Ezek. 43 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta abwerera ku Nyumba yake

1Pambuyo pake munthu uja adapita nane ku chipata choyang'ana kuvuma.

2Ezek. 10.3, 4, 18, 19; 11.22, 23; Chiv. 1.15 Kumeneko ndidaona ulemerero wa Mulungu wa Israele ukuchokera kuvuma. Liwu lake linali ngati mkokomo wa madzi, ndipo dziko lapansi lidaŵala ndi ulemerero wakewo.

3Zimene ndidaziwona m'masomphenya zinali ngati zomwe ndidaaziwona zija pamene Chauta adaabwera kudzaononga mzinda. Zinalinso ngati zimene ndidaaziwona ku mtsinje wa Kebara. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba.

4Ulemerero wa Chauta udakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, kuloŵera chipata choyang'ana kuvuma.

5Mzimu wa Mulungu udandinyamula numandiloŵetsa m'bwalo lam'kati. Ndipo ulemerero wa Chauta udadzaza Nyumba yakeyo.

6Munthu uja ataima pambali panga, ndidamva wina akundilankhula kuchokera m'Nyumba ya Mulungu.

7Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, malo ano ndi malo a mpando wanga waufumu, malo amene ndimapondapo mapazi anga. Kuno ndiye kumene ndidzakhale pakati pa anthu anga Aisraele mpaka muyaya. Iwowo ngakhalenso mafumu ao, sadzaipitsanso dzina langa loyera pokhala osakhulupirika kapena poika mitembo ya mafumu ao ku zitunda zachipembedzo.

8Ankamanga chiwundo chao pafupi ndi changa ndiponso mphuthu zao pafupi ndi zanga, nkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero ankaipitsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao zimene ankachita. Tsono ndidaŵaononga ndili wokwiya.

9Tsopano aleke zonyansa zao, aleke kupembedza milungu ina, ndipo achotse mitembo ya mafumu ao, isakhalenso pafupi ndi Ine. Apo Ine ndidzakhala pakati pao mpaka muyaya.

10“Iwe mwana wa munthu, uŵauze Aisraele za Nyumba ya Mulunguyi, maonekedwe ake ndi mamangidwe ake, kuti achite manyazi ndi machimo ao.

11Akachita manyazi ndi zoipa zonse zimene adachita, uŵasimbire za Nyumba ya Mulungu ndi maonekedwe ake, za makomo ake otulukira ndi oloŵera, za kaonekedwe kake konse ndi za makonzedwe ake onse. Uŵafotokozere malamulo ndi malangizo ake, ndipo uŵalembe iwo akuwona, kuti aziŵakumbukira ndi kumaŵatsatadi.

12Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu imene idzamangidwa pamwamba pa phiri. Pozungulira pake ponse padzakhala poyera kwambiri. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu.

Guwa lansembe

13 Eks. 27.1, 2; 2Mbi. 4.1 “Nayi miyeso ya guwa lansembe potsata miyeso yomwe ija imene adaayesera Nyumba ya Mulungu. Patsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake, ndiponso muufupi mwake. M'milomo mwake mwa ngalandeyo mudzakhala mwa mjintchi wa masentimita 25.

14Guwalo msinkhu wake udzakhala wotere: kuchokera pa tsinde pansi mpaka pa phaka lapansi mita limodzi, muufupi mwake theka la mita. Kuchokera ku phaka laling'ono mpaka ku phaka lalikulu, msinkhu wake udzakhala mamita aŵiri, muufupi mwake mudzakhala masentimita makumi asanu.

15Malo osonkhapo moto pa guwa msinkhu wake udzakhala mamita aŵiri. Pamwamba pake padzatuluka nyanga zinai, kutalika kwake theka la mita.

16Malo osonkhapo motowo kutalika kwake kudzakhala mamita asanu ndi limodzi, muufupi mwakenso mamita asanu ndi limodzi, motero adzakhala olingana mbali zonse.

17Phaka lapakati lidzakhala la mamita asanu ndi aŵiri kutalika kwake, ndiponso asanu ndi aŵiri muufupi mwake, pa mbali zake zonse zinai. Ndipo mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 mjintchi wake. Ngalande ya patsinde pa guwalo idzakhala ya masentimita makumi asanu, ndipo makwerero a paguwapo adzayang'ana kuvuma.”

Mwambo wodalitsa guwa

18 Eks. 29.35-37; 1Am. 4.52-56 Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikukuuza kuti guwa litamangidwa, malamulo ake popereka nsembe yopsereza ndiponso powaza magazi paguwapo, ndi aŵa:

19Ansembe a fuko la Levi, am'banja la Zadoki, ndiwo azibwera pafupi nane kudzanditumikira. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Udzaŵapatse mwanawang'ombe wamphongo kuti aperekere nsembe yopepesera machimo.

20Utaipha, udzatengeko magazi, ndi kuŵapaka pa nyanga zinai za guwa pa ngodya zinai za phaka, ndiponso kuzungulira mkombero. Motero udzaliyeretsa guwalo ndi kulidalitsa.

21Kenaka udzatenge ng'ombe yamphongo imene yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo. Udzaitenthe pa malo ake enieni, m'bwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.

22M'maŵa mwake udzapereke tonde wopanda chilema, kuti nayenso akhale nsembe yopepesera machimo. Ndi tondeyo udzayeretse guwalo monga momwe udachitira ndi ng'ombe yamphongo ija.

23Utaliyeretsa kwathunthu guwalo, udzapereke ng'ombe yamphongo yopanda chilema ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema.

24Udzazipereke pamaso pa Chauta, ndipo ansembe adzazithire mchere ndi kuzipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Chauta.

25Tsiku lililonse pa masiku asanu ndi aŵiri uzidzapereka tonde, ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo, kuperekera nsembe yopepesera machimo. Zonsezo zidzakhale zopanda chilema.

26Masiku asanu ndi aŵiriwo adzachite mwambo wopepesera milandu ndi kuyeretsa guwa, kuti alipatulire Chauta.

27Masiku amenewo atatha, kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka m'tsogolo mwake, ansembe azidzapereka pa guwalo nsembe zanu zopsereza ndiponso nsembe zanu zachiyanjano. Apo ndidzakulandirani. Ndatero Ine Ambuye Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help