Mas. 83 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha kuti adani a Israele agonjetsedweSalmo. Nyimbo ya Asafu.

1Inu Mulungu, musakhalenso chete.

Musangoti phee, musangoti duu, Inu Mulungu.

2Onani, adani anu akuchita chiwawa.

Amene adana nanu akukuukirani.

3Akuchitira anthu anu upo wonyenga.

Akuŵapangira zoipa anthu anu amene mumaŵateteza.

4Iwo amati, “Tiyeni tifafanize mtundu wao wonse.

Dzina la Israele lisakumbukikenso.”

5Zoonadi, akumvana popangana chiwembu,

akupangana zokuukirani,

6anthu okhala m'mahema a Aedomu ndi Aismaele,

Amowabu ndi Ahagara,

7Agebala ndi Aamoni ndi Aamaleke,

Afilisti pamodzi ndi nzika za ku Tiro.

8Aasiriya nawonso agwirizana nawo,

kuti alimbikitse mphamvu za ana a Loti.

9 Owe. 7.1-23; Owe. 4.6-22 Muŵachite zomwe mudaŵachita Amidiyani,

Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni,

10amene adaŵaononga ku Endori,

ndi kuŵasandutsa ndoŵe m'nthaka.

11 Owe. 7.25; Owe. 8.12 Akalonga ao muŵachite

zomwe mudachita Orebu ndi Zeebu,

ndipo ana a mafumu ao onse,

muŵachite zomwe mudachita Zeba ndi Zalimuna,

12amene adati,

“Tiyeni tilande dziko la Mulungu likhale lathu.”

13Inu Mulungu wanga,

muŵasandutse ngati fumbi louluka ndi kamvulumvulu,

akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo.

14Monga momwe moto umatenthera nkhalango,

monga momwe malaŵi amayakira pa mapiri,

15momwemonso Inu muŵapirikitse ndi mkuntho,

ndipo muŵaopseze ndi kamvulumvulu wanu.

16Inu Chauta, muŵachititse manyazi,

kuti azifunafuna dzina lanu.

17Achitedi manyazi ndi mantha mpaka muyaya,

ndipo afe imfa yonyozeka.

18Adziŵe kuti Inu nokha,

amene dzina lanu ndinu Chauta,

ndinu Wopambanazonse wolamulira dziko lonse lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help