1Chaka cha 17 cha ufumu wa Peka mwana wa Remaliya, Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
2Ahazi anali wa zaka 20 pamene adaloŵa ufumu ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Iyeyo sadachite zolungama pamaso pa Chauta monga m'mene Davide kholo lake ankachitira.
3 adapirikitsa Ayuda ku Elati, nalanda mzindawo, kuubwezera kwa Aedomu, ndipo iwo adakhala kumeneko mpaka lero lino.
7Pamenepo Ahazi adatuma amithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya kukanena kuti, “Ine ndine mwana wanu ndiponso mtumiki wanu. Bwerani mudzandipulumutse kwa mfumu ya ku Siriya ndi kwa mfumu ya ku Israele, amene akundithira nkhondo.”
8Ndipo Ahazi adatenga siliva ndi golide amene adampeza m'Nyumba ya Chauta ndi mosungira chuma cha ku nyumba ya mfumu, namtumiza kwa mfumu ya ku Asiriya kuti zikhale ngati mphatso.
9Tsono mfumu ya ku Asiriya idamvera Ahazi ndipo idakathira nkhondo Damasiko nilanda mzindawo ndi kupha Rezini. Anthu ake idaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Kiri.
10Pamene mfumu Ahazi adapita ku Damasiko kuti akakumane ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adaonako guwa kumeneko. Tsono adatumizira wansembe Uriya chitsanzo chake cha guwalo ndi maonekedwe ake, osasiyapo nkanthu komwe.
11Ndiye wansembe Uriya adamanga guwalo, Mfumu Ahazi asanafike kuchokera ku Damasiko. Adalimanga potsata chitsanzo chimene Ahazi adaatumiza kuchokera ku Damasiko.
12Mfumu itabwera kuchokera ku Damasiko, nipenya guwa lija, idasendera pafupi ndi guwalo ndi kukwera kuguwako.
13Tsono mfumuyo idapereka nsembe yopsereza ndi chopereka cha chakudya. Idathiranso nsembe yake yachakumwa, ndipo idawaza magazi a nsembe yake yamtendere paguwapo.
14Eks. 27.1, 2; 2Mbi. 4.1 Kenaka mfumu Ahazi adachotsa guwa lamkuŵa limene linali lomangira Chauta, pakati pa guwa lake ndi Nyumba ya Chauta, ndipo adalisuntha nakalikhazika chakumpoto kwa guwa lakelo.
15Kenaka mfumuyo idalamula wansembe kuti, “Pa guwa lalikululo uperekepo nsembe zopsereza zam'maŵa, ndiponso chopereka chamadzulo cha chakudya. Uziperekanso nsembe zopsereza ndi nsembe zaufa za mfumu, ndiponso za anthu a m'dziko monsemo, pamodzi ndi zopereka za chakumwa. Ndipo pa nsembezo uwazepo magazi onse a nsembe zopsereza ndi a nsembe zonse. Koma guwa lamkuŵalo ndidzaligwiritsa ntchito poombeza.”
16Tsono wansembe Uriya adachita zonsezo, monga momwe mfumu Ahazi adaalamulira.
17 1Maf. 7.23-39; 2Mbi. 4.2-6 Pambuyo pake mfumu Ahazi adamasula mafulemu a maphaka, nachotsapo beseni. Ndipo chimbiya chimene chinali pamwamba pa ng'ombe zamkuŵa adachitsitsa ndi kuchikhazika pa maziko amiyala.
18Ndipo chifukwa chofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya, adachotsa kadenga ka pamwamba pa mpando waufumu kamene anali atakamanga m'kati mwa Nyumba ya Chauta, ndiponso adatseka khomo la panja pamene mfumu inkaloŵera m'Nyumbamo.
19Tsono ntchito zina za Ahazi pamodzi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
20Yes. 14.28 Ahazi adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.