1Tsono Yobe adayankha kuti,
2“Achikhala mavuto anga adaayesedwa,
achikhala masoka anga adaaŵaika pa sikelo,
3bwenzi atalemera kupambana mchenga wonse wam'nyanja.
Nchifukwa chake kulankhula kwanga kuli kokadzulira.
4Zoonadi mivi yake ya Mphambe yandibaya,
thupi langa likumva ululu wa miviyo.
Zoopsa za Mulungu zandizinga, kuti zilimbane nane.
5Kodi bulu amalira akakhala ndi msipu?
Nanga ng'ombe, kodi imalira ikakhala ndi chakudya?
6Kodi chakudya nkuchidya chili zii, chopanda mchere?
Kodi choyera cha dzira chimatsekemera?
7Zakudya zimenezi sindifuna nkuzilaŵa komwe,
zakudya zake ndi zobwerera kukhosi.
8“Achikhala ndidaalandira chomwe ndikufuna,
achikhala Mulungu adaandipatsa chimene ndikukhumba!
9Achikhala kudaamkomera Mulungu kuti anditswanye,
achikhala adaandimenya ndi dzanja lake,
nkundiwonongeratu!
10Zimenezi zikadandisangalatsa,
ndikadakondwa nazo kwambiri ngakhale zipweteke chotani,
podziŵa kuti sindidakane mau a Woyera uja.
11Kodi mphamvu zanga ndi zotani
kuti ndizikhalabe ndi moyo?
Nanga moyo wanga ukupitiriranji,
ngati chiyembekezo palibe?
12Kodi ine ndidachita kuti gwa ngati mwala?
Kodi thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo?
13Zoona, ndilibenso mphamvu zodzipulumutsira,
kulibenso kwina koti nkupezerako chithandizo.
14“Pa mavuto ngati ameneŵa
pafunika abwenzi okhulupirika,
kuwopa kuti mwina mwake
munthu angasiyane ndi Mphambe.
15Koma abwenzi anga ndi onyenga,
ngati mtsinje wothamanga,
ngati mitsinje youma msanga mvula ikasoŵa.
16Ali ngati mitsinje ya madzi abii nthaŵi ya dzinja,
imene madzi ake amakhala ambiri
chifukwa cha kuchuluka kwa mvula.
17Koma pa nthaŵi ya mafundi imauma,
kukatentha imamwerera.
18Anthu apaulendo amapatukirako kufuna madzi,
koma amangoyendayenda nkufera m'chipululu.
19Oyenda pa ngamira a ku Tema amaifunafuna mitsinjeyo.
Alendo a ku Sheba amaidalira.
20Amataya mtima chifukwa ankayembekeza kupeza madzi,
koma pofika kumeneko, angoti kakasi, poti idauma.
21“Tsono umu ndimo m'mene inuyo mwandichitira ine.
Mwaona tsoka langa, ndipo mukuchita mantha.
22Kodi ndanena kuti, ‘Mundipatse mphatso,’
kapena kuti, ‘Mupereke chiphuphu kwa wina
chifukwa cha ine?’
23Kodi ndanena kuti, ‘Mundipulumutse kwa mdani,’
kapena kuti, ‘Mundiwombole kwa ondizunza?’
24“Chabwino, langizeni ndipo ndidzakhala chete.
Dziŵitseni m'mene ndidachimwira.
25Mau oona amalasa mtima,
koma inu mukunditsutsa pa zotani?
26Kodi inu mukufuna kundidzudzuliranji?
Monga simukuwona kuti mau a munthu wotaya
mtima ndi mphepo chabe?
27Zoonadi inu mumapondereza ana amasiye,
ndi kuŵaika pa malonda abwenzi anu omwe.
28“Tsono mundiyang'anitsitse bwino!
Sindikulankhula zabodza pamaso panu.
29Chonde, feŵani mtima, musachite zosalungama.
Musandiimbe mlandu, poti ndine wolungama.
30Kodi mukuganiza kuti ndikulankhula zabodza?
Monga ine sindingasiyanitse chabwino ndi choipa?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.