Yer. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Makhalidwe oipa a ku Yuda

1Ndikadakonda kuti mutu wanga

ukhale ngati chitsime cha madzi,

kuti maso anga akhale ngati kasupe wa misozi,

kuti ndilire usana ndi usiku,

kulirira onse amene adafa a mtundu wa anthu anga?

2Ndani adzandipatse pogona m'chipululu,

kuti ndiŵasiye anthu anga ndi kuŵathaŵa.

Paja onsewo ngachigololo,

ndiponso ndi gulu la anthu onyenga.

3Amapinda lilime ngati uta.

Dziko ladzaza ndi zabodza osati zoona.

“Amanka naonjezeraonjezera zoipa,

ndipo sandidziŵa Ine,”

akuterotu Chauta.

4“Aliyense achenjere ndi mnzake,

asakhulupirire ngakhale mbale wake.

Zoona, aliyense amafuna kulanda malo a mbale wake.

Aliyense amachitira mnzake ugogodi.

5Aliyense amanyenga mnzake,

ndipo sanena zoona.

Pakamwa pao adapazoloŵeza kulankhula zonama.

Amakonda zoipa kwambiri,

kotero kuti sangathenso kulapa.

6Amasanjikiza tchimo pa tchimo linzake,

chinyengo pa chinyengo chinzake.

Amakana kundidziŵa,”

akuterotu Chauta.

7Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti,

“Ndithu, anthu angaŵa ndidzaŵasungunula

ngati chitsulo, ndipo ndidzaŵayesa.

Iwowo ndi ochimwa, ndingathe bwanji kuŵalekerera?

8Lilime lao lili ngati muvi wakuthwa.

Aliyense pakamwa pake pamatuluka mau aubwenzi,

m'menemo mumtima mwake

akukonzekera zomchita mnzake chiwembu.

9Kodi zimenezi ndipanda kuŵalanga nazo?

Monga ndisaulipsire mtundu wotere wa anthu?”

Akutero Chauta

10Ine ndidati,

“Ndidzamva chisoni ndi kulira mokweza

chifukwa cha mapiri.

Ndidzadandaula chifukwa cha mabusa am'chipululu

popeza kuti malo onsewo aonongeka.

Palibe amene amapitako,

sikumveka nkulira kwa ng'ombe komwe.

Mbalame zonse zouluka ndiponso nyama zakuthengo

zathaŵa, osaonekanso.”

11Apo Chauta adati,

“Yerusalemu ndidzamsandutsa bwinja,

ndidzamusandutsa mokhala nkhandwe.

Mizinda ya ku Yuda idzasiyidwa,

simudzakhala anthu.”

12Ine ndidati, “Kodi wanzeru ndani, amene angamvetse zimenezi? Chauta adazifotokozera yani, kuti iyeyo akafotokozere ena? Nanga chifukwa chiyani dziko laonongeka ndi kusanduka chipululu, m'mene anthu sapitamo?”

13Apo Chauta adayankha kuti, “Nchifukwa chakuti anthu angawo sadatsate malamulo amene ndidaŵapatsa, ndipo sadamvere mau anga ndi kuŵasamala.

14Koma ankangotsata zolakwa za mitima yao yokanika. Ankapembedza Abaala monga momwe makolo ao adaŵaphunzitsira.

15Tamvani tsono zimene Ine Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndidzachite. Anthu ameneŵa ndidzaŵadyetsa ziphe ndi kuŵamwetsa madzi azumu.

16Ndidzaŵabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo ao sadaidziŵe. Ndidzaŵalondola ndi ankhondo mpaka kuŵatheratu onse.”

Anthu a ku Yerusalemu apempha chithandizo

17Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti,

“Muziganize bwino,

muitane akazi olira maliro kuti abwere.

Akaziwo akhale aja amadziŵa kwambiri kuliraŵa.”

18Anthu akuti, “Abwere mofulumira adzatilire

kuti m'maso mwathu mudze misozi

nsidze zathu zinyowe.”

19Kukumveka kulira kwa Ziyoni,

akuti, “Kalanga ife! Taonongeka!

Manyazi aakulu atigwera.

Tiyenera kusiya dziko lathu,

chifukwa nyumba zathu azigwetsa.”

20Ine ndidati,

“Inu azimai, mverani mau a Chauta.

Tcherani makutu kuti mumve zimene akunena.

Ana anu aakazi muŵaphunzitse kulira.

Aliyense aphunzitse mnzake nyimbo yamaliro.

21Imfa yatifikira kudzera m'mawindo,

yaloŵa ngakhale m'nyumba zathu zaufumu.

Idapha ana athu m'miseu,

ndipo idatha anyamata m'mabwalo.”

22Chauta adandiwuza kuti ndinene izi:

“Mitembo ya anthu idzagwa,

kuchita kuti mbwembwembwe ngati ndoŵe m'minda,

ngati mitolo pambuyo pa anthu ovuna.

Koma palibe amene adzaitole.”

23Chauta akunena kuti,

“Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake,

munthu wamphamvu asanyadire mphamvu zake,

ndipo munthu wolemera asanyadire chuma chake.

24 Mitundu ina yonseyi njosaumbalidwa, ngakhale banja lonse la Israele nalonso nlosaumbalidwa mu mtima.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help