; Yer. 50.39Adafuula mokweza mau ndi kunena kuti,
“Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja!
Wasanduka malo okhalamo mizimu yoipa,
malo othaŵiramo mizimu yonse yonyansa,
malo othaŵiramo mbalame zonse zonyansa
ndi zodedwa.
3 Yes. 23.17; Yer. 51.7 Pakuti adamwetsa anthu a mitundu yonse
vinyo wa zilakolako zadama.
Mafumu a pa dziko lonse lapansi
adachita naye chigololo,
ndipo anthu amalonda a pa dziko lonse lapansi
ankalemererapo pa zolakalaka zake zodziwunjikira chuma.”
4 Yes. 48.20; Yer. 50.8; 51.6, 45 Pambuyo pake ndidamva mau ena ochokera Kumwamba. Adati,
“Inu anthu anga, tulukanimo mumzindamo,
kuti mungachimwire nawo pamodzi,
miliri yao ingakugwereniko.
5 Gen. 18.20, 21; Yer. 51.9 Paja machimo ake ndi ofika mpaka ku thambo,
ndipo Mulungu wakhala akukumbukira ntchito zake zoipa.
6 Mas. 137.8; Yer. 50.29 Mumubwerezere monga momwe iye adakuchitirani.
Mumchite zomwe iye adaŵachita ena zija,
ndipo mumubwerezere moŵirikiza
pa zimene iye adachita.
M'chikho chimene iye ankamwetseramo ena,
mumkonzeremo chakumwa moŵirikiza.
7 Yes. 47.7-9 Monga momwe iye ankanyadira chuma
ndi zosangalatsa,
momwemonso mumsautse ndi kumliritsa.
Iyeyo mumtima mwake amati,
‘Ine pano, mfumu!
Sindine mkazi wamasiye,
sindidzaona konse zondiliritsa.’
8Nchifukwa chake miliri yomugwera
idzamufikira pa tsiku limodzi.
Miliriyo ndi iyi: nthenda, chisoni, ndi njala.
Ndipo adzamtentha ndi moto.
Pakuti ndi amphamvu Ambuye Mulungu amene amuweruza.”
9 Ezek. 26.16, 17 Mafumu a pa dziko lapansi amene ankachita naye chigololo ndi kudzisangalatsa naye, adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa.
10Iwo adzaima patali chifukwa cha kuwopsedwa ndi mazunzo ake. Ndipo adzanena kuti,
“Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka, iwe Babiloni,
mzinda wotchuka, mzinda wamphamvu!
Pa ora limodzi lokha chilango chako chakugwera.”
11 Ezek. 27.31, 36 Anthu amalonda a pa dziko lapansi adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, pakuti palibenso wogula malonda ao.
12Ezek. 27.12, 13, 22Palibenso wogula malonda ao a golide, siliva, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu; nsalu zoyera, zofiirira, zasilika ndi zamlangali; mitengo yamitundumitundu yonunkhira; zinthu zamitundumitundu zopangidwa ndi mnyanga wanjovu, ndiponso ndi mitengo yamtengowapatali; zinthu zopangidwa ndi mkuŵa, chitsulo ndi mwala wokongola;
13zokometsera chakudya zamitundumitundu, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta, ufa wosalala ndi tirigu, ng'ombe ndi nkhosa, akavalo ndi ngolo, akapolo ndi akaidi.
14Amalondawo adzamuuza kuti,
“Zokoma zimene mtima wako unkalakalaka,
zakuthera.
Zachuma ndi zamakaka zako zonse zakutayikira,
sudzazipezanso konse.”
15 Ezek. 27.31, 36 Anthu ogulitsa zimenezi, amene adalemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha kuwopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kumva chisoni kwambiri,
16ndipo adzanena kuti,
“Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu.
Unkavala nsalu zoyera, zofiirira ndi zamlangali.
Unkadzikongoletsa ndi golide,
ndiponso ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu.
17 Yes. 23.14; Ezek. 27.26-30 Koma pa ora limodzi lokha chuma chonsechi chaonongeka.”
Onse oyendetsa zombo, onse oyenda pa nyanja, antchito apazombo, ndi onse oyendetsa malonda ao pa nyanja, adaima patali.
18Ezek. 27.32Poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa, adafuula kuti, “Ndi mzinda uti udalinganapo ndi mzinda wotchukawu?”
19Ezek. 27.30-34Adadzithira fumbi kumutu, akulira ndi kumva chisoni kwambiri. Ankafuula kuti,
“Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu,
mzinda umene anthu onse okhala ndi zombo zapanyanja
adalemera nacho chuma chake.
Koma pa ora limodzi lokha wasanduka bwinja.”
20 Deut. 32.43; Yer. 51.48 Kondwerani inu, Dziko la Kumwamba,
chifukwa cha kuwonongeka kwake.
Kondwerani inu, anthu a Mulungu,
inu atumwi, ndi inunso aneneri.
Pakuti Mulungu pakuulanga mzindawo,
wautsutsa kuti ndi wolakwa pa zimene udakuchitani.
21 Yer. 51.63, 64; Ezek. 26.21 Pambuyo pake mngelo wina wamphamvu adanyamula mwala, kukula kwake ngati chimphero. Adauponya m'nyanja nanena kuti, “Umu ndi m'mene Babiloni, mzinda wotchuka uja,
“Udzaponyedwere pansi mwamphamvu,
ndipo sudzapezekanso.
22 Ezek. 26.13; Yes. 24.8 Yer. 7.34; 25.10 Mwa iwe simudzamvekanso konse liwu la oimba zeze,
kapena la akatswiri a zoimbaimba,
kapena la oliza chitoliro kapena lipenga.
Mwa iwe simudzapezekanso konse
mmisiri wa ntchito iliyonse.
Mwa iwe simudzamvekanso konse liwu la kupera.
23Mwa iwe simudzaonekanso konse kuŵala kwa nyale.
Mwa iwe simudzamvekanso konse
mau a mkwati wamwamuna kapena wamkazi.
Amalonda anali anthu otchuka kwambiri aja
a pa dziko lapansi.
Unkanyenga anthu a mitundu yonse ndi maula ako.”
24 Yer. 51.49 Mu mzinda umenewo mudapezeka magazi a aneneri,
ndi a anthu a Mulungu,
ndi a anthu onse amene adaphedwa pa dziko lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.