2 Mbi. 30 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Akonzekera chikondwerero cha Paska

1 Num. 9.9-11 Hezekiya adatumiza mau ku Israele konse ndi ku Yuda, ndipo adalembanso makalata kwa Aefuremu ndi kwa Amanase kuti, “Mubwere ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, kudzachita mwambo wa Paska ya Chauta, Mulungu wa Israele.

2Pakuti mfumu, nduna zake ndi anthu onse a ku Yerusalemu anali atapangana kuti azichita Paska pa mwezi wachiŵiri.

3Zidaatero chifukwa sankatha kuchita Paskayo pa nthaŵi yake, popeza kuti ansembe oyeretsedwa anali osakwanira, ndipo anthu nawonso anali asanasonkhane ku Yerusalemu.

4Zimenezi zidakomera mfumu ndi msonkhano wonse.

5Choncho anthuwo adatsimikiza zoti alengeze ku Israele konse, kuyambira ku Beereseba mpaka ku Dani, kuti anthu abwere kudzachita Paska ya Chauta, Mulungu wa Israele, ku Yerusalemu, pakuti si ambiri ankachita Paskayo monga kudaalembedwera.

6Motero amithenga adapita ku Israele konse ndi ku Yuda, atatenga makalata a mfumu ndi a nduna zake. Makalatawo ankanena kuti, ‘Inu Aisraele, bwererani kwa Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele, kuti Iyeyo abwerenso kwa otsalanu, amene mudapulumuka kwa mafumu a ku Asiriya.

7Musati mukhale ngati makolo anu ndi abale anu amene sadakhulupirire Chauta, Mulungu wa makolo ao, kotero kuti adaŵaononga monga momwe mukuwoneramu.

8Musati muumitse makosi anu monga m'mene ankachitira makolo anu, koma mudzipereke kwa Chauta, ndipo muzibwera ku Nyumba yake imene Chautayo waiyeretsa mpaka muyaya. Ndipo muzitumikira Chauta, Mulungu wanu, kuti mkwiyo wake woopsa ukuchokeni.

9Chifukwatu ngati inu mubwerera kwa Chauta, anthu amene adagwira ukapolo abale anu ndi ana anu, adzachita chifundo, ndipo abale anuwo adzabweranso ku dziko lino. Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi wokoma mtima ndi wachifundo, ndipo sadzakufulatirani ngati mubwerera kwa Iyeyo.’ ”

10Choncho amithenga aja adapita ku mzinda uliwonse m'dziko lonse la Efuremu ndiponso m'dziko lonse la Manase mpaka kukafika ku Zebuloni. Koma anthu ankaŵaseka monyodola nkumaŵalalatira.

11Anthu pang'ono chabe a ku Asere ndi a ku Manase ndiponso a ku Zebuloni adadzichepetsa napita ku Yerusalemu.

12Dzanja la Mulungu linalinso ndi anthu a ku Yuda, kuti aŵapatse mtima umodzi wochita zimene mfumu ndi nduna zake adaalamula, monga momwe Chauta adaanenera.

Achita Paska

13Choncho anthu ambiri adabwera ku Yerusalemu kudzachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa pa mwezi wachiŵiri. Unali msonkhano waukulu kwambiri.

14Anthuwo adayambapo kumagwira ntchito, ndipo ku Yerusalemuko adachotsa maguwa operekapo nsembe ndi ena ofukizirapo lubani, nakaŵataya ku chigwa cha Kidroni.

15Ndipo adapha mwanawankhosa wa Paska pa mwezi wachiŵiri. Choncho ansembe ndi Alevi adachita manyazi, kotero kuti adadziyeretsa, nabwera ndi nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta.

16Adakhala m'malo mwao potsata lamulo la Mose, munthu wa Mulungu uja. Ansembewo adawaza magazi amene adalandira kwa Alevi.

17Pakuti mumsonkhanomo munali anthu ambiri amene sadadziyeretse, Alevi ndiwo adayenera kupha mwanawankhosa wa Paska wa munthu aliyense amene anali woipitsidwa pa zachipembedzo, kuti aiyeretse nsembeyo pamaso pa Chauta.

18Ndiye kuti chinamtindi cha anthu, ambiri mwa iwo a ku Efuremu, a ku Manase, a ku Isakara ndi a ku Zebuloni, anali oipitsidwa pa zachipembedzo. Koma adadya naobe Paska, monyozera mwambo wolamulidwa. Koma Hezekiya adaaŵapempherera kuti, “Chauta, Mulungu wabwino, mukhululukire munthu aliyense

19amene amaika mtima pa kufunafuna Mulungu, Chauta, Mulungu wa makolo ake, ngakhale kuti munthuyo sadatsate malamulo onena za kuyeretsedwa koyenera Nyumba ya Chauta.”

20Ndipo Chauta adamvera Hezekiya naŵachiritsa anthuwo.

21Tsono anthu a ku Israele amene analipo ku Yerusalemu kuja, adachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri, ndipo adasangalala kwambiri. Alevi pamodzi ndi ansembe ankatamanda Chauta tsiku ndi tsiku, akumuimbira ndi mphamvu zao zonse.

22Tsono Hezekiya adalankhula moŵalimbitsa mtima Alevi onse ogwira ntchito ya Chauta mwaluso. Choncho anthuwo adachita chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri, napereka nsembe zachiyanjano ndi kuthokoza Chauta, Mulungu wa makolo ao.

Apitiriza chikondwerero cha Paska

23Pambuyo pake msonkhano wonse udavomerezana zopitiriza chikondwererocho masiku asanu ndi aŵiri ena. Choncho adachitadi chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri ena mosangalala.

24Hezekiya mfumu ya ku Yuda adaapereka ng'ombe zamphongo 1,000 ku msonkhanowo, ndiponso nkhosa 7,000 zoyenera kuzipereka ku nsembe. Nduna zake zidaperekanso ng'ombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 10,000. Ansembe ambirimbiri adadziyeretsa.

25Msonkhano wonse wa ku Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, gulu lonse la anthu amene adaachokera ku Israele, alendo ongokhala nao amene adaachokera ku dziko la Israele, ndiponso alendo ongokhala nao a ku dziko la Yuda, onsewo adakondwa.

26Choncho kunali chikondwerero chachikulu ku Yerusalemu, pakuti kuyambira nthaŵi ya Solomoni, mwana wa Davide, mfumu ya Israele, sizidachitikepo zotere ku Yerusalemu.

27Tsono ansembe pamodzi ndi Alevi adaimirira nadalitsa anthu. Mau ao adamveka, ndipo pemphero lao lidakafika ku malo oyera a Mulungu kumwamba.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help