1 1Mbi. 16.34; 2Mbi. 5.13; 7.3; Eza. 3.11; Mas. 100.5; 106.1; 107.1; 118.1; Yer. 33.11 hokozani Chauta chifukwa ngwabwino,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
2Thokozani Mulungu wa milungu,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
3Thokozani Chauta woposa ambuye onse,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
4Chauta yekhayo amachita zodabwitsa zazikulu,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
5 Gen. 1.1 Adalenga zakumwamba ndi nzeru zake,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
6 Gen. 1.2 Adayala dziko lapansi pa madzi,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
7 Gen. 1.16 Adalenga miyuni yaikulu yamumlengalenga,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
8Dzuŵa kuti lizilamulira usana,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
9Mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira usiku,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
10 Eks. 12.29 Adapha ana achisamba a ku Ejipito,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
11 Eks. 12.51 Ndipo adatulutsa Aisraele pakati pao,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
12Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambalitsa,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
13 Eks. 14.21-29 Adagaŵa pakati Nyanja Yofiira,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
14Adaolotsa Aisraele pakati pake,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
15Koma adamiza Farao ndi ankhondo ake m'Nyanja Yofiira,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
16Adatsogolera anthu ake m'chipululu,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
17Adapha mafumu amphamvu,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
18Adaphanso mafumu otchuka,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
19 Num. 21.21-30 Adapha Sihoni, mfumu ya Aamori,
pakuti chikondi chake nchamuyaya,
20 Num. 21.31-35 Adapha Ogi, mfumu ya ku Basani,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
21Napereka dziko la mafumuwo kuti likhale choloŵa,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
22Choloŵa cha Israele mtumiki wake,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
23Adatikumbukira pamene adani adatigonjetsa,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
24Ndipo adatipulumutsa kwa adani athu,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
25Amapatsa zamoyo zonse chakudya,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
26Thokozani Mulungu wakumwamba,
pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.