1 Maf. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nkhondo ndi Asiriya

1Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, adasonkhanitsa magulu ake onse ankhondo, ndipo adagwirizana ndi mafumu ena 32 okhala ndi akavalo ndi magaleta. Iyeyo ndi mafumu anzakewo adapita ndipo adakazinga mzinda wa Samariya nauthira nkhondo.

2Tsono Benihadadi adatuma amithenga ake kwa Ahabu mumzindamo kukamuuza mau akuti

3awapatse amithengawo siliva wake pamodzi ndi golide yemwe. Akazi ake okongola, pamodzi ndi ana omwe.

4Ahabu, mfumu ya ku Israele, adayankha kuti, “Monga m'mene mbuyanga mfumu akuneneramo, ineyo ndine wake pamodzi ndi zonse zomwe ndili nazo.”

5Tsono amithenga aja adabweranso kwa Ahabu kachiŵiri ndi mau a Benihadadi onena kuti, “Ndidaakuuza kuti unditumizire siliva wako pamodzi ndi golide wako, akazi ako pamodzinso ndi ana ako omwe.

6Koma maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, ndidzatuma ankhondo anga kumeneko, adzaloŵa m'nyumba zako ndi za nduna zako, ndipo adzatenga zinthu zonse zimene zidzaŵakomere.”

7Apo mfumu Ahabu adaitana akuluakulu onse am'dzikomo naŵauza kuti, “Tsopano mungathe kuwona kuti munthuyu akufuna kutiwononga ife. Adanditumizira mau akuti ndimpatse akazi anga, ana anga, pamodzi ndi siliva ndi golide yemwe, ndipo ine sindidamkanize.”

8Akuluakulu onsewo pamodzi ndi anthu omwe adati, “Musasamaleko zimenezo kapena kumuvomereza ai.”

9Tsono Ahabuyo adauza amithenga a Benihadadi aja kuti, “Mbuyangayo muuzeni kuti, ‘Zonse zimene adanena poyamba paja ndidzachita zimenezo. Koma zatsopano zokhazi sindingathe kuchita.’ ” Amithenga aja adachoka nakauza Benihadadi mau amenewo.

10Pamenepo Benihadadi adatumizanso mau kwa Ahabu kuti, “Ndibwera ndi anthu anga ambiri kudzaononga mzinda wakowo, ndipo adzausandutsa fumbi lokhalokha. Milungu indilange ngati ndilephera kuchita zimenezi.”

11Ahabu, mfumu ya ku Israele, adayankha kuti, “Kamuuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako mpachulu, kulinga utakwerapo. Wankhondo weniweni ndi amene amadzitama atapambana, osati asanamenye nkhondo.’ ”

12Benihadadi adamva mau ameneŵa, pamene ankamwa pamodzi ndi mafumu anzake aja m'mahema, tsono adauza anthu ake aja kuti, “Konzekerani nkhondo.” Ndipo anthuwo adakonzekera kuuthira nkhondo mzindawo.

Anthu a ku Israele agonjetsa Benihadadi

13Nthaŵi imeneyo mneneri wina adadza kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele, namuuza mau a Chauta akuti, “Kodi ukuchiwona chigulu cha ankhondochi? Ndithudi ndikuchipereka chigulu chimenechi m'manja mwako lero lino. Motero udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

14Ahabu adafunsa kuti, “Kodi zimenezo zidzachitika ndi yani?” Mneneriyo adati, “Chauta akuti zidzachitika ndi ankhondo a nduna zam'maboma.” Ahabu adafunsanso kuti, “Nanga amene adzayambe nkhondoyo ndani?” Mneneriyo adati, “Iweyo.”

15Pamenepo Ahabu adasonkhanitsa ankhondo a nduna zam'maboma, ndipo onse pamodzi analipo 232. Pambuyo pake adasonkhanitsanso gulu la ankhondo a ku Israele zikwi zisanu ndi ziŵiri onse pamodzi.

16Adatuluka masana nthaŵi imene Benihadadi ndi mafumu 32 othandizana nawo aja ankamwa mpaka kuledzera m'mahema mwao.

17Ankhondo a nduna zam'maboma aja, ndiwo amene adayamba kupita ku nkhondo. Nthaŵi yomweyo Benihadadi adatuma anthu oti akazonde. Iwo adadzamuuza kuti, “Kukubwera ankhondo kuchokera ku Samariya.”

18Benihadadiyo adauza azondi aja kuti, “Ngati akubwera ndi mtendere, muŵagwire amoyo. Ngatinso akubwera ndi nkhondo, muŵagwirebe amoyo.”

19Ankhondo a nduna zam'maboma aja adayamba kuthira nkhondo pamodzi ndi gulu la ankhondo a ku Israele limene linkaŵatsata.

20Aliyense mwa iwowo adapha munthu wake. Asiriya aja adathaŵa, ndipo anthu a ku Israele adaŵalondola, koma Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, adapulumuka atakwera kavalo, iye pamodzinso ndi ankhondo ena okwera akavalo.

21Koma mfumu ya ku Israele idagwira akavalowo pamodzi ndi magaleta omwe, ndipo idagonjetsa Asiriya kotheratu.

22Pambuyo pake mneneri uja adadzanso kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele, namuuza kuti, “Tiyeni, valani chamuna, ndipo muganize bwino zoti mudzachite. Pakuti chaka chikudzachi, mfumu ya ku Siriya idzabweranso kudzamenyana nanu nkhondo.”

Nkhondo yachiŵiri ndi Asiriya

23Kwao kuja akuluakulu a mfumu ya ku Siriya adauza mfumu yao kuti, “Milungu ya anthu a ku Israele ndi milungu yam'mapiri, nchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambanira ife. Koma tiyeni tikamenyane nawo ku chigwa, ndithudi tidzaŵapambana.

24Tsono muchite izi: chotsani mafumu onse aja pa ulamuliro wao, ndipo m'malo mwao muikemo akuluakulu ankhondo.

25Kenaka musonkhanitse gulu lankhondo lofanafana ndi gulu lankhondo lidaonongeka lija, akavalo onga omwe aja, ndi magaleta onga omwe ajanso. Pambuyo pake tidzamenyana nawo ku chigwa. Ndithudi, pamenepo tidzaŵapambana.” Benihadadiyo adamvera mau a akuluakulu akewo, ndipo adachitadi momwemo.

A ku Israele agonjetsanso Asiriya kachiŵiri

26Pamene chinkafika chaka china chija, Benihadadi adasonkhanitsa gulu lankhondo la Asiriya, napita ku mzinda wa Afeki, kuti akamenyane ndi ankhondo a ku Israele.

27Anthu a ku Israele adasonkhana, ndipo atalandira zofunikira, adapita kukamenyana ndi Asiriya. Ndiye adamanga zithando zao zankhondo moyang'anana ndi Asiriya ndipo ankangooneka ngati timagulu tiŵiri ta mbuzi, m'menemo Asiriya adaadzaza dera lonselo.

28Nthaŵiyo munthu wa Mulungu adadza kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele, namuuza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Popeza kuti Asiriya akuti Chauta ndi mulungu wakumapiri osati wakuzigwa, ndipereka chigulu chonsechi kwa iwe, ndipo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta!’ ”

29Apo nkuti anthu a ku Israele ndi a ku Siriya atakhala m'zithando moyang'anana masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku la chisanu ndi chiŵiri, nkhondo idagundika. Anthu a ku Israele adakantha Asiriya okwanira 100,000 tsiku limodzi lokha, ankhondo apansi okhaokha.

30Ena otsala adathaŵira ku mzinda wa Afeki, ndipo khoma lidagwa, kugwera pa anthu okwanira 27,000, omwe adatsalawo.

Benihadadi nayenso adathaŵa, nakabisala m'chipinda cham'kati mumzindamo.

31Ndipo akuluakulu ake adamuuza kuti, “Onani tsono, ife tamva kuti mafumu a fuko la anthu a ku Israele ngachifundo. Tiyeni tivale ziguduli m'chiwuno ndi kuzeŵeza zingwe m'khosi, tipite kwa mfumu ya ku Israeleyo, mwina sakakuphani.”

32Motero adavaladi ziguduli m'chiwuno ndi kuzeŵeza zingwe m'khosi, napita kwa mfumu ya ku Israele, nkukaiwuza kuti, “Mtumiki wanu Benihadadi akunena kuti, ‘Chonde, mundisungire moyo.’ ” Ahabu adaŵafunsa kuti, “Kani akali moyobe? Iye ujatu ndi mbale wanga.”

33Tsono anthuwo adaganiza kuti mauwo ngabwino, navomera mofulumira kuti, “Inde, Benihadadi ndi mbale wanudi.” Pompo Ahabuyo adati, “Pitani mukamtenge.” Tsono Benihadadi adabweradi ndipo Ahabu adamkweza pa galeta lake.

34Benihadadi adauza Ahabu kuti, “Mizinda imene bambo wanga adalanda bambo wanu ndidzakubwezerani. Tsono mungathe kumanga nyumba zanu zamalonda ku Damasiko, monga momwe adachitira bambo wanga ku Samariya.” Ahabu adamuuza kuti, “Ukachita zimenezi, ndiye kuti ndidzakulola kuti upite.” Tsono adachita naye chipangano, namlola kuti apite.

Mneneri adzudzula Ahabu

35Tsiku lina munthu wina, mmodzi mwa aneneri, atalamulidwa ndi Chauta, adauza mneneri mnzake kuti, “Iwe, menye ndithu, ndakupemba.” Koma mnzakeyo adakana kummenya.

361Maf. 13.24 Tsono mneneri uja adati, “Popeza kuti sudamvere mau a Chauta, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndiyedi atangochoka pamenepo, adakumana ndi mkango, numupha.

37Tsono mneneriyo adapeza mneneri mnzake winanso, namuuza kuti, “Chonde, undimenye.” Mnzakeyo adammenyadi, namtematema pomumenyapo.

38Tsono mneneri uja adachokapo, nakadikirira mfumu pa njira, atadzizimbaitsa pokulunga nsalu kumaso.

39M'mene mfumu inkapita pamenepo, mneneri uja adafuula kuti, “Ine mtumiki wanu ndidapita kukailowerera nkhondo pakati penipeni. Ndipo wankhondo wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa adani athu, nanena kuti, ‘Sunga munthu uyu. Akasoŵa mwa njira iliyonse, ndiye kuti ndidzakupha kapena udzalipira ndalama 3,000 zasiliva.’

40Pamene ine mtumiki wanu ndinkatanganidwa apa ndi apa, munthuyo adazemba.” Apo Ahabu, mfumu ya ku Israele, adamuuza kuti, “Momwemo ndimo ukhalire mlandu wako. Iweyo wadzitsutsa wekha.”

41Munthuyo adachotsa msangamsanga nsalu kumaso, ndipo Ahabu adamzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri.

42Tsono mneneriyo adamuuza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Poti wamtaya munthu amene Ine ndidati umuphe, ndiye kuti iweyo ndiwe amene udzaphedwe m'malo mwa iyeyo, ndipo anthu ako adzaphedwa m'malo mwa anthu ake.’ ”

43Motero Ahabu, mfumu ya ku Israele, adabwerera kunyumba kwake mwachisoni ndi mosakondwa, naloŵa mu mzinda wa Samariya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help