1Dariusi adayera kukhosi nkuika akalonga 120 kuti azilamulira mu ufumu wake, ndi kuyang'anira madera onse a ufumuwo.
2Kenaka adasankha Daniele ndi ena aŵiri kuti akhale nduna zazikulu zoyang'anira akalongawo, kuti zinthu za mfumu zisungike bwino osaonongeka.
3Posachedwa Daniele adaonetsa kuti angathe kugwira ntchito bwino kupambana nduna zinzake ndi akalonga aja, chifukwa choti iye anali wanzeru kwambiri. Motero mfumuyo idatsimikiza zoti Daniele akhale wolamulira dziko lonse.
4Poona zimenezi, nduna zinzake ndi akalonga aja adayamba kufunafuna zolakwa pa zimene Daniele ankachita poyendetsa dzikolo. Koma sadapeze cholakwa chilichonse chifukwa Daniele anali wokhulupirika, ndipo sankachita cholakwa kapena choipa chilichonse.
5Ndiye adauzana kuti, “Sitimpeza cholakwa Daniele kupatula chinthu chokhudzana ndi chipembedzo chake.”
6Motero adapita kukaonana ndi mfumu Dariusi, namuuza kuti, “Inu amfumu, mukhale moyo mpaka muyaya.
7Tonsefe amene timayendetsa ufumu wanu, nduna zazikulu, akalonga, aphungu ndi abwanamkubwa, tapangana kuti inuyo amfumu mukhazikitse lamulo lamphamvu loti anthu onse azilitsata. Mulamule kuti pa masiku makumi atatu pasapezeke munthu wopempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu wina aliyense, kupatula kwa inu nokha basi. Aliyense wophwanya lamulo limeneli aponyedwe m'phanga la mikango.
8Tsono inu amfumu mukhazikitse lamulo limeneli, ndipo musainepo dzina lanu kuti ndi lamulo. Motero potsata malamulo a Amedi ndi Apersi amene sangathe kusinthika, ilolonso likhale losatha kusinthika.”
9Choncho Dariusi adasaina lamulo loletsa lija.
10Daniele atamva kuti lamulo limeneli lakhazikitsidwa, adaloŵa m'nyumba mwake. M'chipinda chake cham'mwamba munali mawindo oyang'ana ku Yerusalemu. Ndipo m'menemo ankagwada pansi katatu pa tsiku ndi kumapemphera ndi kutamanda Mulungu wake, monga momwe ankachitira kale.
11Adani ake ankafunafuna nthaŵi yoti amugwirire Daniele. Tsiku lina adampezadi akupemphera ndi kudandaula zina kwa Mulungu wake.
12Anthuwo adafika pamaso pa mfumu namkumbutsa za lamulo lake. Adati, “Inu amfumu, kodi suja mudakhazikitsa lamulo loti pa masiku makumi atatu akudzaŵa aliyense amene adzapemphe kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu wina, osati kwa inu nokha, ameneyo adzaponyedwe m'phanga la mikango?” Mfumuyo idayankha kuti, “Inde ndi momwemodi. Lamulo la Amedi ndi Apersi nlosasinthika.”
13Apo anthuwo adati, “Ndipotu Daniele, mmodzi mwa akapolo a ku Yuda aja, waphwanya lamulo limene inu amfumu mudakhazikitsa. Moti amapemphera kwa Mulungu wake katatu pa tsiku.”
14Pamene mfumu idamva zimenezi, idavutika kwambiri. Idayamba kuganiza zopulumutsa Daniele, ndipo idayesetsa ndithu mpaka dzuŵa tswi.
15Tsono anthu omwewo adapangana nthaŵi yoti akaonanenso ndi mfumu. Adauza mfumuyo kuti, “Amfumu, mudziŵetu kuti paja malinga ndi lamulo la Amedi ndi Apersi, palibe choletsedwa kapena cholamulidwa chokhazikitsidwa ndi mfumu chimene chingathe kusinthika.”
16Motero mfumu idalamula kuti Daniele akamtenge ndi kukamponya m'phanga la mikango. Koma tsono mfumu idauza Daniele kuti, “Mulungu wako amene umamtumikira nthaŵi zonse, akupulumutse.”
17Pakhomo pa phangalo adatsekapo ndi mwala, ndipo mfumuyo idasindikizapo chizindikiro chake ndi cha akuluakulu ake, kuti wina asasinthepo kanthu pa za Daniele.
18Mfumu idabwerera kunyumba kwake, ndipo idakhala usiku wonse osadya kanthu, osavomera zomkondweretsa zilizonse, ndipo m'maso mwake munali gwa.
19M'mamaŵa kuli mbuu, mfumuyo idadzuka, nipita ku phanga la mikango lija mofulumira.
20Itafika kumeneko, idaitana mwankhaŵa kuti, “Daniele, mtumiki wa Mulungu wamoyo! Kodi Mulungu wako amene umamtumikira nthaŵi zonse wakupulumutsa ku mikango?”
21Daniele adayankha kuti, “Amfumu, mukhale ndi moyo mpaka muyaya!
22Mulungu wanga adatuma mngelo wake kuti adzatseke pakamwa pa mikangoyi, ndipo sidandipweteke konse, chifukwa chakuti Mulungu adaona kuti ndine wosalakwa ndiponso kuti sindidakulakwireni inuyo amfumu.”
23Mfumuyo idakondwa kwambiri, ndipo idalamula kuti Daniele amtulutse m'phangamo. Motero Daniele adamtulutsa ali wosapweteka mpang'ono pomwe, chifukwa adaakhulupirira Mulungu wake.
24Tsono mfumu idalamula kuti oneneza Daniele aja akaŵagwire ndi kukaŵaponya m'phanga la mikango lija, iwowo pamodzi ndi akazi ao ndi ana ao omwe. Ndipo asanafike ndi pansi pomwe m'phangamo, mikangoyo idaŵaŵakha ndi kuŵaphwanya mafupa.
25Tsono mfumu Dariusi adalembera anthu a mitundu yonse, a mafuko onse ndi a zilankhulo zosiyanasiyana pa dziko lonse lapansi, adati, “Mtendere uchuluke pakati panu!
26Ndikuika lamulo lakuti, Anthu onse a mu ufumu wanga azimuwopa ndi kumchitira ulemu Mulungu wa Daniele:
“Iye ndi Mulungu wamoyo ndi wamuyaya,
mphamvu za ufumu wake sizidzaonongeka,
ulamuliro wake sudzatha konse.
27Iyeyo ndiye woombola, wopulumutsa,
amachita zizindikiro ndi zodabwitsa,
kumwamba ndi pa dziko lapansi.
Ndiye amene wapulumutsa Daniele ku mphamvu za mikango.”
28Motero Daniele adapeza ulemerero pa nthaŵi ya ufumu wa Dariusi ndi wa Kirusi wa ku Persiya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.