1 Yes. 25.10-12; Yer. 48.1-47; Ezek. 25.8-11; Amo. 2.1-3; Zef. 2.8-11 Nawu ulosi wonena za Mowabu:
Chifukwa chakuti mzinda wa Ari
waonongedwa usiku umodzi wokha,
dziko la Mowabu lagwa.
Chifukwa chakuti mzinda wa Kiri
waonongedwa usiku umodzi wokha,
dziko la Mowabu lagwa.
2Anthu a ku Diboni akukwera
ku nyumba ya milungu yao,
akukwera ku akachisi ao kukalira.
Anthu a ku Mowabu akulira mzinda
wa Nebo ndi wa Medeba.
Mutu uliwonse wametedwa mpala,
ndevu zonse zametedwa.
3M'miseu akuvala ziguduli,
pamadenga ndi m'mabwalo
aliyense akulira kwamphamvu,
misozi ili pupupu.
4Anthu a ku Hesiboni ndi ku Eleale
akulira mofuula.
Mau ao akumveka mpaka ku Yahazi.
Nchifukwa chake asilikali a ku Mowabu akulira mofuula,
ataya mtima.
5Inenso ndikulira Mowabu.
Anthu ake othaŵa nkhondo akuthaŵira
ku Zowari, ku Egilati-Selisiya.
Akupita nalira ku chikweza cha Luhiti,
akulira mosweka mtima pa mseu wopita ku Horonaimu.
6Ku mtsinje wa Nimurimu madzi adaphwa,
udzu udauma, msipu udafota,
palibenso chomera chobiriŵira.
7Nchifukwa chake anthu akuthaŵa
atanyamula chuma chao.
Afuna kuwoloka nacho Chigwembe cha Misondodzi.
8Kulira kwao kukumveka ku dziko lonse la Mowabu,
kukumveka kuchokera kumpoto ku Egilaimu
mpaka kumwera ku Beerelimu.
9Madzi a ku Diboni asakanizika ndi magazi,
komabe ndidzafikitsa zovuta zina zambiri pa Diboni.
Ndidzafikitsa mkango woti udzagwire
aliyense wopulumuka ku Mowabu,
ndiponso aliyense wotsalira m'dzikomo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.