1Naŵa mau otsiriza a Davide:
Nayi nyimbo ya Davide, mwana wa Yese,
mau a munthu amene Mulungu adamkweza pamwamba,
amene Mulungu wa Yakobe adamdzoza kuti akhale mfumu,
munthu wokonda kuimba nyimbo zokoma za Israele:
2“Mzimu wa Chauta ukulankhula mwa ine,
mau ake ali pakamwa panga.
3Mulungu wa Israele walankhula,
Thanthwe la Israele landiwuza kuti,
‘Munthu amene amalamulira anthu mwachilungamo,
kuŵalamulira molemekeza Mulungu,
4amaŵafikira ngati kuŵala kwam'maŵa
amaŵaŵalira ngati dzuŵa lam'maŵa pa tsiku lamitambo.
Alinso ngati mvula imene imameretsa udzu pa nthaka.’
5Motero Mulungu adzadalitsa zidzukulu zanga
chifukwa Iye adachita nane chipangano chosatha,
chipangano cholongosoka bwino ndi chosasinthika.
Izi nzimene ndikulakalaka,
ndiponso zimene zidzandipulumutsa.
Ndi Mulungu amene adzachita zonsezi.
6Koma anthu oipa onse amachotsedwa ngati minga.
Anthu satha kuigwira ndi manja.
7Koma amaidula ndi chigwandali nakaitentha pa moto.”
Ankhondo otchuka a Davide.(1 Mbi. 11.10-41)8Naŵa maina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti, wa ku Takemoni, mkulu wa atsogoleri ankhondo atatu. Iye adaamenyana nkhondo ndi anthu 800, naŵapha onsewo ndi mkondo wake.
9Mnzake wotsatana naye mwa anthu atatu amphamvu aja anali Eleazara, mwana wa Dodo, mwana wa Aho. Iyeyo anali pamodzi ndi Davide pamene ankaputa Afilisti omwe adaasonkhana kuti amenyane naye nkhondo ku Pasi-Damimu. Aisraele anali atathaŵa.
10Koma iyeyo adatsalira, nakantha Afilisti mpaka dzanja lake kuchita kutopa, komabe osataya lupanga. Tsiku limenelo Chauta adampambanitsa. Aisraelewo adabwerera pambuyo pake kudzangofunkha za ophedwawo.
11Wotsatana ndi ameneyo anali Sama, mwana wa Age Muharari. Nthaŵi ina Afilisti adasonkhana ku Lehi kumene kunali munda wa mphodza. Aisraele nkuthaŵa Afilisti aja.
12Koma iyeyo adaima pakatimpakati pa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo, chifukwa Chauta adampambanitsa kwambiri.
13Nthaŵi yokolola, atatu mwa ankhondo otchuka makumi atatu aja, adapita kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu lankhondo la Afilisti linkamanga zithando zankhondo ku chigwa cha Refaimu.
14Pamenepo nkuti Davide ali m'phanga muja, ndipo kagulu kankhondo ka Afilisti kali ku Betelehemu.
15Tsono Davide adalankhula molakalaka kuti, “Ha, wina akadandipatsa madzi akumwa a m'chitsime chimene chili ku chipata ku Betelehemu kuti ndimwe!”
16Pamenepo anthu atatu amphamvu aja adapita, nabzola zithando za Afilisti, nkutunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo, nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo adangoŵathira pansi, kuŵapereka kwa Chauta,
17nati, “Ndithudi pali Chauta, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao paminga.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja.
18Tsono Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, ndiye anali mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja. Ndiye adapha anthu 300 ndi mkondo wake, nakhala wotchuka ngati anthu atatu ena aja.
19Iyeyo anali womveka kwambiri mwa atsogoleri makumi atatu aja, ndipo adasanduka mkulu wao. Komabe sadafikepo pa anthu atatu aja.
20Benaya mwana wa Yehoyada, wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima amene ankachita ntchito zamphamvu. Iyeyo adapha ankhondo aŵiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa, adatsikira m'chitsime, naphamo mkango.
21Adaphanso Mwejipito wina, wa maonekedwe okongola. Mwejipitoyo adaali ndi mkondo m'manja, koma Benaya adapita kwa iyeyo ndi ndodo chabe. Adalanda mkondowo ku manja mwa Mwejipito uja, namupha ndi mkondo wake womwewo.
22Zimenezi ndi ntchito zimene adatchuka nazo Benaya mwana wa Yehoyada, yemwe anali m'modzi wa anthu makumi atatu amphamvu aja.
23Iyeyo anali womveka pakati pa atsogoleri makumi atatu aja, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Davide adamuika kuti azilamulira asilikali ake omuteteza.
24M'gulu la anthu makumi atatu aja munalinso aŵa: Asahele, mbale wa Yowabu, Elihanani, mwana wa Dodo, wa ku Betelehemu,
25Sama wa ku Harodi, Elika wa ku Harodi
26Helezi Mpeleti, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa,
27Abiyezere wa ku Anatoti, Mebunai Muhusa,
28Zalimoni Mwahohi, Maharai wa ku Netofa,
29Helebi mwana wa Baana wa ku Netofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea, Mbenjamini.
30Panalinso Benaya wa ku Piratoni, Hidai wa ku mitsinje ya ku Gaasi,
31Abiyaliboni Mwaraba, Azimaveti wa ku Bahurimu,
32Eliyaba wa ku Saaliboni, ana a Yaseni, Yonatani,
33Sama Muharari, Ahiyamu mwana wa Sarara Muharari,
34Elipeleti mwana wa Ahasibai wa ku Maaka, Eliyamu mwana wa Ahitofele wa ku Gilo,
35Heziro wa ku Karimele, Paarai Mwaraba,
36Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi,
37Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, wonyamula zida za Yowabu, mwana wa Zeruya,
38Ira Mwitiri ndi Garebu Mwitiri ndi
39Uriya Muhiti uja. Onse pamodzi anali anthu 37.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.