1Aisraele adanyamuka ulendo nakamanga mahema ao m'zigwa za Amowabu patsidya pa Yordani ku Yeriko.
Mfumu ya Amowabu iitana Balamu2Balaki mwana wa Zipora adaona zonse zimene Aisraele adachita Aamori.
3Amowabu adaopa anthuwo kwambiri, chifukwa anali ambirimbiri. Amowabu adachitadi mantha ndi Aisraele.
4Choncho Amowabuwo adauza akuluakulu a ku Midiyani kuti, “Tsopano khamu limeneli libudula zonse zimene zatizungulira, monga momwe ng'ombe zimabudulira udzu wam'munda.” Pamenepo Balaki mwana wa Zipori amene anali mfumu ya Mowabu nthaŵi imeneyo,
5Num. 31.8; 2Pet. 2.15, 16; Yuda 1.11 adatuma amithenga kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate m'dziko la kwao, kuti akamuitane ndi kumuuza kuti, “Anthu ochokera ku Ejipito adzaza dziko lonse, ndipo akuyang'anana ndi ine.
6Bwerani tsono muŵatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga, poti ngamphamvu kopambana ine. Mwina mwake ndidzatha kuŵagonjetsa ndi kuŵapirikitsa m'dziko mwanga. Pakuti ndikudziŵa kuti amene inu mumamdalitsa, amadalitsidwa, ndipo amene mumamtemberera, amatembereredwa.”
7Choncho akalonga a ku Mowabu ndi akalonga a ku Midiyani adanyamuka, atatenga ndalama m'manja zokaombedzera. Tsono adafika kwa Balamu namuuza mau a Balaki.
8Balamu adaŵauza kuti, “Gonani konkuno lero, ndipo ndikubwezerani mau monga momwe Chauta andiwuzire.” Choncho akalonga a ku Mowabu adagona kwa Balamu.
9Ndipo Mulungu adadza kwa Balamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iweŵa ndani?”
10Balamu adayankha kuti, “Balaki mwana wa Zipora mfumu ya Mowabu, watumiza uthenga kudzandiwuza kuti,
11‘Anthu amene achokera ku Ejipito, adzaza dziko lonse. Bwerani tsono, muŵatemberere m'malo mwanga, mwina mwake ndidzatha kumenyana nawo nkhondo ndi kuŵapirikitsa.’ ”
12Apo Mulungu adauza Balamu kuti, “Usapite nao, ndipo usaŵatemberere anthuwo, chifukwa ngodalitsidwa.”
13Tsono Balamu adadzuka m'maŵa, naŵauza akalonga a Balaki aja kuti, “Bwererani ku dziko lakwanu, pakuti Chauta sadandilole kuti ndipite nanu.”
14Tsono akalonga a Mowabu aja adanyamuka napita kwa Balaki, ndipo adakamuuza kuti, “Balamu wakana kubwera.”
15Balaki adatumanso akalonga ochuluka ndi olemekezeka kopambana oyamba aja.
16Iwo adafika kwa Balamu namuuza kuti, “Balaki mwana wa Zipora akunena kuti, ‘Musalole kuti chinthu chilichonse chikuletseni kubwera kwa ine.
17Ndithudi, ndidzakuchitirani ulemu waukulu, ndipo chilichonse chimene mundiwuze, ndidzachita. Bwerani, mudzatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga.’ ”
18Koma Balamu adayankha atumiki a Balakiwo kuti, “Ngakhale Balaki akadati andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindikadatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta, Mulungu wanga, wandilamula. Sindikadatha kuchepetsa kapena kuwonjeza.
19Ndiye inu tsono, gonani konkuno usiku uno, monga adachitira anzanu aja, kuti ndidziŵe ngati pali zina zimene Chauta andiwuze.”
20Ndipo Mulungu adadza kwa Balamu usiku umenewo namuuza kuti, “Ngati anthuwo abwera kudzakuitana, nyamuka upite nao. Koma ukachite zokhazo zimene ndikakulamule.”
Za Balamu ndi bulu wake21Choncho Balamu, atadzuka m'maŵa mwake, adaika chishalo pa bulu wake, ndipo adanyamuka pamodzi ndi akalonga aja.
22Komabe Mulungu adapsa mtima chifukwa choti Balamuyo adapita. Ndipo mngelo wa Chauta adaimirira mu mseu, kuti amtsekere njira. Pamenepo nkuti atakwera bulu, ndipo ali ndi anyamata ake aŵiri.
23Bulu uja adaona mngelo wa Chauta ataima mu mseu, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono bulu adasiya mseu nakaloŵa m'munda. Apo Balamu adammenya bulu uja kuti abwerere mu mseu.
24Pambuyo pake mngelo wa Chauta uja adakaimirira m'kanjira kophaphatiza, kodzera pakati pa minda yamphesa, kokhala ndi khoma pa mbali zonse ziŵiri.
25Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adadzipanikiza ku khoma, nakanikiza phazi la Balamu kukhomako. Pomwepo Balamu adamenya buluyo kachiŵiri.
26Kenaka mngelo wa Chauta adatsogolako nakaimiriranso pa malo ophaphatiza, opanda koti nkutembenukira kumanja kapena kumanzere.
27Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adagona pansi, Balamu ali pamsana pake. Balamu adapsa mtima kwambiri, namenya buluyo ndi ndodo yake.
28Pamenepo Chauta adatsekula pakamwa pa buluyo, ndipo adalankhula, nafunsa Balamu kuti, “Kodi ndakuchitani chiyani kuti muzindimenya chotere katatu?”
29Balamu adauza buluyo kuti, “Chifukwa choti ukuseŵera nane, ndikadakhala ndi lupanga m'manja mwanga, ndikadakupha.”
30Buluyo adafunsanso Balamu kuti, “Kodi sindine bulu wanu amene mwakhala mukundikwera moyo wanu wonse mpaka lero lino? Kodi zimenezi ndidakuchitiranipo nkale lonse?” Balamu adayankha kuti “Iyai.”
31Pomwepo Chauta adatsekula maso a Balamu, ndipo adaona mngelo wa Chauta ataimirira m'njira, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono Balamu adazyolika, nadziponya pansi.
32Mngelo wa Chauta adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako chotere katatu? Ndabwera kudzakutsekera njira, chifukwa ulendo wakowu ukundiipira.
33Bulu wako anandiwona, ndipo anasiya njira katatu konse atandiwona. Akadapanda kusiya njira atandiwona, ndithu ndikadakuphera pomwepo, koma buluyo ndikadamleka kuti akhale moyo.”
34Balamu adayankha mngelo wa Chauta uja kuti, “Ndachimwa. Sindinalikudziŵa kuti mukunditsekera njira. Nchifukwa chake tsono, ngati zakuipirani, ndibwerera.”
35Apo mngelo wa Chauta adauza Balamu kuti, “Pita nawo anthuŵa. Koma ukanene zokhazo zimene ndikakuuze.” Choncho Balamu adapitirira ulendo wake pamodzi ndi akalonga a Balaki aja.
Balaki achingamira Balamu36Balaki atamva kuti Balamu wafika, adatuluka kukamchingamira ku mzinda wina wokhala pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, umene umachita malire a dziko la Mowabu, kumapeto kwake kwenikweni.
37Ndipo Balaki adafunsa Balamu kuti, “Kodi sindidakutumireni mithenga yodzakuitanani? Chifukwa chiyani simudabwere? Kodi sindingathe kukuchitirani ulemu?”
38Balamu adayankha Balaki kuti, “Inde, ndabwera, koma kodi ndili ndi mphamvu zoti ndilankhule chinthu chilichonse? Ndiyenera kulankhula zokhazo zimene Mulungu andiwuze.”
39Tsono Balamu adapita limodzi ndi Balaki, nakafika ku Kiriyati-Huzoti.
40Kumeneko Balaki adapereka nsembe ya ng'ombe ndi nkhosa, natumizako nyama kwa Balamu ndi kwa akalonga amene anali naye aja.
Mau oyamba auneneri a Balamu41M'maŵa mwake Balaki adatenga Balamu, napita naye ku mapiri a Bamoti-Baala, kumene Balamuyo ankatha kuwona mahema onse a Aisraele mpaka ku mathero ake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.