1 Sam. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Elikana ndi banja lake ku Silo.

1Padaali munthu wina dzina lake Elikana, wa ku Ramataimu-Zofimu ku dziko lamapiri la Efuremu. Anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, wa fuko la Efuremu.

2Elikanayo anali wamitala, mkazi wina dzina lake anali Hana, winayo anali Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe.

3Chaka ndi chaka Elikana ankapita ku Silo kuchokera ku mzinda kwao, kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Chauta Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana aŵiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, amene anali ansembe a Chauta.

4Tsiku limene Elikana ankapereka nsembe, ankapatsako magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake aamuna ndi aakazi.

5Ndipo ngakhale ankakonda Hana, ankangompatsa gawo limodzi chifukwa choti Chauta sadampatse ana.

6Tsono chifukwa choti Chauta sadampatse ana, mkazi mnzake uja ankangomnyodola ndi kumpeputsa, kuti amkwiyitse.

7Zimenezi zinkachitika chaka ndi chaka. Nthaŵi zonse akamapita ku nyumba ya Chauta, mkazi mnzakeyo ankamputa. Nchifukwa chake Hana ankangolira, ndipo sankafuna ndi kudya komwe.

8Mwina Elikana mwamuna wake ankamufunsa kuti, “Hana, kodi watani apa ukulira ndi kuwoneka wachisoni ndiponso sukufuna kudya? Kodi kwa iwe ineyo sindikuposa ana aamuna khumi?”

Hana ndi Eli.

9Tsiku lina iwo atatha kudya ku Silo kuja, Hana adaimirira nakapemphera. Nthaŵi imeneyo nkuti Eli, wansembe uja, ali pa mpando pambali pa khomo la Nyumba ya Chauta.

10Hanayo ankavutika kwambiri mumtima mwake, ndipo adapemphera kwa Chauta, akulira ndi mtima woŵaŵa.

11

12Iyeyo akupemphera chotero pamaso pa Chauta, Eli ankamuyang'ana pakamwa.

13Hana ankalankhula chamumtima, milomo yake yokha ndiyo inkagwedezeka, koma mau ake sankamveka. Nchifukwa chake Eli adamuyesa woledzera.

14Tsono adamufunsa kuti, “Mai, kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, akayambe watha vinyo mwamwayu.”

15Koma Hana adayankha kuti, “Iyai mbuyanga, sindidamwe vinyo kapena chakumwa chaukali chilichonse. Munthune ndili ndi chisoni choopsa. Ndakhala ndikulira kwa Chauta chifukwa cha chisoni changachi.

16Musayese kuti ine mdzakazi wanu ndine mkazi wachabechabe, pakuti nthaŵi yonseyi ndakhala ndikuulula kwa Chauta nkhaŵa yanga yaikulu ndi zovuta zanga.”

17Apo Eli adamuyankha kuti, “Pitani ndi mtendere, Mulungu wa Israele akupatseni zimene mwampemphazo.”

18Tsono Hana adati, “Mundikomerebe mtima mdzakazi wanune.” Pompo mkaziyo adachoka nakadya, ndipo sadaonekenso wachisoni.

Kubadwa kwa Samuele ndi kuperekedwa kwake.

19M'maŵa mwake Elikana ndi banja lake adadzuka m'mamaŵa, ndipo atatha kupembedza Chauta, adabwerera kwao ku Rama. Elikana adakhala ndi mkazi wake Hana, ndipo Chauta adamkumbuka Hanayo.

20Motero Hana adaima, ndipo adabala mwana wamwamuna namutcha dzina loti Samuele, kunena kuti, “Ndidachita kumpempha kwa Chauta.”

21Tsono Elikana ndi banja lake lonse adapitanso kukatsira nsembe ya chaka ndi chaka kwa Chauta, ndi kukakwaniritsa lonjezo lake.

22Koma Hana sadapite nao chifukwa adaauza mwamuna wake kuti, “Malinga mwanayu akaleka kuyamwa, ndidzapita naye kuti ndikampereke kwa Chauta, ndipo adzakhala komweko moyo wake wonse.”

23Elikana mwamuna wake adamuuza kuti, “Uchite zimene zikukukomera, uyembekeze mpaka mwanayo ataleka kuyamwa. Kungoti Chauta achitedi monga momwe afunira.” Choncho mkaziyo adatsalira, namalera mwana wake uja mpaka atamletsa kuyamwa.

24Atamuletsa kuyamwa, adapita naye ku nyumba ya Chauta ku Silo. Adatenga ng'ombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogramu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. Ngakhale mwanayo anali wamng'ono ndithu, adapita nayebe.

25Kumeneko adapha ng'ombe yamphongo ija ndipo mwanayo adampereka kwa Eli.

26Tsono Hana adati, “Inu mbuyanga, ndikunenetsa kuti ndithudi ine ndine mkazi uja amene ndidaaimirira pano pamaso panu, ndikupemphera kwa Chauta.

27Mwana uyu ndidachita kupempha, ndipo Chauta wandipatsa chopempha changacho.

28Nchifukwa chake ndampereka kwa Chauta. Moyo wake wonse mwanayu adzakhala wake wa Chauta.” Ndipo onsewo adapembedza Chauta kumeneko.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help