1Masiku amenewo, pamene ku Israele kunalibe mfumu, munthu wina wachilevi ankakhala kutali ku dziko lamapiri la ku Efuremu. Iyeyo adakwatira mzikazi wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda.
2Tsiku lina mzikazi wake uja adamkwiyira mwamunayo ndipo adathaŵa napita kwa bambo wake ku Betelehemu m'dziko la Yuda. Adakhala kumeneko miyezi inai.
3Tsono mwamuna wake adanyamuka namtsatira kuti akakambe naye mofatsa, kumpempha kuti abwerere. Mwamunayo anali ndi mtumiki wake ndi abulu ake aŵiri. Ndipo adafika ku nyumba ya bambo wake wa mkaziyo. Tsono mkaziyo adamloŵetsa m'nyumba ndipo bambo wake adamlandira ndi manja aŵiri.
4Mpongozi wakeyo, bambo wake wa mkazi uja, adamuuza kuti aswere, choncho adakhalako masiku atatu. Ankadya, namamwa ndi kumagona kumeneko.
5Tsiku lachinai lake iwo adadzuka m'mamaŵa, iye nkukonzeka kuti azipita. Koma bambo wake wa mkaziyo adauza mkamwini wake uja kuti, “Yambani mwadya chakudya, pambuyo pake mutha kupita.”
6Choncho anthu aŵiriwo adakhala pansi, nadya ndi kumwa limodzi. Bambo wa mkaziyo adauza mwamunayo kuti, “Gonaninso konkuno lero, musangalale.”
7Pamene munthuyo adanyamuka kuti azipita, mpongozi wake adamkakamiza kuti agonenso komweko.
8Tsiku lachisanu lake adadzuka m'mamaŵa kuti azipita. Bambo wake wa mkaziyo adamuuza kuti, “Yambani mwadya chakudya ndipo mudikire mpaka madzulo.” Choncho aŵiri onsewo adadyera limodzi.
9Pamene munthuyo ndi mzikazi wake ndiponso mtumiki wake adanyamuka kuti azipita, bambo wake wa mkaziyo adaŵauza kuti, “Onani, dzuŵa ndiye lapita, ndipo ano ndi madzulo. Gonaninso konkuno lero ndapota nanu. Onani kulikuda. Gonani konkuno, musangalale. Maŵa mudzuka m'mamaŵa nkumapita kwanu.”
10Koma munthu uja sadafune kugonanso tsiku limenelo. Mwakuti adanyamuka nkumapita, nakafika ku malo oyang'anana ndi Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu). Iyeyo anali atatenga abulu aŵiri okhala ndi zishalo zake, ndipo mzikazi wake uja anali naye limodzi.
11Pamene ankayandikira ku Yebusi, nkuti kuli madzulo ndithu, ndipo mtumiki uja adauza mbuyake kuti, “Bwanji tsopano tingopatuka, kuloŵa mu mzinda wa Ayebusiwu ndi kukagona momwemo?”
12Mbuyake adayankha kuti, “Sitipatuka kuloŵa mu mzinda wa alendo amene sali Aisraele. Koma tipitirira mpaka ku Gibea.”
13Motero adauza mtumiki wakeyo kuti, “Tiye tikafike pafupi ndi malo ndatchulawo, ndipo tikagone ku Gibea kapena ku Rama.”
14Choncho adapitirira nayenda ulendo wao, ndipo dzuŵa lidaŵaloŵera atafika pafupi ndi Gibea, mzinda wa fuko la Benjamini.
15Adapatukira kumeneko kuti akaloŵe mu mzinda wa Gibea, ndi kugona komweko usiku umenewo. Adakaloŵa mumzindamo nakakhala pansi pa bwalo, pakuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adaŵalandira kunyumba kwake, kuti apeze pogona.
16Kenaka adangoona munthu wina wokalamba akuchokera ku ntchito kumunda kwake madzulo. Anali wa ku dziko lamapiri la ku Efuremu, koma ankakhala nao ku Gibea. (Eni ake malowo anali Abenjamini).
17Munthu wokalamba uja atakweza maso adaona wapaulendo uja atakhala pa bwalo la mumzindamo, namufunsa kuti, “Kodi ulendowu, mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?”
18Mlendoyo adayankha kuti, “Tikupita kutali ku dziko lamapiri la ku Efuremu kumene ndimakhala, ndipo tikuchokera ku Betelehemu ku dziko la Yuda. Ndidaapita ku Betelehemu ndipo tsopano ndikupita kwathu, koma palibe ndi mmodzi yemwe wondilandira m'nyumba mwake.
19Tili nawo udzu ndi chakudya cha abulu athu. Ndili nayenso buledi ndi vinyo wondikwanira ine, mdzakazi wangayu, ndi mtumiki amene ali ndi ifeyu. Palibe chimene tikusoŵa.”
20Apo munthu wokalambayo adati, “Mtendere ukhale nanu. Ndikuthandizani pa zosoŵa zanu zonse, koma tsono musagone pa bwalo usiku uno.”
21Choncho adapita nawo kunyumba kwake, naŵapatsa chakudya abulu aja. Ndipo alendowo adasamba mapazi ao, nalandira chakudya ndi chakumwa.
22 Gen. 19.5-8 Pamene anali kudya mosangalala, adangoona anthu amumzindamo, anthu achabechabe, ataizinga nyumbayo, namamenya chitseko. Adauza munthu wokalamba uja, mwini wake wa nyumbayo, kuti, “Mtulutse munthu uja wabwera m'nyumba mwakoyu, tiseŵere naye.”
23Mwini wake wa nyumba uja adatuluka nakaŵauza kuti, “Iyai, abale anga, musachite zoipa zotere. Munthuyu wabwera m'nyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere.
24Onani pano pali mwana wanga wanamwali wosamdziŵa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsireni ameneŵa tsopano lino, muŵatenge ndipo muchite nawo zimene mufuna. Koma musachite chinthu chonyansa ndi mlendoyu.”
25Koma anthuwo sadafune kumumvera. Choncho mlendo uja adagwira mzikazi wake uja namtulutsira kunali iwoko, iwowo nkugona naye, nachita naye zoipa usiku wonse mpaka m'maŵa. M'bandakucha adamlola kuti apite.
26Ndipo m'maŵa kulikucha, mkaziyo adabwera nagwa pansi pakhomo pa nyumba ya munthu uja m'mene munali mwamuna wake muja. Adakhala pamenepo ali thasa mpaka kudayera.
27Mwamuna wakeyo adadzuka m'maŵa, ndipo atatsekula zitseko za nyumba kuti azipita, anangoona mzikazi wake uja ali thasa pakhomo pa nyumba, manja ake ali pa chiwundo.
28Adamuuza kuti, “Dzuka tizipita.” Koma mkaziyo sadayankhe kanthu. Tsono adamkweza pabulu, ndipo mlendoyo adanyamuka kupita kwao.
291Sam. 11.7 Ataloŵa m'nyumba mwake, adatenga mpeni, naduladula thupi la mkaziyo m'nthuli khumi ndi ziŵiri. Ndipo adazitumiza m'dziko lonse la Israele.
30Onse amene adaona zimenezi ankati, “Zoterezi sizinachitikepo kuyambira nthaŵi imene Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mpaka lero lino. Tiziganize bwino ndipo tipangane ndi kuchitapo kanthu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.