1Davide adasonkhanitsa ku Yerusalemu akuluakulu onse a Aisraele, ndiye kuti akuluakulu a mafuko, akapitao a magulu amene ankatumikira mfumu, atsogoleri a ankhondo zikwi, atsogoleri a ankhondo mazana, akulu osunga katundu yense ndi ng'ombe za mfumu ndi za ana ake, pamodzi ndi akulu oyang'anira nyumba ya mfumu, anthu amphamvu, ndiponso ngwazi zonse zankhondo.
2 ndiye kuti akerubi amene ankatambasula mapiko ao kuphimbira Bokosi lachipangano la Chauta.
19Davide adati, “Zonse ndalembazi zikugwirizana ndi mau amene adalembedwa potsata malangizo a Chauta mwiniwake, ndipo ndidamvetsa bwino kuti ntchito yonseyo iyenera kuchitika potsata mapulaniwo.”
20Tsono Davide adauza mwana wake Solomoni kuti, “Khala wamphamvu ndipo uchite zimenezo molimba mtima. Usaope, usataye mtima, pakuti Chauta Mulungu wanga ali nawe. Sadzaleka kukusamala ndipo sadzakusiya pa ntchito zonse za Nyumba ya Chautazi.
21Magulu a ansembe ndi a Alevi oyenera kugwira ntchito zonse za ku Nyumba ya Chauta ngokonzeka ndithu. Ndipo iwe, pa ntchito yonseyo, udzakhala nawo anthu aluso odzipereka pa ntchito yao. Anthu wamba onse ndi atsogoleri ao omwe uzidzaŵalamulira ndiwe zoti achite.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.