Yes. 22 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ulosi wonena za Yerusalemu

1Nawu ulosi wonena za chigwa chooneramo zinthu m'masomphenya:

Kodi chachitika nchiyani

kuti nonse mukwere pa madenga?

2Ndinu anthu osokera,

okhala mu mzinda wachiwawa ndi waphokoso.

Anthu anu ophedwa sadaphedwe ndi lupanga,

kapena kufera pankhondo.

3Atsogoleri anu onse adathaŵa nagwidwa,

osaponyako ndi muvi umodzi womwe.

Nonsenu amene mudapezeka mudagwidwa,

ngakhale mudaathaŵiratu adani akali kutali.

4Nchifukwa chake ndidati,

“Muchoke, mundileke ndilire ndi mtima woŵaŵa.

Musayese kundipepesa

pa za kuwonongeka kwa abale anga.”

5Nthaŵi ino ndi yamavuto,

yogonjetsedwa ndiponso yachisokonezo

m'chigwa chooneramo zinthu m'masomphenya.

Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse,

ndiwo atichita zimenezi.

Malinga adagumuka

ndipo anthu adakalirira ku mapiri.

6Ankhondo a ku Elamu adadza atakwera pa akavalo,

m'manja muli mauta ndi mivi,

ndipo ankhondo a ku Kiri

anali okonzeka ndi zishango zao.

7Zigwa zanu zachonde zinali zodzaza ndi magaleta,

ndipo asilikali okwera pa akavalo

adakaima kumaso kwa zipata za mzinda.

8Zonse zoteteza Yuda zidalandidwa.

Tsiku limenelo mudayang'ana ku zida zankhondo zimene zinali m'Nyumba ya Nkhalango ija.

9Mudapeza malo ena m'makoma a mzinda wa Yerusalemu ali ogumuka. Mudasunga madzi m'chidziŵe chakunsi.

10Mudaŵerenga nyumba zonse mu mzinda wa Yerusalemu, ndipo mudagwetsa zina kuti mupeze miyala yokonzera makoma a mzindawo.

11Pakati pa makoma aŵiri mudamangapo chitsime chosungiramo madzi ochokera ku chidziŵe chakale. Koma simudaganizeko za Mulungu amene adachititsa zimenezi, simudasamaleko za Iye amene adazikonza kale lomwe.

12Nthaŵi imeneyo Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse,

adakuitanani kuti mulire ndi kudza misozi,

kumeta ndi kuvala ziguduli.

13 1Ako. 15.32 Koma inu mudakondwa ndi kusangalala,

mudapha ng'ombe ndi nkhosa ndi kuzidya,

ndiponso mudamwa vinyo.

Mudati, “Tidye, timwe, poti maŵa tifa.”

14Chauta Wamphamvuzonse adandiwululira

pondinong'oneza m'khutu kuti,

“Ndithudi, tchimo limeneli

sindidzakukhululukirani mpaka kufa kwanu,”

akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.

Ulosi wonena za Sebina

15Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adandiwuza kuti ndipite kwa Sebina, kapitao woyang'anira nyumba yaufumu, kukamufunsa kuti,

16“Kodi ukuchita chiyani kuno? Walimba mtima bwanji kuti udzikumbire manda kuno, kudzikumbira manda pa phiri, ndi kudzisemera mopumulira m'thanthwe?

17Chauta adzakugwira dzolimba ndi kukuponya mwamphamvu, iweyo wanyongawe.

18Adzakusandutsa ngati mpira ndipo adzakuponya m'dziko lalikulu. Kumeneko nkumene ukafere, ndipo magaleta ako amene unkanyadira adzatsalira komwekonso, iwe wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wakowe.

19Chauta adzakuchotsa pa ukapitao wako, ndipo adzakutsitsa pakuthetsa udindo wako.”

20Chauta adauza Sebina kuti, “Tsiku limenelo ndidzaitana mtumiki wanga Eliyakimu, mwana wa Hilikiya.

21Ndidzam'veka mkanjo wako ndi lamba wako ndi kumpatsa ulamuliro wako. Tsono adzalamulira anthu onse okhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda.

22Chiv. 3.7 Ndidzampatsa makii a ulamuliro wa pa banja la mfumu Davide. Akadzatsekula, palibe amene adzatseke. Ndipo adzatseka, popanda wina wotsekula.

23Ndidzamulimbitsa ngati chikhomo pa udindo wakewo, ndipo adzakhala wopatsa ulemu kwa banja la atate ake.

24“Koma ana ndi adzukulu ake adzakhala katundu wolemera pa iye m'banja la atate ake, monga ngati ziŵiya zonse zimene zimapachikidwa pa chikhomo.

25Tsiku limenelo chikhomo chokhoma dzolimba chija chidzasukusa, chidzazuka ndipo chidzagwa. Tsono zonse zopachikidwa pachikhomopo zidzaonongedwa.” Akutero Chauta Wamphamvuzonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help