Mas. 45 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo ya pa ukwati wa mfumuKwa Woimbitsa Nyimbo. Kutsata maimbidwe a nyimbo ya Akakombo. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo yapaukwati.

1Mtima wanga wadzaza ndi nkhani yokoma.

Ndikuimbira mfumu nyimbo yangayi.

Lilime langa lili ngati cholembera cha katswiri

wodziŵa kulemba bwino.

2Inu ndinu wokongola kwambiri kuposa anzanu ena onse.

Pakamwa panu pamatulutsa zokoma zokhazokha.

Nchifukwa chake Mulungu wakudalitsani mpaka muyaya.

3Inu ngwazi yolimba mtima,

mangirirani lupanga lanu m'chiwuno,

mu ulemerero ndi ukulu wanu.

4Pitani ndi ulemerero wanuwo,

kuti mukagonjetse adani anu onse,

mukateteze zimene zili zoona,

zachifatso ndi zachilungamo.

Dzanja lanu lamanja likaonetse ntchito zanu zoopsa.

5Mivi yanu ndi yakuthwa,

imalasa mitima ya adani.

Mitundu ina ya anthu imagwa pansi pamaso panu.

6 Ahe. 1.8, 9 Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, ndi wamuyaya,

mumaweruza molungama mu ufumu wanu.

7Mumakonda chilungamo ndipo mumadana ndi zoipa.

Nchifukwa chake Mulungu, Mulungu wanu, wakusankhani.

Wakudzozani ndi kukusangalatsani

kupambana anzanu ena onse.

8Zovala zanu nzonunkhira mure, aloe ndi kasiya.

Nyumba zanu zachifumu nzomangidwa ndi mnyanga.

M'menemo zoimbira zansambo zimakusangalatsani,

9ana aakazi a mafumu

ali m'gulu la mbumba zanu zolemekezeka.

Ku dzanja lanu lamanja kwaima mfumukazi,

yovala zovala za golide wa ku Ofiri.

10Tsono mvera kuno, mkwati wamkaziwe,

imva mau anga ndipo uŵaganizire bwino.

Iŵala abale ako ndiponso nyumba ya bambo wako.

11Mfumu idzakukonda

chifukwa cha kukongola kwako.

Umuŵeramire popeza kuti ndiye mbuyako.

12Anthu a ku Tiro adzakukopa ndi mphatso,

olemera kwambiri adzakunyengerera

13ndi chuma chao chamitundumitundu.

Mwana wamkazi wa mfumu ali m'chipinda mwake,

wadzikongoletsa kwambiri,

wavala zovala zoluka ndi thonje lagolide.

14Akupita naye kwa mfumu atavala zovala zamaluŵa,

pamodzi ndi anamwali anzake omperekeza.

15Akuŵaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo

pokaloŵa m'nyumba ya mfumu.

16Inutu zidzukulu zanu

zidzaloŵa m'malo mwa makolo anu,

mudzaŵasandutsa mafumu pa dziko lonse lapansi.

17Ndidzamveketsa mbiri ku mibadwo yonse,

nchifukwa chake mitundu ya anthu

idzakutamandani mpaka muyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help