1Usamavutika ndi anthu oipa.
Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa,
2pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu,
ndipo amafota ngati masamba aaŵisi.
3Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino.
Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika.
4Kondwa mwa Chauta,
ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.
5Udzipereke m'manja mwa Chauta,
umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.
6Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako,
ndipo kulungama kwako kudzaŵala ngati usana.
7Khala bata pamaso pa Chauta,
ndipo umdikire mosadandaula.
Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino,
ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
8Lewa kupsa mtima ndi kukwiya.
Usachite zimenezi, pakuti sudzapindula nazo kanthu.
9Pajatu anthu oipa adzaonongeka,
koma okhulupirira Chauta
adzalandira dziko kuti likhale lao.
10Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso,
ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri,
simudzampezapo.
11 Mt. 5.5 Koma anthu ofatsa adzalandira dziko
kuti likhale lao,
ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.
12Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino,
namamtuzulira maso mwachidani.
13Koma Chauta amamseka munthu woipayo,
poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera.
14Anthu oipa amasolola lupanga,
ndipo amakoka mauta,
kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa,
amene amayenda molungama.
15Koma lupanga lao lidzalasa mitima ya eniake omwewo,
ndipo mauta ao adzaŵathyokera m'manja.
16Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka,
kupambana kukhala nazo zokoma zambiri
zimene munthu woipa ali nazo.
17Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa,
koma adzalimbikitsa anthu onse abwino.
18Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro,
ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya.
19Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika,
pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.
20Koma anthu oipa amatha.
Adani a Chauta amafota ngati maluŵa,
amazimirira ngati utsi.
21Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza,
koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.
22Anthu amene Chauta adaŵadalitsa,
adzalandira dziko kuti likhale lao,
koma amene Chauta adaŵatemberera adzaonongeka.
23Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama,
amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
24Ngakhale agwe sadzapweteka,
popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.
25Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno,
sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu,
kapena ana ake akupempha chakudya.
26Nthaŵi zonse munthu wolungama amapatsa mosaumira,
ndipo amakongoza mwaufulu,
ana ake amakhala madalitso.
27Tsono leka zoipa, ndipo chita zabwino,
motero udzakhala pa mtendere mpaka muyaya.
28Chauta amakonda chilungamo,
sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika.
Iye adzawasunga mpaka muyaya,
koma adzaononga ana a anthu oipa.
29Anthu a Mulungu adzalandira dziko
kuti likhale lao,
ndipo adzakhala m'menemo mpaka muyaya.
30Munthu wabwino amalankhula zanzeru,
pakamwa pake pamatuluka zachilungamo.
31Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake,
motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno.
32Munthu woipa amazonda munthu wabwino,
amafunafuna kuti amuphe.
33Koma wolungamayo Chauta sadzamsiya yekha
m'manja mwa mdani wake,
sadzalola kuti pomuweruza, mlandu wake umuipire.
34Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake.
Motero adzakukweza
ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako.
Udzaona anthu oipa akuwonongeka.
35Ndidaona munthu woipa akunyada
ndi kudzitukumula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
36Koma pambuyo pake, podutsanso,
ndidaona kuti palibe.
Ngakhale ndidamfunafuna, sindidathe kumpeza.
37Upenye munthu wopanda cholakwa ndi wolungama,
ndipo udzapeza kuti munthu wamtendere
ali ndi zidzukulu zambiri.
38Koma anthu ochimwa adzaonongekeratu kwathunthu,
iwo pamodzi ndi zidzukulu zao zomwe.
39Chipulumutso cha anthu abwino
chimachokera kwa Chauta.
Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.
40Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa.
Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa,
popeza kuti anthuwo amadalira Iye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.