1 Yes. 23.1-18; Yow. 3.4-8; Amo. 1.9, 10; Zek. 9.1-4; Mt. 11.21, 22; Lk. 10.13, 14 Pa chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, tsiku loyamba la mwezi, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Tiro adanyodola Yerusalemu kuti, ‘Ha! Uja adaali chipata choloŵerapo mitundu ya anthuyu, waonongeka. Zipata zake zatitsekukira ife tsopano. Tilemera, poti iye tsopano wasanduka bwinja.’
3“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikukukana iwe Tiro. Ndipo ndidzakubweretsera anthu a mitundu yambiri kuti adzalimbane nawe, monga momwe mafunde am'nyanja amaŵindukira.
4Anthuwo adzaononga malinga a Tiro ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake, ndi kumsandutsa thanthwe lambee.
5Adzakhala malo oyanikapo kombe pakati pa nyanja. Mau anga ndi amenewo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Adzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina.
6Anthu a m'midzi yake yakumtunda adzaphedwa pa nkhondo. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
7“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Iwe Tiro ndidzakubweretsera Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto. Adzabwera ndi akavalo ndi magaleta, ndiponso okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu lankhondo.
8Anthu a m'midzi yako yakumtunda adzaŵapha pa nkhondo. Adzakuzinga ndi zithando zankhondo, ndiponso ndi ziwundo zankhondo. Adzakukwezera zishango kuti alimbane nawe.
9Adzagwetsa malinga ako ndi makina ogumulira, ndipo adzagwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake.
10Akavalo ake ochuluka adzakukwirira ndi fumbi lao. Malinga ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo ndiponso ndi mkokomo wa mikombero ya magaleta poloŵa pa zipata zako, monga momwe zimachitikira poloŵa mu mzinda umene wagumulidwa.
11Akavalo ake adzapondereza miseu yako yonse ndi ziboda zao. Anthu ako adzaŵapha ndi lupanga. Mizati yako yolimba adzaigwetsa.
12Adzafunkha chuma chako ndi kulanda malonda ako. Malinga ako adzaŵagumula, ndipo nyumba zako zokongola adzazigwetsa. Miyala yako, mitengo yako ndi dothi lako lomwe adzaziponya m'nyanja.
13Chiv. 18.22 Motero ndidzaletsa phokoso la nyimbo zako, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso.
14Ndidzakusandutsa thanthwe lambee. Udzasanduka malo okayanikapo kombe, ndipo sudzamangidwanso. Ine Chauta ndalankhula. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
15“Zimene Ine Ambuye Chauta ndikukuuza iwe mzinda wa Tiro ndi izi: Nyanja idzagwedezeka pamodzi ndi zilumba, pakumva za kugwa kwako, ndiponso poona opweteka akubuula, ndipo anthu akuphedwa pakati pako.
16Chiv. 18.9, 10 Pamenepo mafumu onse akunyanja adzatsika pa mipando yao yaufumu. Mikanjo yao adzaiika pambali, ndipo adzavula zovala zao zopetapeta zija. Adzachita mantha nakhala pansi akunjenjemera kosalekeza, ndipo adzangoti pakamwa gwirire poona zimene zakugwera.
17Apo adzayamba kuimba nyimbo yokudandaulira. Adzati,
“ ‘Mzinda wotchuka iwe,
nkuchita kuwonongeka chotere!
Unali wamphamvu pa nyanja,
iweyo ndi anthu ako.
Iweyo ndi anthu ako
munkaopsa anthu a m'mbali mwa nyanja.
18Tsopano maiko a m'mbali mwa nyanja akunjenjemera
chifukwa cha kugwa kwako.
Nawonso okhala ku zilumba agwidwa ndi mantha
chifukwa cha kutha kwako.’
19“Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mzinda umene munthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama am'nyanja, madzi amphamvu oti akumize.
20Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ndidzakusunga kudzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene adafa kale. Motero sudzakhalanso ndi anthu m'dziko la amoyo.
21Chiv. 18.21Ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Ngakhale anthu adzakufunefune, sadzakupezanso. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.