Miy. 26 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za munthu wopusa.

1Ulemu woulandira chitsiru

uli ngati chisanu chambee chomagwa nthaŵi yachilimwe,

kapena mvula yomagwa nthaŵi yokolola.

2Monga imachitira mpheta yokhalira kuuluka,

monga amachitira namzeze kumangoti zwezwezwe,

ndimonso limachitira temberero lopanda chifukwa,

silitha.

3Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo,

chitsulo ncha m'kamwa mwa bulu,

chonchonso ndodo ndi yoyenerera zitsiru.

4Chitsiru usamachiyankha potsata uchitsiru wake,

kuwopa kuti ungafanefane nacho.

5Koma mwina uzichiyankha chitsiru

potsata uchitsiru wake,

kuwopa kuti chingamadziyese chanzeru.

6Amene amatuma chitsiru kukanena uthenga,

amachita ngati kudzidula mapazi

ndipo amadziitanira mavuto.

7Monga miyendo ya munthu wopunduka

imakhala yopanda ntchito,

ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru.

8Amene amachitira chitsiru ulemu

ali ngati munthu wokulunga mwala m'khwenengwe.

9Monga imachitira minga yobaya dzanja la chidakwa

ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru.

10Amene amalemba ntchito chitsiru

chongodziyendera kapena chidakwa,

ali ngati munthu woponya mivi

amene amangolasa anthu chilaselase.

11 2Pet. 2.22 Chitsiru chimene chimabwerezabwereza za uchitsiru wake

chili ngati galu wodya masanzi ake omwe.

12Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi,

pali chikhulupiriro,

koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.

Za munthu waulesi ndi pakamwa pake pabodza

13Waulesi amati, “Pali mkango pa njira!

Mumseumo muli mkango!”

14Monga chitseko chimatembenukira uku ndi uku

pa zomangira zake,

ndimonso waulesi amangokunkhulira pabedi pake.

15Waulesi amati akapisa dzanja lake m'mbale,

kumamtopetsa kuti alifikitse kukamwa kwake.

16Waulesi amadziyesa wanzeru

kupambana anthu asanu ndi aŵiri

amene angathe kuyankha mochenjera.

17Amene angoloŵerera ndeu ya eniake,

ali ngati munthu wombwandira galu wongodziyendera.

18Monga munthu wopenga

amene amangoponya nsakali zamoto,

kapena mivi yoopsa,

19ndimonso amakhalira munthu wonyenga mnzake,

amene amati, “Ai, ndi zoseka chabe!”

20Moto umazima pakasoŵa nkhuni,

chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu.

21Monga momwe aliri makala pa moto wonyeka

ndiponso nkhuni pa moto woyaka,

ndimonso amakhalira munthu wandeu poutsa mikangano.

22Mau a kazitape ali ngati zakudya zokoma,

zimene zimatsikira m'mimba msanga.

23Monga m'mene chiziro chimakutira chiŵiya chadothi,

ndimonso mau oshashalika amabisira mtima woipa.

24Munthu wachidani pakamwa pake pamalankhula zabwino,

pamene mumtima mwake muli zonyenga.

25Woteroyo akamalankhula mokometsa mau, usamkhulupirire,

pakuti mumtima mwake mwadzaza zoipa.

26Ngakhale amabisa chidani mochenjera,

kuipa kwakeko kudzaoneka poyera pakati pa anthu.

27 Mphu. 27.25-27 Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha,

amene amakunkhuniza mwala, udzampsinja iye yemweyo.

28Munthu wonama amadana ndi amene iye adaŵapweteka,

pakamwa poshashalika mpoononga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help