Lev. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Malamulo a mphatso zopereka kwa Chauta

1Chauta adauza Mose kuti,

2“Uza Aisraele kuti: Ngati munthu adalumbira kuti adzapereka munthu mnzake kwa Mulungu, koma pambuyo pake akufuna kumuwombola,

3zoyenera kupereka ndi izi: pa munthu wamwamuna wa zaka makumi aŵiri mpaka zaka 60, pakhale masekeli asiliva 50, potsata kaŵerengedwe ka kunyumba ya Mulungu.

4Munthu wake akakhala wamkazi, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva makumi atatu.

5Akakhala munthu wa zaka zisanu mpaka zaka makumi aŵiri, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva makumi aŵiri pa munthu wamwamuna, ndipo khumi pa munthu wamkazi.

6Akakhala munthu wa mwezi umodzi mpaka zaka zisanu, mtengo wake ukhale wokwana mashekeli asiliva zisanu pa munthu wamwamuna, ndipo zitatu pa munthu wamkazi.

7Munthu wake akakhala wa zaka 60 kapena kupitirirapo, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva 15 pa munthu wamwamuna, ndipo khumi pa munthu wamkazi.

8Munthu akakhala wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira mtengo umenewo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo aike mtengo pa iye. Mtengo umene wansembeyo aike ukhale wolingana ndi momwe munthu wolumbirayo angalipire.

9“Ikakhala nyama yonga imene anthu amaperekera nsembe kwa Chauta, zonse zimene anthu amapereka kwa Chauta nzopatulika.

10Munthu asapereke ina m'malo mwake kapena kuisinthitsa ndi ina, asapereke yabwino m'malo mwa yoipa, kapena yoipa m'malo mwa yabwino. Ndipo akasinthitsa nyama ina ndi inzake, nyamayo pamodzi ndi inzake waisinthitsayo zikhala zopatulika.

11Ikakhala nyama yonyansa, yonga imene siloledwa kuipereka ngati nsembe kwa Chauta, munthuyo abwere ndi nyamayo kwa wansembe.

12Ndipo wansembe atchule mtengo wake poona ngati njabwino kapena ai. Monga momwe iwe wansembe utchulire, mtengo udzakhala momwemo.

13Koma akafuna kuti aiwombole, aonjezepo pa mtengo wake wa nyamayo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wakewo.

14“Pamene munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulikira Chauta, wansembe aiwone ngati ili yabwino kapena ai. Monga momwe wansembe aiwonere, idzakhala momwemo.

15Munthu woiperekayo akafuna kuti aombole nyumba yakeyo, pa mtengo wake wa nyumbayo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo, ndipo idzakhala yake.

16“Munthu akapereka kwa Chauta chigawo cha dera la choloŵa chake, mtengo umene uike ukhale wolingana ndi mbeu zodzabzalamo. Pa mbeu za barele zokwanira makilogaramu 20, mtengo wake ukhale wokwana mashekeli asiliva 50.

17Akapereka munda wake kuyambira pa chaka chokondwerera zaka 50, mtengo wake ukhale wathunthu monga momwe iwe udaikira.

18Koma akapereka munda wake chitatha chaka chokondwerera zaka 50, wansembe aŵerenge mtengo wa ndalama molingana ndi zaka zotsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka 50, ndipo achotse pa mtengo umene wansembe waika.

19Munthu amene adapereka munda, akafuna kuti auwombole, pa mtengo wa mundawo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo, ndipo udzakhala wake.

20Koma ngati safuna kuti aombole kapena ngati waugulitsa kwa munthu wina, mundawo sudzaombolekanso.

21Mwini mundawo atausiya pa chaka chokondwerera zaka 50, udzakhala wopatulikira Chauta ngati munda woperekedwa. Wansembe adzautenga kuti ukhale wake.

22Munthu akapereka kwa Chauta munda umene waugula, umene suli chigawo cha choloŵa chake,

23wansembe aŵerenge mtengo wake kufikira pa chaka chokondwerera zaka 50. Tsono munthuyo apereke ndalama zokwanira mtengo wake pa tsikulo, kuti zikhale zopatulikira Chauta.

24Pa chaka chokondwerera zaka 50, mundawo udzabwezedwa kwa munthu amene adaugulitsayo, amene mtundawo unali wake ngati choloŵa chake.

25Potchula mtengo uliwonse, wansembe aziŵerenga monga momwe amaŵerengera m'Nyumba ya Chauta, ndiye kuti sekeli imodzi ikwanire magera makumi aŵiri.

26“Koma pasakhale munthu amene apereke mwana woyamba wa nyama. Mwanayo ali kale wa Chauta, popeza kuti ndi woyamba. Ngakhale ikhale ng'ombe kapena nkhosa, nja Chauta imeneyo.

27Ikakhala nyama yonyansa pa chipembedzo, aiwombole pa mtengo umene wansembe aike, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake. Koma akapanda kuiwombola, igulitsidwe pa mtengo umene wansembe aike.

28 kwa Chauta, kaya ndi munthu kapena nyama kapena munda umene uli choloŵa chake, chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Chinthu chilichonse choperekedwa choncho kwa Chauta, nchopatulika kopambana.

29Munthu aliyense amene waperekedwa kotheratu, sangathe kuwomboledwa, aziphedwa basi.

30 Num. 18.21; Deut. 14.22-29 “Chigawo chilichonse chachikhumi cham'dziko, kaya ndi cha mbeu zam'nthaka, kaya ndi cha zipatso zam'mitengo, nchake cha Chauta. Chimenecho nchopatulikira Chauta.

31Munthu akafuna kuti aombole chigawo chimodzi chachikhumi chilichonse, aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake.

32Ndipo chigawo chachikhumi chilichonse cha nsambi wa ng'ombe ndi wa nkhosa, ndiye kuti nyama yachikhumi iliyonse imene mbusa aiŵerenge, ikhale yopatulikira Chauta.

33Mwiniwake asafunse ngati nyamayo njabwino kapena njoipa, ndipo asaisinthitse. Akaisinthitsa ndi ina, imeneyo pamodzi ndi imene waisinthitsayo zidzakhala zopatulikira Chauta, ndipo sangaziwombole.”

34Ameneŵa ndiwo malamulo amene Chauta adalamula Mose pa phiri la Sinai kuti auze Aisraele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help