1Bokosi lachipangano la Chauta lidakhala m'dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iŵiri.
2Tsono Afilisti adaitana ansembe ao ndi anthu amaula naŵafunsa kuti, “Tichite nalo chiyani Bokosi lachipanganoli? Tiwuzeni. Kodi Bokosi limeneli tingalibwezere ku malo ake mwa njira yanji?”
3Iwo adati, “Mukafuna kubwezera Bokosili, musalitumize lopanda kanthu, koma mwa njira iliyonse mulitumize pamodzi ndi mphatso, kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake mudzachira, ndipo pamenepo mudzadziŵa chifukwa chiyani chilango cha Mulungu sichikukuchokani.”
4Apo anthuwo adafunsa kuti, “Kodi nsembe yopepesera machimoyo idzakhale ya mtundu wanji?” Iwo adayankha kuti, “Idzakhale zifanizo zagolide za mafundo asanu ndi za mbeŵa zisanu kuŵerengetsa akalonga asanu a Afilisti, pakuti mliri womwewo unali pa inu nonse ndi pa akalonga anu.
5Tsono mupange zifanizo za mafundo anu aja ndi za mbeŵa zimene zikuwononga m'dziko mwanu, ndipo mulemekeze Mulungu wa Aisraele. Mwina mwake sadzakuvutaninso, inu ndi milungu yanu ndi dziko lanu.
6Chifukwa chiyani mukufuna kukhala okanika ngati Aejipito aja ndi Farao? Kodi Aejipitowo, Mulungu ataŵazunza, suja adaŵalola Aisraele kuti apite, ndipo adapitadi?
7Ndiye inu, konzani galeta latsopano ndipo mutenge ng'ombe ziŵiri zazikazi zamkaka zimene sizidavalepo goli ndi kale lonse. Mumange ng'ombezo ku galeta, koma makonyani ake muŵasiye kumudzi kwanu.
8Tsono mutenge Bokosi lachipanganolo, muliike pa galeta, ndipo pambali pake muikepo bokosi la zinthu zagolide zija zimene mukutumiza kwa Chauta, kuti zikhale nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake muzitaye ng'ombezo ndipo galeta lizipita.
9Tsono muziliyang'ana. Likamangopita kulondola kwao kwa Bokosilo mpaka kukafika ku Betesemesi, ndiye kutidi ndi Mulungu wa Aisraele amene adatidzetsera zovuta zazikuluzi. Koma zikapanda kutero, tidzadziŵa kuti sindiye amene adatizunza, zidangochitika mwatsoka.”
10Anthu aja adachitadi momwemo. Adatenga ng'ombe ziŵiri zamkaka nazimanga ku galeta, natsekera makonyani ake m'khola.
11Ndipo adaika Bokosi lachipangano pa galeta, ndi bokosi lija m'mene munali mbeŵa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao.
12Tsono ng'ombezo zidapita molunjika potsata mseu waukulu wokafika ku Betesemesi, zikunka zikulira. Sizidacheukire kumanzere kapena kumanja, ndipo akalonga a Afilisti ankazitsata pambuyo, mpaka kukafika ku malire a ku Betesemesi.
13Nthaŵiyo anthu a ku Betesemesi ankadula tirigu m'chigwa. Ndipo pamene adati tha, napenya Bokosi lachipanganolo likubwera, adakondwa.
14Galeta lija lidafikira ku munda wa Yoswa ku Betesemesi ndi kuima komweko. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu am'mudzimo adaliŵaza nkhuni galetalo ndipo adapha ng'ombezo nazipereka kwa Chauta ngati nsembe yopsereza.
15Alevi anali atatsitsa Bokosi lachipangano la Chauta ndi bokosi lina lija la pambali pake m'mene munali zinthu zagolide, naŵaika pa mwala waukuluwo. Ndipo anthu a ku Betesemesi adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina kwa Chauta pa tsiku limenelo.
16Akalonga asanu a Afilisti aja ataona zimenezo, adabwerera ku Ekeroni tsiku lomwelo.
17Zifanizo zagolide za mafundo zija zimene Afilisti adapereka ngati nsembe zopepesera Chauta, zinkakhalira mizinda isanu: chimodzi chinali cha ku Asidodi, china cha ku Gaza, china cha ku Asikeloni, china cha ku Gati, china cha ku Ekeroni.
18Nazonso zifanizo zagolide za mbeŵa adazipereka moŵerengetsa mizinda yonse ya Afilisti imene inali ya akalonga asanu aja. Ina inali mizinda yamalinga, ina inali midzi yapamtetete. Mwala waukulu uja umene adaikapo Bokosi lachipangano lija m'munda wa Yoswa ku Betesemesi, udakalipo mpaka pano ngati mboni.
19Pambuyo pake Chauta adaphapo anthu 70 a ku Betesemesi chifukwa choti adaasuzumira m'Bokosi lachipangano, ndipo anzao adalira, popeza kuti Chauta adaapha anthu ambiri pakati pao.
Bokosi lachipangano ku Kiriyati-Yearimu20Tsono anthu a ku Betesemesi adati, “Angathe ndani kuima pamaso pa Chauta, Mulungu woyerayu? Ndipo Bokosi lachipanganoli lidzapita kuti likachoka kuno?”
21Choncho adatuma amithenga kwa nzika za ku Kiriyati-Yearimu kukanena kuti, “Afilisti abweza Bokosi lachipangano la Chauta. Bwerani kuno, mudzalitenge, kupita nalo kwanuko.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.