Eks. 36 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1“Ndipo Bezalele, Oholiyabu, pamodzi ndi aluso onse amene Chauta adaŵapatsa luso ndi nzeru zodziŵira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Chauta adalamulira.”

Anthu abwera ndi zopereka zochuluka

2Pamenepo Mose adaitana Bezalele, Oholiyabu ndi onse aluso amene Chauta adaŵapatsa nzeru, ndiponso onse amene anali okonzeka kuthandiza.

3Ndipo Mose adaŵapatsa zopereka zonse zaufulu zomangira malo opatulika zimene Aisraele adabwera nazo. Koma Aisraelewo ankapatsabe Mose zopereka zao m'maŵa mulimonse.

4Tsono aluso onse amene ankagwira ntchito zomanga malo opatulika aja, aliyense potsata luso lake, adasiya ntchito zao,

5nadzauza Mose kuti, “Anthu akubwera ndi zipangizo za ntchitoyi zochuluka, kuposa m'mene zidzafunikire pogwira ntchito imene Chauta adalamula kuti ichitike.”

6Motero Mose adalamula anthu m'mahema monse kuti, “Mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense asaperekenso zopereka zomangira malo opatulika.” Motero anthu adaleka kubwera ndi zopereka.

7Zimene anali atazisonkhanitsa zidachuluka kuposa zimene zinkafunika kuti amalize ntchitoyo.

Za mapangidwe a chihema cha Chauta(Eks. 26.1-37)

8Tsono amuna onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo, adapanga chihema cha Chauta ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Pa nsalu zonsezo adapetapo zithunzi za akerubi.

9M'litali mwa nsalu iliyonse munali mamita 13, ndipo muufupi mwake munali masentimita 183. Zonsezo zinali zofanana.

10Ndipo adasokerera nsalu zisanu, kuti zikhale chinsalu chimodzi, zisanu zinazonso adazisokerera nkukhalanso chinsalu chimodzi.

11Pambuyo pake adasoka magonga a tinsalu tobiriŵira m'mphepete mwa chimodzi kubwalo kwake, ndipo adachitanso chimodzimodzi ndi chinacho.

12Adasoka magonga makumi asanu pa chinsalu choyambacho, ndi magonga ena makumi asanu pa chinsalu chinacho, mopenyana ndi magonga a chinsalu choyamba aja.

13Kenaka adapanga ngoŵe zokoŵera zagolide makumi asanu, nalumikiza nsalu zazikulu ziŵirizo ndi ngoŵezo. Pamenepo chihema cha Chauta chidakhala chimodzi.

14Pambuyo pake adasoka nsalu khumi ndi imodzi za ubweya wambuzi, napanga chophimbira pamwamba pa chihemacho.

15M'litali mwa nsalu iliyonse munali mamita 14, ndipo muufupi mwake munali masentimita 183. Zonsezo zinali zofanana.

16Tsono adasokerera nsalu zisanu nkukhala chinsalu chimodzi, ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, adazisokereranso kuti zikhale chinsalu chimodzi.

17Adasokanso magonga makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu yomalizira ya chinsalu choyambacho, ndi magonga ena makumi asanu m'mphepete mwa chinsalu chinacho.

18Kenaka adapanga ngoŵe zokoŵera zokwanira makumi asanu zamkuŵa zolumikizira pamodzi nsalu ziŵirizo, kuti apange chinsalu chimodzi chophimbira chihema.

19Ndipo adapanga chophimbira china chofiira cha zikopa za nkhosa zamphongo. Potsiriza adapanganso chophimbira china cha zikopa zofeŵa, nkuchiika pamwamba pa zophimba zina zonse.

20Pambuyo pake adapanga mafulemu a chihemacho ndi matabwa a mtengo wa kasiya.

21M'litali mwa fulemu lililonse munali mamita anai ndi theka, ndipo muufupi mwake munali masentimita 69.

22Thabwa lililonse linali ndi zolumikizira ziŵiri, ndipo mafulemu onse adaŵapanga ndi zolumikizira ziŵiri. Mafulemu onse adaŵapanga ndi zolumikizira zotere.

23Pa mbali yakumwera adapanga mafulemu makumi aŵiri,

24ndi masinde makumi anai chapansi pake. Pa fulemu lililonse adapanga masinde aŵiri asiliva, ogwirana ndi zolumikizira ziŵiri zija.

25Pa mbali yakumpoto ya chihemacho adapanganso mafulemu makumi aŵiri

26ndi masinde ake makumi anai asiliva, masinde aŵiri pansi pa fulemu lililonse.

27Adapanganso mafulemu asanu ndi limodzi kumbuyo kwake kwa chihemacho chakuzambwe,

28ndiponso mafulemu aŵiri am'ngodya, kumbuyo kwake kwa chihemacho.

29Mafulemu aŵiri am'ngodyawo anali olumikizika pansi pake ndi ogwirizana mpaka pamwamba ku ngoŵe yokoŵera yoyamba ija. Ndimo m'mene mafulemu aŵiri opanga ngodya ziŵiri aja adapangidwira.

30Motero panali mafulemu asanu ndi atatu, ndi masinde asiliva 16, aŵiri pansi pa fulemu lililonse.

31Kenaka adapanga mitanda ya matabwa a mtengo wa kasiya, isanu ya mafulemu a mbali imodzi ya chihema,

32isanu ya mafulemu a mbali inayo, ndiponso isanu ya mafulemu a mbali yakuzambwe, kumbuyo kwake kwa chihema.

33Tsono adapanga mtanda wapakati chapakatimpakati, wogwira mafulemuwo kuyambira ku mbali imodzi ya chihema mpaka mbali ina.

34Mafulemu onsewo adaŵakuta ndi golide, ndipo adamangapo mphete zagolide zopisiramo mitanda ija, imene adaikutanso ndi golide.

35Pambuyo pake adapanga nsalu yochingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndipo adapetapo zithunzi za akerubi.

36Adapanga nsanamira zinai zakasiya zogwirizira nsalu yochingira ija. Nsanamirazo zinali zitakutidwa ndi golide, ndipo adaika ngoŵe zokoŵera ku nsanamirazo. Adapanga masinde anai asiliva ogwirizira nsanamirazo.

37Pa chipata choloŵera m'chihemamo, adaikapo nsalu yochinga yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso.

38Tsono adapanga nsanamira zisanu zokhala ndi ngoŵe zokoŵera nsaluyo, ndipo mitu yake ndi mitanda yake adaikuta ndi golide, koma masinde ake anali amkuŵa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help