1Ana inu, mverani malangizo a atate anu,
tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu.
2Ine ndikukupatsani malamulo abwino,
musasiye zimene ndikukuphunzitsani.
3Pamene ndinali mwana m'nyumba mwa atate anga,
m'menemo ndili kamwana kapamtima ka amai anga,
4atatewo adandiphunzitsa ndi mau akuti,
“Ugwiritse mumtima mwako zimene ndikukuuzazi,
usunge malamulo anga, kuti ukhale ndi moyo.
5Usaiŵale mau a pakamwa pangaŵa, usatayane nawo,
Ukhale ndi nzeru, ndiponso khalidwe la kumvetsa zinthu.
6Usaisiye nzeru, ndipo idzakusunga.
Uziikonda, ndipo idzakuteteza.
7Chachikulu pa nzeru ndi ichi:
Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo,
usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
8Uziilemekeza nzeruyo, ndipo idzakukweza.
Uifungate ndipo idzakupatsa ulemerero.
9Idzaika pamutu pako nsangamutu yokongola yamaluŵa.
Idzakuveka chisoti chaufumu chaulemu.”
10Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena.
Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka.
11Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru.
Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama.
12Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana.
Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai.
13Uŵasamale zedi,
pakuti moyo wako wagona pamenepo.
14Usayende m'njira za anthu oipa,
usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa.
15Njira zao uzipewe, usapitemo konse.
Uzilambalale, ndi kungozipitirira.
16Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa.
Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu.
17Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao,
kuchita ndeu ndiye chakumwa chao.
18Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu,
ili ngati kuŵala kwa mbandakucha,
kumene kumanka kukukulirakulira
mpaka dzuŵa litafika pamutu.
19Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani.
Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani.
20Mwana wanga, mvetsetsa mau anga.
Tchera khutu ku zimene ndikunena.
21Zisachoke m'mutu mwakomu,
uzisunge bwino mumtima mwako.
22Paja zimampatsa moyo amene wazipeza,
zimachiritsa thupi lake lonse.
23Mtima wako uziwulonda bwino,
pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo.
24Ulekeretu kulankhula zokhotakhota,
usiyiretu kukamba zopotoka.
25Maso ako aziyang'ana kutsogolo molunjika,
uzipenya kutsogolo osacheukacheuka.
26 Ahe. 12.13 Uzisamala m'mene mukupita mapazi ako,
ndipo njira zako zonse zidzakhala zosapeneketsa.
27Usapatukire kumanja kapena kumanzere,
usayende pamene pali choipa chilichonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.