1Davide adasonkhanitsanso ankhondo okwanira 30,000, amene adaŵasankha pakati pa Aisraele.
2
9Davide adachita mantha ndi Chauta tsiku limenelo, ndipo adafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Chautali lingafike bwanji kwathu?”
10Motero Davide sadafunenso kuti abwere nalo Bokosi la Chautalo kwao ku mzinda wake wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti.
111Mbi. 26.4, 5Choncho Bokosi lachipanganolo lidakhala miyezi itatu m'nyumba ya Obededomu wa ku Gati. Ndipo Chauta adadalitsa Obededomu ndi banja lake lonse.
12Tsono Davide adamva kuti Chauta wadalitsa banja la Obededomu ndi zinthu zonse zimene anali nazo, chifukwa cha Bokosi lachipangano. Choncho iye adapita kukatenga Bokosi lachipanganolo, kulichotsa m'nyumba ya Obededomu, napita nalo ku mzinda wake, akukondwera.
13Ndipo anthu amene ankanyamula Bokosi lachipanganolo ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, Davide ankapereka nsembe ya ng'ombe yamphongo ndi mwanawang'ombe wonenepa.
14Davide atavala efodi yabafuta ankavina molemekeza Chauta ndi mphamvu zake zonse.
15Choncho iye pamodzi ndi Aisraele onse adabwera ndi Bokosi lachipangano akufuula ndi kuliza mbetete.
16Pamene Bokosi lachipangano linkaloŵa mu mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina molemekeza Chauta. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake.
17Anthu adaloŵa nalo Bokosi lachipangano lija, nakalikhazika pamalo pake m'kati mwa hema limene Davide adaamangira Bokosilo. Tsono Davide adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Chauta.
18Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjanozo, adadalitsa anthu m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse.
191Mbi. 16.43Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli yanyama, ndiponso keke ya mphesa zouma. Tsono anthu onse adachokapo, napita aliyense kunyumba kwake.
20Pamene Davide adabwerera kuti akadalitse banja lake, Mikala, mwana wa Saulo, adadzamchingamira nati, “Nkutero mfumu ya Aisraele kudzilemekeza kwake lero! Mpaka kuchita kudzivula pamaso pa adzakazi a antchito ake, monga m'mene amachitira munthu wamisala, opanda ndi manyazi omwe!”
21Davide adamuyankha kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Chauta, amene adandisankhula ine kupambana bambo wako, ndiponso kupambana banja lonse la bambo wako. Ndipo adandiika kuti ndikhale mfumu ya Aisraele, anthu a Chauta. Choncho ndidzasangalalabe ndi kulemekeza Chauta.
22Ndidzadzinyoza ndithu kupambana pamenepa. Kapena ndidzakhala wonyozeka m'maso mwako, koma m'maso mwa adzakazi amene ukunenawo, ndidzakhala wolemekezeka.”
23Tsono Mikala, mwana wa Saulo, adaferamo osamuwona mwana.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.