Yob. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1“Moyo wa munthu pa dziko lapansi

ndi wa ntchito yakalavulagaga.

Masiku ake ali ngati a munthu waganyu.

2Paja kapolo amalakalaka mthunzi,

wantchito amayembekezera malipiro ake,

3ndiye inenso ndimangovutika nthaŵi zonse.

Ngakhale usiku ndimapezabe mavuto.

4Ndikamagona ndimafunsa kuti, ‘Kodi kucha liti?’

Koma usiku ndi wautali, sindigona tulo,

ndimangoti sadabusadabu mpaka mbandakucha.

5Thupi langa ladzaza mphutsi ndi zonyansa.

Khungu langa lang'ambika, ndipo likudza mafinya.

6Masiku anga ndi othamanga

kupambana makina oombera nsalu,

amatha opanda chikhulupiriro chilichonse.

7“Inu Mulungu kumbukirani kuti

moyo wanga uli ngati mpweya.

Masiku abwino sindidzaŵaonanso.

8Amene akundiwona tsopano, sadzandiwonanso.

Nthaŵi yomwe iye adzandifunafuna,

ine ndidzakhala nditapita.

9 Lun. 2.1-4 Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka,

momwemonso munthu woloŵa ku manda sabwerako.

10Sabweranso kunyumba kwake,

ndipo onse omdziŵa amamuiŵala.

11“Nchifukwa chake sindidzatseka pakamwa.

Ndiyenera kulankhula,

chifukwa kukhosi kwanga kuli nthumanzi.

Ndiyenera kudandaula,

chifukwa mumtima mwanga muli zoŵaŵa.

12Kodi ine ndine nyanja, kapena chilombo cham'nyanja,

kuti inu mundiikire alonda?

13Ndikagona pansi kuti ndithuze mtima,

ndi kupeza mpumulo pabedi panga,

14inu mumandichititsa mantha ndi maloto,

mumandiwopsa ndi zinthu zondiwonekera m'masomphenya.

15Choncho ndikadasankha kudzikhweza kapena kufa kumene,

kupambana kupirira zovuta

zimene ndikuzimva m'thupi mwanga.

16Ndatopa nawo moyo wanga,

sindingakonde kukhala moyo nthaŵi zonse.

Ingondisiyani, poti moyo wanga uli ngati mpweya chabe.

17 Mas. 8.4; 144.3 Inu Mulungu, kodi munthu nchiyani,

kuti muzimganizira chotere,

kuti muzisamala zochita zake?

18Mumampenyetsetsa masiku onse,

ndipo mumamuyesa nthaŵi zonse.

19Kodi mudzaleka liti kumandizonda,

kuti ndingopezako mpata womeza malovu?

20Kodi ndikachimwa, ndimakuvutani bwanji,

Inu Wopenyetsetsa anthu?

Chifukwa chiyani mwandiika kuti ndikhale

ngati choponyerapo chandamale chanu?

Chifukwa chiyani ndikukhala ngati

katundu wolemera kwa Inu?

21Chifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga

ndi kundichotsera zolakwa zanga?

Nthaŵi yoti ndiloŵe m'manda ili pafupi.

Inu mudzandifunafuna, koma simudzandiwonanso.”

Bilidadi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help