1Tsono Yobe adayankha kuti,
2“Mumvetsere bwino zimene ndikulankhula,
kunditonthoza mtima kwanu kukhale komweko basi.
3Loleni ndilankhuleko,
ndikatha kulankhula, munditonzeretonzere.
4Kodi ine ndimadandaulira munthu?
Tsono ndilekerenji kupsa mtima?
5Mundipenye, ndipo mudabwe,
mugwire dzanja pakamwa.
6Ndikaganiza zimenezo, ndimachita mantha,
ndimanjenjemera kwambiri.
7“Kodi anthu oipa amakhaliranji moyo?
Bwanji amafika mpaka ukalamba,
ndi kusanduka amphamvu pa ulamuliro?
8Amaona zidzukulu zao,
ana ao amakula bwino iwo akupenya.
9Mabanja ao amakhala pabwino opanda mantha,
mkwapulo wa Mulungu suŵakhudza nkomwe.
10Ng'ombe zao zamphongo zimabereketsa nthaŵi zonse,
ng'ombe zao zazikazi sizipoloza.
11Ana ao amaseŵera pa bwalo,
namavinavina ngati anaankhosa.
12Anawo amaimba, namaliza ng'oma ndi pangwe.
Amakondwa pomva kulira kwa chitoliro.
13Masiku ao amatha iwowo akukondwa,
amatsikira ku manda mwamtendere.
14“Anthuwo amauza Mulungu kuti,
‘Tichokereni! Sitifuna kudziŵa njira zanu.
15Kodi Mphambeyo ndaninso kuti tizimtumikira?
Timapindula chiyani tikamapemphera kwa Iye?’
16Iwowo akuti amapambana chifukwa cha ntchito zao.
Koma ineyo maganizo amenewo sindigwirizana nawo.
17“Nkangati nyale ya oipa idazimapo?
Nkangati tsoka limaŵagwera?
Nkangati Mulungu amaŵakwiyira naŵalanga?
18Nkangati amaŵachotsa ngati phesi louluka ndi mphepo,
ngati mungu wouluzika ndi kamvulumvulu?
19Paja amati, ‘Mulungu amalanga mwana
chifukwa cha machimo a bambo wake.’
Ai, koma Mulungu aŵabwezere chilango ochimwawo,
kuti adziŵedi kuti Mulungu ndiye amalanga ochimwa.
20Zoonadi ochimwawo alangidwe ndithu,
alaŵe ukali wa Mphambe.
21Nanga kodi amalabadira chiyani za ana ao iyeyo atafa,
chiŵerengero cha nthaŵi yake chitatha?
22Kodi alipo wina woti angaphunzitse Mulungu nzeru,
poti Iyeyo amaweruza ngakhale anthu apamwamba?
23Ena amafa ali olemera kwambiri,
ali pabwino, ndi pa mtendere.
24Ndi onenepa, thupi lao lili nenjenenje!
Ndiponso ali ndi chuma chambiri.
25Koma ena amafa mtima wao uli woŵaŵa,
osalaŵapo chabwino chilichonse.
26Koma olemera ndi osauka omwe
onsewo amafa naikidwa m'manda, ndipo amagwa mphutsi.
27“Ndikudziŵa zimene mukuganiza,
ndikudziŵanso chiwembu chanu chimene mukuti mundichite.
28Inu mumafunsana kuti,
‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti?
Kodi hema limene munkakhala anthu oipa aja lili kuti?’
29Kodi simudaŵafunsepo anthu oyenda mu mseu?
Nanga kodi simuvomereza zimene iwowo amanena?
30Pa tsiku lakuti Mulungu alanga anthu,
munthu woipa salangidwa konse.
Amapulumuka pa tsiku loonekera mkwiyo wa Mulungu.
31Palibe ndi mmodzi yemwe
amene amadzudzula munthu woipa,
kapena kumbwezera zoipa zimene adachita.
32Pamene aikidwa m'manda,
anthu amachezera pa manda ake.
33Anthu onse amatsatira mtembo wake.
Amene amatsogola ndi osaŵerengeka,
ndipo amakaika mtembo wakewo bwinobwino.
34Nanga inu mudzandisangalatsa bwanji
ndi mau opanda pake?
Zimene mwayankhazi ndi mabodza okhaokha.”
Kukambirana kwachitatu(22.1—27.23)Elifazi
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.