1Inu Chauta, imvani pemphero langa,
kulira kwanga kufike kwa Inu.
2Musandibisire nkhope yanu pa tsiku la mavuto anga.
Tcherani khutu kuti mundimve,
mundiyankhe msanga pa tsiku limene ndikukuitanani.
3Masiku anga amangopita ngati utsi,
ndipo thupi langa likuyaka ngati ng'anjo.
4Mtima wanga wakanthidwa,
ndipo wafota ngati udzu,
zoonadi, ngakhale chakudya chimandinyansa.
5Ndaonderatu ngati munthu wachitopa,
ntchito yanga ndi kubuula nthaŵi zonse.
6Ndili ngati mbalame yakuchipululu,
ngati kadzidzi wam'mabwinja.
7Ndimagona osapeza tulo,
ndili ngati mbalame yokhala yokha pa denga,
8Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe,
onse ondinyoza amatchula dzina langa potemberera.
9Inetu ndimadya phulusa ngati chakudya,
chakumwa changa ndimasakaniza ndi misozi,
10chifukwa cha ukali wanu ndi mkwiyo wanu,
popeza kuti Inu mwandinyamula ndi kunditaya.
11Masiku anga ali pafupi kutha ngati mthunzi wamadzulo.
Ndikufota ngati udzu.
12Koma Inu Chauta,
mumakhala pa mpando wanu waufumu mpaka muyaya.
Anthu a mibadwo yonse adzakukumbukirani.
13Mudzadzuka nkuchitira chifundo mzinda wa Ziyoni,
zoonadi, nthaŵi yake youkomera mtima yafika.
14Mzindawo amaukondabetu anthu anu,
ngakhale waonongeka ndi kusanduka bwinja.
15Mitundu ya anthu idzalemekeza Chauta moopa,
mafumu onse a pa dziko lapansi adzaopa ulemerero wake.
16Chauta adzamanganso Ziyoni,
ndipo adzaonekera mu ulemerero wake.
17Adzayankha pemphero la anthu ake otayika,
sadzanyoza kupemba kwao.
18Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mbadwo wakutsogolo,
kuti anthu amene mpaka tsopano lino sanabadwebe,
nawonso adzatamande Chauta,
19Iye adayang'ana pansi ali m'malo ake oyera kumwamba,
ali kumwambako, Chauta adayang'ana pa dziko lapansi,
20kuti amve kubuula kwa anthu am'ndende,
kuti aŵapulumutse amene adaayenera kuphedwa.
21Motero anthu adzalalika dzina la Chauta ku Ziyoni,
ndipo adzamtamanda ku Yerusalemu,
22pamene mitundu ya anthu ndi mafumu adzasonkhana
kuti apembedze Chauta.
23Chauta wathyola mphamvu zanga ndisanakule,
wafupikitsa masiku anga.
24Ndikuti,
“Mulungu wanga, musandichotse tsopano ndisanakalambe,
Inu amene zaka zanu sizitha mpaka muyaya.”
25 Ahe. 1.10-12 Inu mudaika maziko a dziko lapansi kalekale,
ndipo zakumwamba mudazipanga ndi manja anu.
26Zonsezi zidzatha ngati malaya,
koma Inu mulipobe.
Inu mumazisintha ngati chovala, ndipo zimatha.
27Koma Inu simusintha,
zaka zanu sizitha.
28Ana a ife atumiki anu adzakhala opanda nkhaŵa,
zidzukulu zathu zidzakhazikika pamaso panu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.