Yos. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kupasuka ndi kuwonongeka kwa mzinda wa Ai.

1Pambuyo pake Chauta adauza Yoswa kuti, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga ankhondo onse, ndipo upite nawo ku Ai. Ndidzapereka m'manja mwanu mfumu ya ku Ai pamodzi ndi anthu ake onse. Mzindawo pamodzi ndi dzikolo, zonsezo zidzakhala zanu.

2Mzinda wa Ai ndi mfumu yake yomwe, muuchite zomwe mudachita Yeriko ndi mfumu yake. Koma katundu wamumzindamo ndi zoŵeta, musunge zikhale zanu. Muulalire mzindawo, ndipo muuthire nkhondo cha kumbuyo kwake.”

3Motero Yoswa adakonzeka ndi ankhondo ake kupita ku Ai. Adasankhula ankhondo ena olimba mtima zikwi makumi atatu, ndipo adaŵatuma usiku.

4Adaŵapatsa malamulo akuti, “Kabisaleni kumbuyo kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma kakhaleni okonzekera kuuthira nkhondo.

5Anthu anga pamodzi ndi ine ndiye tidzayambe kuuputa mzindawo cha kumaso kwake. Tsono akadzangotuluka kuti alimbane nafe, ife tidzabwerera m'mbuyo, monga momwe tidachitira tsiku lina lija.

6Adzatithamangitsa motero, mpaka ife titaona kuti ali kutali ndi mzindawo, chifukwa iwowo azidzati, ‘Akutithaŵa monga kale lija.’

7Pamenepo tsono mudzatuluke kuja mudzakhale mutabisalaku, ndipo mudzalanda mzindawo. Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani mzinda umenewo.

8Mutaulanda, dzauyatseni moto, monga Chauta walamulira. Ameneŵa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.”

9Motero Yoswa adaŵatuma, ndipo iwo adapita ku malo obisalakowo kukaulalira mzindawo. Malowo anali cha kuzambwe kwa Ai, pakati pa Ai ndi Betele. Koma Yoswa ndi gulu lake lankhondo adakhala m'zithando usiku wonse.

10M'mamaŵa, Yoswa adadzuka naitana ankhondo ake onse. Tsono iyeyo ndi atsogoleri a Aisraele, adapita ku Ai.

11Ankhondo omwe anali ndi iyeyo adatsogolako, nakamanga zithando chakumpoto kupenyana ndi chipata cha mzindawo. Pakati pa iwowo ndi mzinda wa Aiwo panali chigwa.

12Yoswa adapatula anthu zikwi zisanu, naŵabisa cha kuzambwe kwa mzindawo, pakati pa Ai ndi Betele.

13Adakhazika ankhondo mokonzekera nkhondo, ndipo gulu lalikulu la ankhondowo lidamanga zithando cha kumpoto kwa mzinda, m'chigwamo, koma gulu lina lija lidakamanga chakuzambwe.

14Mfumu ya ku Ai itaona anthu a Yoswawo, idachita zinthu mofulumira. Pamodzi ndi anthu ake idapita ku malo otsika oyang'anana ndi Araba, kuti ikamenyane ndi Aisraele kumeneko ngati kale lija. Iyo sinkadziŵa kuti aithira nkhondo cha kumbuyo kwake.

15Yoswa pamodzi ndi anthu akewo adachita ngati akuthaŵa, kumaloŵera chakuthengo ndithu.

16Anthu onse amumzindamo adauzidwa kuti aŵatsate pambuyo, ndipo pamene ankapirikitsa Yoswa, iyeyo ankathaŵira kutsogolo ndithu, kutalikirana ndi mzinda wao uja.

17Choncho mwamuna aliyense wamumzindamo anali atatulukamo kuthamangitsa Aisraele. Mzindawo udangotsala wokha, popanda woti angautchinjirize.

18Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Loza mkondo wako ku Ai. Mzindawu ndikukupatsa iwe.” Yoswa adachitadi monga adamuuzira.

19Tsono atangokweza dzanja lake, anthu amene adabisala aja, adavumbuluka msangamsanga, adathamangira mu mzindawo naugonjetsa, ndipo adautentha pomwepo.

20Anthu a ku Ai aja atacheukira m'mbuyo adangoona utsi uli tolotolo! Malo oti iwowo athaŵireko panalibe, chifukwa choti Aisraele aja adaathaŵira kuthengoŵa adabwerera kudzalimbana nawo.

21Yoswa ndi anthu anali nawo aja, ataona kuti anzao aja alanda mzindawo, ndipo kuti utsi uli tolotolo, adatembenuka nayamba kupha anthu a ku Ai aja.

22Nawonso Aisraele amene anali mumzindamo adabwera kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho onsewo anali atazingidwa ndi Aisraele, ndipo onsewo adaphedwa.

23Palibe ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka kapena kutulukamo wamoyo, koma mfumu ya ku Ai yokha. Mfumuyo adaigwira, napita nayo kwa Yoswa.

24Motero Aisraele adapha adani ao m'chigwa ndi m'thengo m'mene adaŵapirikitsira. Ndipo adabwereranso ku Ai, naphanso otsala amene anali kumeneko.

25Chiŵerengero chonse cha anthu a ku Ai amene adaphedwa pa tsikulo chinali zikwi khumi ndi ziŵiri, amuna ndi akazi omwe pamodzi.

26Yoswa ankalozabe mkondo wake uja ku Ai, osatsitsa dzanja lake mpaka munthu aliyense mumzindamo ataphedwa.

27Ndipo Aisraele adatenga zoŵeta ndi katundu yense wamumzindawo, monga momwe Chauta adauzira Yoswa.

28Pomwepo Yoswa adautentha mzinda wa Ai, nausiya bwinja monga uliri leromu.

29Mfumu ya mzindawo adaipachika pa mtengo ndi kuisiya pompo mpaka madzulo. Madzulo ndi kachisisira, Yoswa adalamula kuti akatsitse mtembowo, ndipo atatero adautaya pansi ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo adaunjikapo mulu wa miyala. Muluwo uli pomwepo mpaka lero lino.

Aŵerenga malamulo ku Ebala.

30 Deut. 27.2-8 Tsono Yoswa adamangira Chauta guwa pa phiri la Ebala.

31Eks. 20.25 Adalimanga potsata malangizo amene Mose mtumiki wa Chauta adaapatsa Aisraele, ndi potsata mau a m'buku la malamulo a Mose onena kuti, “Guwa likhale la miyala yosasema ndi zipangizo zachitsulo.” Pa guwa limenelo adaperekapo nsembe zopsereza kwa Chauta, ndipo adaperekanso zopereka zamtendere.

32Kumeneko, Aisraele onse akupenya, Yoswa adalemba pa miyala chitsanzo cha malamulo aja amene Mose adaalemba.

33Deut. 11.29; 27.11-14 Aisraele onse, pamodzi ndi atsogoleri ao, akuluakulu ao, aweruzi ao ndiponso alendo omwe amene anali pakati pao, adaimirira pa mbali ziŵiri za Bokosi lachipangano lija, ena uku ena uku, moyang'anana ndi ansembe Achilevi amene anali kunyamula Bokosilo. Theka lina la anthu lidaimirira kuyang'anana ndi phiri la Gerizimu, ndipo theka lina kuyang'anana ndi phiri la Ebala. Pachiyambi penipeni, Mose mtumiki wa Chauta adaaŵalamula iwowo kuti azichita zimenezi pofuna kulandira madalitso.

34Tsono Yoswa adaŵerenga mau onse a malamulo momveka bwino, pamodzi ndi madalitso ndiponso matemberero, monga momwe zidalembedwera m'buku la malamulo a Mose.

35Yoswayo adaŵerenga lililonse mwa malamulo a Mose, kuŵerengera anthu onse amene adasonkhana. Akazi ndi ana, pamodzi ndi alendo omwe okhala pakati pao, anali pomwepo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help