Amo. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu adzalanga mitundu ya anthu

1 2Maf. 15.1-7; 2Mbi. 26.1-23; 2Maf. 14.23-29 Naŵa mau a Amosi amene ankaŵeta nkhosa ku Tekowa. Zimenezi, zodzachitikira Aisraele, Chauta adamuululira pa nthaŵi ya Uziya, mfumu ya ku Yuda, ndi pa nthaŵi ya Yerobowamu, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Israele, kutatsala zaka ziŵiri kuti chivomezi chija chichitike.

2 Yow. 3.16 Amosi adati,

“Chauta akukhuluma ku Ziyoni,

mau ake akumveka ngati bingu ku Yerusalemu.

Nchifukwa chake mabusa akuuma,

msipu wa pa phiri la Karimele ukufota.”

Chilango cha Asiriya

3 Yes. 17.1-3; Yer. 49.23-27; Zek. 9.1 Zimene akunena Chauta ndi izi:

“Chifukwa anthu a ku Damasiko

akunka nachimwirachimwira,

sindileka kuŵalanga.

Iwo ankazunza anthu a ku Giliyadi mwankhanza.

4Tsono Ine ndidzaponya moto pa nyumba ya Hazaele,

ndipo motowo udzatentha malinga a Benihadadi.

5Ndidzathyola mpiringidzo

woteteza mzinda wa Damasiko.

Ndidzaonongeratu mfumu yolamulira ku Chigwa cha Aveni,

ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu ku Betedeni.

Anthu a ku Siriya adzatengedwa ukapolo

kupita nawo ku dziko la Kiri.”

Akuterotu Chauta.

Chilango cha Afilisti

6 Yes. 14.29-31; Yer. 47.1-7; Ezek. 25.15-17; Yow. 3.4-8; Zef. 2.4-7; Zek. 9.5-7 Zimene akunena Chauta ndi izi:

“Chifukwa anthu a ku Gaza

akunka nachimwirachimwira,

sindileka kuŵalanga.

Iwo adatenga mtundu wathunthu wa anthu

kunka nawo ku ukapolo,

ndipo adaupereka ku Edomu.

7Tsono Ine ndidzaponya moto

pa makoma ozinga Gaza,

udzatentha malinga ake.

8Ndidzaonongeratu onse okhala ku Asidodi,

kudzanso iye amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni.

Ndidzakantha mzinda wa Ekeroni ndi dzanja langa,

ndipo Afilisti onse otsalira adzaonongeka.”

Akuterotu Ambuye Chauta.

Chilango cha anthu a ku Tiro

9 Yes. 23.1-18; Ezek. 26.1—28.19; Yow. 3.4-8; Zek. 9.1-4; Mt. 11.21, 22; Lk. 10.13, 14 Zimene akunena Chauta ndi izi:

“Chifukwa anthu a ku Tiro

akunka nachimwirachimwira,

sindileka kuŵalanga.

Iwo adapereka mtundu wathunthu wa anthu ku Edomu,

osasunga chipangano chaubale chija.

10Ndiye Ine ndidzaponya moto pa makoma ozinga Tiro,

ndipo motowo udzatentha malinga ake.”

Chilango cha Aedomu

11 Yes. 34.5-17; 63.1-6; Yer. 49.7-22; Ezek. 25.12-14; 35.1-15; Oba. 1.1-14; Mal. 1.2-5 Zimene akunena Chauta ndi izi:

“Chifukwa anthu a ku Edomu

akunka nachimwirachimwira,

sindileka kuŵalanga.

Iwo adathamangitsa abale ao lupanga lili kumanja,

popanda nchifundo chomwe.

Ndiponso anali ndi ukali wosatonthozeka,

ndi mkwiyo wosapozeka.

12Ndiye Ine ndidzaponya moto pa mzinda wa Temani,

ndipo motowo udzapsereza ndi malinga a ku Bozira omwe.”

Chilango cha Aamoni

13 Yer. 49.1-6; Ezek. 21.28-32; 25.1-7; Zef. 2.8-11 Zimene akunena Chauta ndi izi:

“Chifukwa Aamoni akunka nachimwirachimwira,

sindileka kuŵalanga.

Iwo pofuna kufutuza malire ao,

adatumbula akazi apakati ku Giliyadi,

14Ndiye Ine ndidzaponya moto pa makoma a ku Raba,

ndipo motowo udzapsereza malinga ake.

Padzakhala kufuula kwakukulu pa tsiku lankhondolo,

kumenyana kudzakhala kwafumbi

ngati mkuntho wa kamvulumvulu.

15Tsono mfumu yao idzatengedwa kunka ku ukapolo,

iyoyo pamodzi ndi nduna zake.”

Akuterotu Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help