1Chifukwa cha zimenezi Yona adakhumudwa kwambiri, nakwiya.
2Eks. 34.6Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, nzimenezitu zimene ndinkaopa ndili kwathu. Nchifukwa chake ndidaayesetsa kuthaŵira ku Tarisisi. Ndidaadziŵa kuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, woleza mtima ndi wa chikondi chosasinthika, ndiponso wokhululukira machimo nthaŵi zonse.
31Maf. 19.4Ndiye tsono Inu Chauta, ndapota nanu, ingondiphani basi. Nkhwabwino kuti ndife kupambana kukhala moyo.”
4Chauta adamufunsa kuti, “Kodi iwe wachita bwino pokwiya chotere?”
5Yona adatuluka mumzindamo nakakhala pansi chakuvuma kwake. Kumeneko adadzimangira chithando nakhala m'menemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitike mumzindamo.
6Tsono Chauta Mulungu adameretsa msatsi kuti uchitire Yona mthunzi ndi kumchotsa mavuto ake. Yona adakondwa kwambiri chifukwa cha msatsiwo.
7Koma m'maŵa mwake mbandakucha, Mulungu adatuma mphanzi kuti ikadye msatsiwo, ndipo udafota.
8Pamene dzuŵa linkatuluka, Chauta adautsira Yona mphepo yotentha kuti iwombe kuchokera kuvuma. Dzuŵa lidamtentha pa mutu Yona, mpaka kulenguka nalo. Tsono adapempha kuti afe, adati, “Nkwabwino kuti ndife kupambana kukhala moyo.”
9Koma Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi wachita bwino pokwiya chifukwa cha msatsiwu?” Iye adati, “Inde ndachita bwino kukwiya. Kukwiya kwake nkofa nako.”
10Chauta adati, “Iwe ukumvera chisoni msatsi umene sudaugwirire ntchito, sindiwe udaubzala ndi kuukuza. Udamera pa usiku umodzi, nufanso pa usiku umodzi.
11Nanga Ine, kodi sindiyenera kuumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M'mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziŵa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziŵeto zochuluka.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.