1 Eks. 32.11-14; Num. 14.13-19; 1Sam. 7.5-9 Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga akupempherera anthu ameneŵa, sindikadaŵamvera chisoni. Achotseni, ndisaŵaonenso, apite basi.
2Chiv. 13.10 Akakufunsa kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ Uŵauze kuti Ine ndati,
“ ‘Oyenera mliri adzafa ndi mliri,
oyenera lupanga adzafa ndi lupanga,
oyenera njala adzafa ndi njala,
oyenera ukapolo, adzapita ku ukapolo.’
3“Ndidzaŵagwetsera zinthu zinai izi zoŵaononga: lupanga loŵapha, agalu oŵaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zilombo zoti ziŵaphe ndi kuŵadya.
42Maf. 21.1-16; 2Mbi. 33.1-9Ndidzaŵasandutsa chinthu chochititsa nyansi kwa anthu a m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, adachita ku Yerusalemu.”
5Chauta akuti,
“Kodi inu a ku Yerusalemu adzakumverani chisoni ndani?
Adzakulirani ndani?
Ndani adzapatuke kuti akufunseni za moyo wanu?
6Ine mudandikana,
mukupitirirabe kundifulatira.
Motero ndidakweza mkono wanga nkukukanthani.
Ndidatopa nako kukhululuka.
7Ndidaŵabalalitsira uku ndi uku,
monga momwe amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero.
Ndidaŵaliritsa anthu anga ndi kuŵaononga,
chifukwa sadafune kusiya makhalidwe ao oipa.
8Akazi amasiye ndidaŵachulukitsa,
kupambana mchenga wakunyanja.
Amai ndidaŵaonongera ana ao
akali anyamata abiriŵiri.
Mwadzidzidzi ndidaŵagwetsera chisoni ndi nkhaŵa.
9Mai wa ana asanu ndi aŵiri wakomoka,
akupuma mwabefu.
Mdima wamgwera kukadali masana.
Adamchititsa manyazi ndipo wataya mtima.
Otsala onse ndidzaŵapereka kwa adani
kuti aŵaphe ndi lupanga,”
akuterotu Chauta.
Kulira kwa Yeremiya10Inu mai wanga, tsoka kwa ine kuti mudandibala ine munthu wokangana ndi wotsutsana ndi anthu pa dziko lonse. Sindidakongole kanthu kwa munthu kapena kukongoza munthu kanthu. Komabe anthu onse akunditukwana.
11Chauta adayankha kuti, “Koma zoonadi ndidzakulanditsa kuti upeze bwino. Ndithudi, adani ako adzakupemba pa nthaŵi ya tsoka ndi ya mavuto.
12Kodi munthu angathe kudula chitsulo, chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuŵa?
13“Anthu inu, chuma chanu chonse pamodzi ndi katundu wanu ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro, chifukwa cha machimo anu ambiri m'dziko lonse.
14Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu m'dziko limene simulidziŵa. Ndithudi, mkwiyo wanga wayaka, ndipo udzakutenthani kosalekeza.”
15Ine ndidati,
“Inu Chauta, mumadziŵa zonse.
Mundikumbukire ndipo mundithandize.
Mundilipsirire anthu ondizunza.
Mundilezere mtima, musandilande moyo.
Onani mavuto amene ndikupeza chifukwa cha Inu.
16Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino,
mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo.
Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse,
ndimadziŵika ndi dzina lanu.
17Sindidakhale nao m'gulu la anthu amadyera,
sindidasangalale nawo anthu amenewo.
Ndidakhala ndekha chifukwa choti
dzanja lanu linali pa ine,
ndipo mumtima mwanga mudadzaza mkwiyo.
18Nanga chifukwa chiyani mavuto anga sakutha?
Chilonda changa nchosatha, sichikupola.
Monga nkuti mwandinyenga ngati chitsime chouma
kapena ngati mtsinje wopanda madzi?”
19Chauta adayankha kuti,
“Ukabwerera kwa Ine,
ndidzakulandiranso,
ndipo udzanditumikiranso.
Ukamalankhula zenizeni, osati zachabe,
udzakhala wondilankhulira.
Anthu ameneŵa ayenera kudzabweranso kwa iwe,
koma iwe usabwerere kwa iwowo.
20Ndidzakusandutsa wolimba ngati linga
lamkuŵa kwa anthuwo.
Iwo adzalimbana nawe,
koma sadzakupambana,
pakuti Ine ndili nawe,
ndidzakulanditsa ndi kukupulumutsa.
21Ndidzakulanditsa kwa anthu oipa,
ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza,”
akuterotu Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.