Mt. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Fanizo la anamwali khumi

1 Lk. 12.35 “Pa nthaŵi imeneyo za Ufumu wakumwamba zidzafanafana ndi zimene zidaachitikira anamwali khumi. Iwowo adaatenga nyale zao nkumakachingamira mkwati.

2Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera.

3Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera.

4Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao.

5Popeza kuti mkwati adaachedwa, onse aja adayamba kuwodzera, nagona tulo.

6“Tsono pakati pa usiku kudamveka kufuula kuti, ‘Mkwati akubwera! Tulukani, kamchingamireni!’

7Anamwali khumi aja adadzuka, nkuyamba kukonza nyale zao zija.

8Opusa aja adapempha ochenjera aja kuti, ‘Tipatseniko mafuta, onani nyale zathu zikuzima.’

9Koma ochenjera aja adati, ‘Hi, ai, tikatero satikwanira tonsefe. Bwanji osati mungopita ku sitoro mukagule anu.’

10Pamene ankakagula, mkwati adafika. Amene anali okonzekeratu aja adaloŵa naye pamodzi m'nyumba yaphwando; pambuyo pake adatseka chitseko.

11 Lk. 13.25 “Kenaka m'mbuyomwalendo anamwali ena aja nawonso adabwera nati, ‘Bwana, Bwana, titsekulireni!’

12Koma mkwatiyo adati, ‘Pepani, sindikukudziŵani!’ ”

13Pomaliza Yesu adati, “Ndiyetu inu, muzikhala maso, poti simudziŵa tsiku lake kapena nthaŵi yake.”

Fanizo la antchito atatu(Lk. 19.11-27)

14 Lk. 19.11-27 “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake.

15Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo.

16Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu.

17Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri.

18Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija.

19“Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija.

20Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’

21Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’

22Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’

23Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’

24“Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu.

25Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’

26Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu?

27Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake.

28Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo.

29Mt. 13.12; Mk. 4.25; Lk. 8.18Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.

30Mt. 8.12; 22.13; Lk. 13.28Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Chiweruzo chomaliza

31 Mt. 16.27; Mt. 19.28 “Pamene Mwana wa Munthu adzabwera ndi ulemerero wake, pamodzi ndi angelo onse, adzachita kukhalira pa mpando wake wachifumu.

32Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzaŵalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi.

33Nkhosa adzazikhazika ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi ku dzanja lake lamanzere.

34Tsono Iyeyo ngati Mfumu adzauza a ku dzanja lamanjawo kuti, ‘Bwerani kuno inu odalitsidwa a Atate anga. Loŵani mu ufumu umene adakukonzerani chilengedwere dziko lapansi.

35Mphu. 7.32-36Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu.

36Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’

37Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa?

38Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani?

39Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’

40Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’

41“Pambuyo pake Mfumuyo idzauzanso a ku dzanja lake lamanzere aja kuti, ‘Chokani apa, inu otembereredwa. Pitani ku moto wosatha, umene Mulungu adakonzera Satana ndi angelo ake.

42Ine ndidaali ndi njala, inu osandipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu osandipatsa chakumwa.

43Ndidaali mlendo, inu osandilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu osandiveka. Ndinkadwala, ndidaalinso m'ndende, inu osadzandichetsa.’

44Apo nawonso adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, kapena muli ndi ludzu, kapena wamaliseche, ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife osachitapo kanthu?’

45Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti, nthaŵi iliyonse pamene munkakana kuthandiza wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkakana kuthandiza Ine amene.’

46Dan. 12.2Pamenepo iwowo adzachoka kumapita ku chilango chosatha, olungama aja nkumapita ku moyo wosatha.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help