Lun. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

CHILUNGAMO NDIYE GWERO LA MOYOWofuna Mulungu ayenera kuleka zoipa

1 Lun. 6.1-11 Muzikonda chilungamo,

inu olamulira dziko lino lapansi.

Muzikhala ndi maganizo olongosoka

pa kusinkhasinkha za Ambuye.

Muzifunafuna Iwowo ndi mtima woona.

2Pajatu amene sapenekera Ambuye, amaŵapezadi,

ndipo Ambuyewo amadziŵonetsa

kwa anthu oŵakhulupirira.

3Maganizo opotoka amalekanitsa anthu ndi Mulungu,

ndipo Iye amaŵachititsa manyazi

anthu opusa, ofuna kupeputsa mphamvu zake.

4Luntha sililoŵa mu mtima wa munthu wonyenga,

silikhala mwa munthu wogonjera machimo.

5Mzimu woyera, wophunzitsa anthu,

umaŵathaŵa anthu onyenga,

sukhalapo pamene pali maganizo opusa;

umakhumudwa ndi makhalidwe osalungama.

Mulungu amadziŵa maganizo athu

6Luntha ndi mzimu wachifundo kwa anthu,

koma sililekerera munthu

wonyoza Mulungu mwachipongwe,

chifukwa Mulungu amadziŵa zam'kati zonse,

amafufuza za mumtima mwa munthu

ndi kumva zimene amalankhula.

7Ndithudi, mzimu wa Ambuye wadzaza

pa dziko lonse lapansi,

umagwirizira zinthu zonse pamodzi,

umadziŵa zonse zimene anthu amalankhula.

8Nchifukwa chake munthu wolankhula zoipa sangabisale,

chilungamo sichidzalephera kumutsutsa.

9Munthu wonyoza Mulungu adzazengedwa mlandu

pa zolinga zake,

nkhani yake idzafika mpaka kwa Ambuye

ndipo adzamutsutsa kuti ndi wopalamula ndithu.

10Khutu latcheru la Mulungu limamva zonse,

limamva ngakhale madandaulo ong'ung'udza.

11Tsono chenjerani

kuti musamangoŵiringula pachabe,

ndipo musakhale akazitape,

chifukwa ngakhale zonena kuseri

zimakhala ndi zotsatira zake,

ndipo wokamba zonama

amaononga moyo wamumtima.

Mulungu sadalenge imfa

12Musadziitanire imfa

ndi mayendedwe anu oipa,

kapena kudzigwetsera chiwonongeko

ndi ntchito za manja anu.

13 Ezek. 18.32; 33.11; 2Es. 3.7; 2Pet. 3.9 Mulungu sadapange imfa,

sakondwera ndi imfa ya anthu amoyo.

14Iye adalenga zonse kuti zizikhalapo.

Zolengedwa zonse za m'dziko lapansi nzabwino,

zilibe ululu wopha anthu.

Imfa ilibe ulamuliro pansi pano,

15chifukwa chilungamo chidzakhalapo

mpaka muyaya.

16 Miy. 8.36; Yes. 28.15; Mphu. 14.12 Koma anthu osamvera Mulungu

amadziitanira imfa,

chifukwa cha ntchito zao ndi mau ao.

Amaisandutsa ngati bwenzi lao,

ndipo amailakalaka kwabasi.

Amachita nayo chipangano,

motero ayeneradi kukhala m'gulu lake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help