1“Iwe Yobe, itana tsono.
Kodi alipo wina aliyense adzakuyankhe?
Kodi ndi kwa mngelo uti ungapeze thandizo?
2Pajatu mkwiyo umapha chitsiru,
ndipo njiru zimaononga wopusa.
3Ine ndidaona chitsiru chitamera mizu,
koma mwadzidzidzi nyumba yake ndidaitemberera.
4Ana ake alibe nchitetezo chomwe,
amaŵapondereza m'bwalo lamilandu,
palibe wina aliyense woŵapulumutsa.
5Anthu anjala amamdyera zokolola zake,
amamtengera ndi zapaminga zomwe.
Anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.
6Masautso satuluka m'fumbi,
ndipo zovuta sizichokera m'dothi ai.
7Koma chibadwire
munthu amangodzitengera mavuto yekha mosalephera,
monga momwe sizilepherera mbaliwali
kuulukira ku mlengalenga, kuchokera pa moto.
8“Achikhala ndinali ine,
ndikadatembenukira kwa Mulungu,
ndikadapereka mlandu wanga kwa Iye.
9 Mphu. 43.32 Ntchito zake ndi zazikulu ndi zosamvetseka.
Zodabwitsa zimene amachita ndi zosaŵerengeka.
10Amagwetsa mvula pa dziko lapansi,
ndipo amathirira minda ya anthu.
11Amakweza anthu oluluka,
ndipo amasangalatsa anthu olira.
12 1Ako. 3.19 Amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera,
kotero kuti cholinga chao sichiphula kanthu.
13Amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwao,
amathetsa msanga zimene akapsala adakonza kuti achite.
14Iwowo amakumana ndi mdima ngakhale masana,
amayambasa masanasana ngati usiku.
15Koma Mulungu amateteza amphaŵi
kwa adani oŵasinjirira,
amapulumutsa osauka kwa anthu ofuna kuŵapanikiza.
16Choncho amphaŵi amaŵalimbitsa mtima,
koma anthu oipa amaŵatseka pakamwa.
17 Miy. 3.11, 12; Ahe. 12.5, 6 “Ndi wodala munthu amene Mulungu amamdzudzula.
Nchifukwa chake usamanyoze chilango cha Mphambe.
18 Hos. 6.1 Pakuti ndiye amene amavulaza namangaponso mabala.
Amakantha, komanso manja ake amachiritsa.
19Iye adzakupulumutsa ku masautso nthaŵi ndi nthaŵi.
Zovuta sizidzakukhudza konse, zingachuluke bwanji.
20Pa nthaŵi ya njala adzakusamala,
pa nthaŵi ya nkhondo adzakupulumutsa.
21Adzakuteteza kwa anthu osinjirira,
chiwonongeko chikadzafika, sudzachiwopa.
22Pa nthaŵi ya chiwonongeko ndi ya njala uzidzaseka,
zilombo zakuthengo sudzaziwopa.
23M'minda mwako simudzakhala miyala,
nyama zakuthengo sizizakuvuta.
24Udzadziŵa kuti nyumba yako ndi malo amtendere,
udzaona kuti pa zoŵeta zako palibe chosoŵa.
25Udzadziŵa kuti ana ako adzakhala ambiri,
ndipo kuti zidzukulu zako zidzachuluka ngati udzu.
26Udzafika ku manda utakalamba,
monga m'mene zokolola zimachera pa nyengo yake.
27Iwe Yobe, zonsezi ife tazifufuzafufuza,
ndipo taona kuti ndi zoona.
Uzimvere ndi kuzitsata zimenezi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.