1Chauta akunena kuti,
“Pa nthaŵi imeneyo ndidzakhala Mulungu
wa mabanja onse a Israele,
ndipo iwo adzakhala anthu anga.”
2Mau a Chauta ndi aŵa,
“Anthu amene adapulumuka ku nkhondo,
ndidaŵakomera mtima m'chipululu.
Pamene Aisraele ankafuna kupumula,
3Ine ndidaŵaonekera ndili chakutali.
Inu Aisraele ndakukondani kwambiri ndi
chikondi chopanda malire,
ndakhala wokhulupirika kwa inu mpaka tsopano.
4Ndidzakusamaliraninso inu anthu a ku Israele,
motero mudzapezanso bwino.
Mudzakondwanso poimba ting'oma tolira,
ndipo mudzapita nawo limodzi anthu ovina mwachimwemwe.
5Mudzalimanso minda yamphesa pa mapiri a Samariya.
Alimi adzabzala mphesa ndipo adzadya zipatso zake.
6Lidzafika tsiku pamene alonda a pa mapiri
a Efuremu adzafuula kuti,
‘Tiyeni, tipite ku Ziyoni kwa Chauta, Mulungu wathu!’ ”
7Chauta akuti,
“Imbani mokweza ndi mosangalala chifukwa cha Yakobe.
Fuulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse.
Lalikani, tamandani ndi kulengeza kuti,
‘Chauta wapulumutsa anthu ake,
wasunga otsala a Israele.’
8Ndidzaŵatulutsa kuchokera ku dziko lakumpoto.
Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku malekezero
a dziko lapansi.
Ndidzasonkhanitsa akhungu ndi opunduka,
akazi amene ali ndi pakati ndi amene ali pa
nthaŵi yao yochira.
Chidzakhala chinamtindi cha anthu obwerera kuno.
9Adzabwerera kwao akulira,
koma Ine ndidzaŵaperekeza ndi mtima wachifundo.
Ndidzaŵatsogolera ku mitsinje yodzaza ndi madzi.
Sadzaphunthwa, njira yao idzakhala yosalala kwambiri.
Ine ndine bambo wake wa Israele,
Efuremu ndi mwana wanga wachisamba.
10“Mverani mau a Chauta,
inu anthu a mitundu yonse.
Mulalike mauwo ku maiko akutali
a m'mbali mwa nyanja.
Mulungu amene adabalalitsa Aisraele
adzaŵasonkhanitsanso.
Adzaŵasamala monga momwe mbusa amasamalira nkhosa zake.
11Ndithu, Chauta waombola fuko la Yakobe.
Adaŵapulumutsa m'mavuto amene sakadatha kutulukamo.
12Anthuwo adzabwera akuimba mofuula pa mapiri a Ziyoni,
adzakhala osangalala kwambiri
chifukwa cha zabwino zochuluka zochokera kwa Chauta.
Zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano,
mafuta, anaankhosa ndi anaang'ombe.
Moyo wao udzakhala ngati munda wothirira,
ndipo sadzamvanso chisoni.
13Anamwali adzavina mokondwa,
achinyamata ndi okalamba omwe adzasangalala.
Kulira kwao kuja ndidzakusandutsa chimwemwe.
Ndidzaŵasangalatsa, ndidzaŵakondwetsa,
nkuchotsa chisoni chao.
14Ansembe ndidzaŵadyetsa chakudya chabwino,
ndipo anthu anga adzakhuta zabwino za chifundo changa,”
akuterotu Chauta.
Chauta achitira Aisraele chifundo15 Gen. 35.16-19; Mt. 2.18 Mau a Chauta ndi aŵa:
“Imvani, kulira kukumveka ku Rama,
kulira komvetsa chisoni.
Rakele akulira ana ake.
Sakutonthozeka,
chifukwa choti ana ake asoŵa.”
16Chauta akunena kuti,
“Tonthola, usadzenso misozi.
Ndithu udzalandira mphotho ya ntchito zako,
akutero Chauta.
Ndipo anthu adzabwerako ku dziko la adani.
17Tsono chikhulupiriro chilipo pa zakutsogolo,
zidzukulu zanu zidzabweranso kudziko kuno,”
akutero Chauta.
18“Ndamva Aefuremu akulira mwachisoni kuti,
‘Inu mwatilanga
ngati mwanawang'ombe wosaphunzitsidwa,
ndipo taphunziradi kumvera.
Mutibweze kuti tithe kubwerera,
Pakuti inu ndinu Chauta, Mulungu wathu.
19Tsopano poti tatembenuka mtima, tikumva chisoni.
Tsopano poti taphunzira,
tikudzigunda pa mtima.
Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa,
chifukwa cha machimo athu apaubwana.’
20Kodi suja Efuremu ndi mwana wanga wapamtima,
mwana amene ndimakondwera naye kwambiri?
Nthaŵi zonse ndikamamdzudzula,
ndimamkumbukirabe ndi chikondi,
mwakuti mtima wanga umamlakalaka.
Ndimamumvera chifundo chozama zedi,”
akuterotu Chauta.
21“Mudziikire zizindikiro,
mudziikire zikwangwani.
Muuyang'anitsitse mseuwo,
mseu umene mudaadzera popita.
Bwerera namwaliwe Israele,
bwerera ku mizinda yako ija.
22Kodi udzakhala ukutepeka mpaka liti,
iwe mwana wanga wosakhulupirika?
Zoona, Chauta walenga chinthu chatsopano
pa dziko lapansi:
mkazi ndiye atsogola kufunafuna mwamuna.”
23Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Pamene ndidzabwezeranso anthu ufulu, kudzamvekanso mau ku dziko la Yuda ndi ku mizinda yake. Mau ake adzakhala akuti, ‘Chauta akudalitse iwe malo achilungamo, ndiponso iwe phiri loyera.’
24Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake, pamodzi ndi alimi ndi oŵeta nkhosa.
25Ndidzatsitsimutsa anthu ofooka, ndipo anthu anjala ndidzaŵadyetsa chakudya nadzakhuta.”
26Pamenepo ndidadzuka nkudzati maso mwalamwala, ndipo ndidaona kuti ai ndidaatipha tulo.
27Chauta akunena kuti, “Ikubwera nthaŵi pamene ndidzachulukitsa anthu ndi ziŵeto mu Israele ndi Yuda.
28Monga momwe ndidaŵasamalira, kuŵazula, kuŵapasula, kuŵagumula, kuŵaononga ndi kuŵachita zoipa, momwemonso ndidzasamala kuti ndiŵamange ndi kuŵabzalanso,” akuterotu Chauta.
29Ezek. 18.2 “Masiku amenewo anthu sadzanenanso kuti, ‘Makolo adya mphesa zosapsa, koma ana ndiye achita dziru.’
30Koma munthu aliyense adzafa chifukwa cha machimo ake. Aliyense wodya mphesa zosapsa, ndi iye yemweyo amene adzachite dziru.”
Za chipangano chatsopano31 Mt. 26.28; Mk. 14.24; Lk. 22.20; 1Ako. 11.25; 2Ako. 3.6 Ahe. 8.8-12 Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzachite chipangano chatsopano ndi anthu a ku Israele ndi a ku Yuda.
32Sichidzakhalanso ngati chipangano chija chimene ndidaachita ndi makolo ao, pamene ndidaŵagwira padzanja nkuŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Chipangano chimenecho iwo adaphwanya, ngakhale ndinali Mbuye wao.
33Ahe. 10.16 Koma chipangano chimene ndidzachite ndi anthu a ku Israele atatha masiku amenewo, ndi ichi: Ndidzaika malamulo anga mwa iwo, ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Tsono Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga.
34Ahe. 10.17 Nthaŵi imeneyo wina sazidzachitanso kuphunzitsa mnzake kapena mbale wake kuti adziŵe Chauta. Pakuti onsewo, ana ndi akulu omwe adzandidziŵa, Ndidzaŵakhululukira machimo ao, sindidzakumbukiranso machimo aowo,” akuterotu Chauta.
35Chauta akunenanso kuti,
“Iye amene amaŵalitsa dzuŵa masana,
amene amaŵalitsa mwezi ndi nyenyezi usiku,
amene amavundula nyanja
kuti mafunde ake achite mkokomo,
ndiye amene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
36Ngati zochitika zimenezi zilekeka,
Ine ndili pomwepo,
pamenepo ndiye fuko la Israele lidzathe,
ndipo silidzakhalanso mtundu wa anthu
pamaso panga mpaka muyaya.
37Atangopezeka munthu wotha kupima zakumwamba
nkufufuza maziko a dziko lapansi,
pamenepo Inenso ndidzalitaya fuko lonse la Israele,
chifukwa cha zoipa zimene iwo adachita,”
akuterotu Chauta.
38Chauta akuti, “Ikubwera nthaŵi pamene mzinda uja wa Chauta udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananele mpaka ku Chipata cha Ngodya.
39Kuyambira pamenepo malire ake adzapitirira mpaka ku phiri la Garebe, nkudzakhota kuloza ku Gowa.
40Chigwa chonse m'mene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku mtsinje wa Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Kavalo chakuvuma, zonsezo zidzakhala zopatulikira Chauta. Mpakampaka mzinda wa Yerusalemu sudzaonongedwanso kapena kugwetsedwa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.