Owe. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za Tola.

1Atafa Abimeleki, padabwera winanso wodzapulumutsa Aisraele. Iyeyu anali Tola, mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo, wa fuko la Isakara. Ankakhala ku Samiri, m'dziko lamapiri la Efuremu.

2Adaweruza Aisraele zaka 23. Pambuyo pake adamwalira, naikidwa ku Samiri.

Za Yairo.

3Atafa Tola padabwera Yairo Mgiliyadi amene adaweruza Aisraele zaka 22.

4Iyeyu anali nawo ana makumi atatu amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Anawo anali nayonso mizinda makumi atatu imene mpaka pano ikutchedwa Havoti-Yairo m'dziko la Giliyadi.

5Pambuyo pake Yairo adamwalira, naikidwa ku Kamoni.

Aamoni asautsa Aisraele.

6Aisraele adachitanso zoipira Chauta potumikira Abaala ndi Aasitaroti, milungu ya ku Siriya, milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu, milungu ya Aamoni ndiponso milungu ya Afilisti. Aisraelewo adasiyadi Chauta osamamtumikiranso ai.

7Tsono Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, ndipo adalola kuti Afilisti ndi Aamoni aŵagonjetse.

8Chaka chimenecho anthuwo adagonjetseratu Aisraele nayamba kuŵasautsa. Pa zaka 18, adakhala akuŵasautsa Aisraele onse amene anali patsidya pa mtsinje wa Yordani m'dziko la Aamori, ku Giliyadi.

9Ndipo Aamoni adaoloka mtsinje wa Yordani kukamenyana nkhondo ndi fuko la Yuda, la Benjamini ndiponso la Efuremu, kotero kuti Aisraele adazunzika kwambiri.

10Tsono Aisraele adalira kwa Chauta nati, “Takuchimwirani popeza kuti tasiya Inu Mulungu wathu ndipo tatumikira Abaala.”

11Chauta adafunsa Aisraele kuti, “Kodi suja Ine ndidakupulumutsani kwa Aejipito, Aamori, Aamoni ndi Afilisti?

12Pamene Asidoni, Aamaleke ndi Amaoni, adaakusautsani, inu nkundilirira kuti ndikuthandizeni, suja Ine ndidakupulumutsani kwa anthu amene aja?

13Komabe Ine mwandisiya, mukutumikira milungu ina. Nchifukwa chake sindidzakupulumutsaninso.

14Pitani mukalirire milungu imene mwaisankhulayo. Ikupulumutseni milungu imeneyo pa nthaŵi ya kuzunzika kwanu.”

15Apo Aisraele adayankha Chauta kuti, “Ai, tachimwadi ife, tichiteni zimene zikukomereni. Tapota nanu, mungotipulumutsako lero lokha.”

16Choncho adachotsa milungu yachilendo pakati pao nayamba kutumikira Chauta, ndipo Chauta adamva chisoni poona Aisraele akuzunzika.

17Nthaŵi imeneyo Aamoni adasonkhana kuti adzamenye nkhondo, ndipo adakamanga zithando zankhondo ku Giliyadi. Aisraele nawonso adasonkhana nakamanga zithando zao ku Mizipa.

18Tsono anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi adayamba kufunsana kuti, “Kodi munthu woti ayambe kumenyana ndi Aamoniŵa ndani? Iyeyo ndiye amene akhale mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help