1Ndikuitana Inu Chauta, Inu thanthwe langa,
musachite ngati simukundimva,
chifukwa ngati mukhala chete,
ndidzafanafana ndi anthu otsikira ku manda.
2Imvani kupempha kwanga,
pamene ndikulirira Inu kuti mundithandize,
pamene ndikukupembedzani pokweza manja anga
ku malo anu opatulika kopambana.
3Musandichotsere kumodzi ndi anthu oipa,
anthu amene amachita zonyenga,
amene amalankhula zamtendere ndi anzao,
koma mitima yao ndi yodzaza ndi chidani.
4 Chiv. 22.12 Muŵabwezere anthu otere molingana ndi ntchito zao,
muŵalange molingana ndi zoipa zimene ankachita.
Muŵabwezere molingana ndi ntchito zao,
Muŵalange molingana ndi kuipa kwa ntchito zao.
5Chifukwa chakuti iwo sasamalako ntchito za Chauta,
ngakhale zimene adalenga Iye.
Chauta adzaŵagumula ngati nyumba, osaŵamanganso.
6Chauta atamandike,
pakuti wamva liwu la kupempha kwanga.
7Chauta ndiye mphamvu zanga,
ndiyenso chishango changa chonditeteza.
Ndaika mtima wanga wonse pa Iye.
Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala,
ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
8Chauta ndiye mphamvu zimene anthu ake amadalira,
ndiye kothaŵira komwe wodzozedwa wake amapulumukirako.
9Pulumutsani anthu anu, Inu Chauta,
mudalitse amene mudaŵasankha.
Mukhale mbusa wao,
muŵasamale mpaka muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.