1Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe,
inu maiko onse.
2Tumikirani Chauta mosangalala.
Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa.
3Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu.
Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake.
Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
4Loŵani pa zipata zake mukuthokoza,
pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda.
Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
5 1Mbi. 16.34; 2Mbi. 5.13; 7.3; Eza. 3.11; Mas. 106.1; 107.1; 118.1; 136.1; Yer. 33.11 Paja Iye ndi wabwino.
Chikondi chake nchamuyaya,
kukhulupirika kwake nkosatha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.