1Pali ntchito inanso yosiyana zedi,
ntchito ya munthu woika mtima pa kuphunzira za
Malamulo a Wamphamvuzonse.
Munthu ameneyo amafufuzafufuza nzeru za anthu akale
ndipo amaika mtima pa zimene aneneri adanena.
2Amasonkhanitsa nkhani za anthu otchuka
ndipo amayesetsa kulondola nzeru zozama
za mafanizo.
3Amasanthula matanthauzo obisika a miyambi
ndipo amatha kulongosola zinsinsi za nthano.
4Amagwira ntchito yotumikira akuluakulu
ndipo amapezeka pakati pa olamulira.
Amayenda ku maiko achilendo
kuti akafufuze za makhalidwe oipa ndi abwino a anthu.
5Amachita khama kuuka m'mamaŵa
kuthamangira kwa Ambuye, Mlengi wake,
ndipo amapemphera kwa Mulungu Wopambanazonse.
Amapemphera ndi mtima wonse ndi pakamwa pomwe
napepesa kuti amkhululukire machimo ake.
6Ambuye, Mulungu wamkulu, akafuna,
adzamdzaza nazo nzeru zodziŵira zinthu.
Pamenepo munthuyo adzalalika mau anzeru,
ndipo adzayamika Ambuye popemphera.
7Adzaongolera maganizo ake ndi nzeru zake pakuphunzira,
ndipo adzasinkhasinkha zachinsinsi
zimene adaphunzirazo.
8Pa zophunzitsa zake adzadziŵika
kuti ndi wanzeru,
adzanyadira Malamulo
a chipangano cha Ambuye.
9Ambiri adzamtamanda chifukwa cha nzeru zake,
ndipo sizidzaiŵalika.
Mbiri yake sidzafafanizika,
dzina lake lidzakhala lotchuka pa mibadwo yonse.
10Mitundu ya anthu idzakamba za nzeru zake,
ndipo mpingo udzamuyamika pa msonkhano.
11Akadzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali,
adzakhala wotchuka koposa anthu chikwi chimodzi.
Akadzafa msanga,
mbiri yakeyo idzamkwanira.
Nyimbo yotamanda Mulungu12Mumtima mwangamu muli zinanso zambiri zoti ndinene.
Ndili wodzaza monga m'mene umaonekera mwezi wathunthu.
13Ndimvereni, ana anga ouzika,
mukule monga duŵa lokongola lobzala m'mbali mwa mtsinje.
14Mwazani fungo lokoma ngati lubani,
phukani maluŵa ngati kakombo.
Mwazani fungo lokoma,
imbani nyimbo yotamanda.
Tamandani Ambuye chifukwa cha ntchito zao zonse.
15Lalikani za ukulu wa dzina la Ambuye,
muŵayamike ndi kuŵatamanda ndi nyimbo zapakamwa ndi azeze.
Muŵatamande ndi mau akuti,
16“Zonse zimene Ambuye adalenga nzabwino kwambiri.
Zonse zimene amalamula zimachitika pa nthaŵi yake.”
17Munthu wina asafunse kuti, “Kodi ichi nchiyani?
Nanga izo bwanji?”
Funso lililonse lili ndi nthaŵi yake.
Pamene Ambuye adalankhula, madzi adaundana,
mau ake adapanga maiŵe a madzi.
18Akalamula, chilichonse chimachitikadi momwe afunira,
palibe munthu amene angachepetse mphamvu zake zopulumutsira.
19Amaona zochita za anthu onse,
palibe choti nkubisira maso ake.
20Amakhala maso chiyambire cha nthaŵi mpaka muyaya,
palibe chinthu chodabwitsa pamaso pa Ambuye.
21Munthu wina asafunse kuti, “Kodi ichi nchiyani?
Nanga izo bwanji?”
Chinthu chilichonse chidalengedwa ndi cholinga chake.
22Madalitso ake ali ngati mtsinje wosefukira
umene umanyowetsa nthaka youma.
23Koma anthu akunja amaŵakwiyira,
monga adasandulitsa madzi abwino kuti akhale amchere.
24Kwa anthu oyera mtima njira za Mulungu nzolungama
koma kwa anthu ochimwa nzokhumudwitsa.
25Kuyambira pa chiyambi zinthu zabwino zidalengedwa
chifukwa cha anthu abwino,
zinthu zoipa zidalengedwa chifukwa cha anthu ochimwa.
26Zinthu zofunika kwambiri pa moyo wa munthu ndi izi:
madzi, moto, chitsulo, mchere,
ndiponso ufa, uchi, mkaka, vinyo, mafuta ndi zovala.
27Zonsezi nzabwino kwa anthu oopa Mulungu,
koma zimasanduka zoipa kwa anthu ochimwa.
28Pali mphepo zina zimene zidalengedwa kuti zizilanga anthu,
ndipo mkuntho wake umaŵasautsa.
Pa nthaŵi ya chiwonongeko zimaonetsa mphamvu zake,
zimapoza ukali wa amene adazilenga.
29Moto ndi matalala, njala ndi imfa,
zonsezi zidalengedwa kuti zikhale chilango.
30Zilombo, zinkhanira, mamba ndi lupanga
zimenezi nzolanga anthu osapembedza ndi kuŵaononga,
31Zonsezi zimakondwera kuchita zimene Mulungu amalamula.
Nzokonzeka kutumikira Ambuye pamene kufunikira,
ndipo nthaŵi yake ikakwana sizinyozera malamulo ake.
32Ndidazivomera zonsezi chiyambire,
ndipo nditaganizaganiza ndidalemba kuti,
33“Ntchito zonse za Ambuye nzabwino,
amapereka zonse zofunika pa nthaŵi yake.”
34Munthu wina asanene kuti,
“Ichi si chabwino ngati icho,”
chifukwa zinthu zonse zidzadziŵika kuti nzabwino
pa nthaŵi yake.
35Tiyeni tsopano, ndi mtima wanu wonse muimbe mokweza,
ndipo mutamande dzina la Ambuye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.