1 Yer. 3.6 Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene adadaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 31 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.
2Iyeyo adachita zolungama pamaso pa Chauta, namatsata chitsanzo cha Davide kholo lake pa zonse, osapatukira kumanja kapena kumanzere.
3Chaka cha 18 cha ufumu wake, Yosiya adatuma Safani mwana wa Azaliya, mwana wa Mesulamu, mlembi wa ku Nyumba ya Chauta, nati,
4“Pita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe, ukamuuze kuti aŵerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Chauta, zimene alonda apakhomo adasonkhanitsa kwa anthu.
5Ndalama zimenezo azipereke kwa akapitao okonzetsa Nyumba ya Chauta aja. Iwowo azipereke kwa antchito aja okonza Nyumba ya Chauta.
6Ndiye kuti alipire amisiri a matabwa, amisiri omanga nyumba, amisiri omanga ndi miyala ndiponso amene adapereka mitengo ndi miyala yosema yokonzera Nyumbayo.
72Maf. 12.15Koma anthu amene apatsidwe ndalama zolipirira antchito okonza Nyumbawo asaŵafunse kuti afotokoze za kamwazidwe ka ndalamazo, popeza kuti ndi anthu okhulupirika.”
8Tsono Hilikiya, mkulu wa nsembe uja, adauza Safani, mlembi uja, kuti, “Ndalipeza buku la Malamulo lija m'Nyumba ya Chauta.” Ndipo Hilikiya adapereka bukulo kwa Safani, iye naliŵerenga.
9Tsono Safani mlembi uja adapita kwa mfumu, nakafotokozera mfumuyo kuti, “Atumiki anu atenga ndalama zija zinali m'Nyumbazi, ndipo azipereka kwa anthu amene akuyang'anira ntchito yokonza Nyumba ya Mulungu.”
10Tsono Safani adauza mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsira buku.” Ndipo Safani adaliŵerenga bukulo pamaso pa mfumu.
Hulida mneneri wamkazi11Mfumu itamva mau a m'buku la Malamulo, idang'amba zovala zake mwachisoni.
12Pomwepo idalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Akibori mwana wa Mikaya, Safani mlembi uja ndi Asaya mtumiki wa mfumu, kuti,
13“Pitani mukafunse Chauta m'malo mwanga ndi m'malo mwa anthu a m'dziko lonse la Yuda, za mau a m'buku limene lapezekali. Ndithu mkwiyo wa Chauta umene watiyakirawu ngwaukulu, chifukwa choti makolo athu sadamvere mau a m'bukuli, ndipo sadatsate zonse zimene zidalembedwa m'menemo.”
14Motero wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani ndi Asaya adapita kwa mneneri wamkazi dzina lake Hulida, mkazi wa Salumu. Salumuyo, wosunga zovala zachifumu anali mwana wa Tikiwa, mwana wa Harihasi. Mkaziyu ankakhala ku Yerusalemu m'dera latsopano la mzindawo. Tsono anthu aja atalankhula naye,
15iyeyo adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Muuzeni munthu wakutumani kwa Ineyo kuti,
16Ine Chauta ndikuti, Ndidzabweretsa choipa pa mzinda uno ndi pa anthu onse am'menemo, potsata mau onse a m'buku limene mfumu ya ku Yuda idaliŵerenga.
17Chifukwa chakuti anthuwo andisiya Ine namafukiza lubani kwa milungu ina, nkumandichimwira ndi mafano ao, ntchito zonse za manja ao, Ine pano mkwiyo wanga wayakira mzinda uno ndipo sudzazima.
18Koma mfumu ya ku Yuda imene idakutumani kuti mukafunse Chauta, mukaiwuze kuti Ine Chauta Mulungu wa Aisraele ndikuti, Kumva wamvadi mauwo,
19pakuti mtima wako walapa ndipo wadzichepetsa pamaso pa Ine Chauta, utamva mau amene ndidalankhula otsutsa mzinda uno ndi anthu onse okhala m'menemo. Ndithudi mzinda uno udzakhala bwinja ndi malo otembereredwa. Popeza kuti wang'amba zovala zako numalira pamaso panga, Inenso ndamva pemphero lako, ndatero Ine Chauta.
20Nchifukwa chake Ine ndidzakutenga, iweyo ukalondole makolo ako ndipo udzaikidwa m'manda mwamtendere. Motero maso ako sadzaona zoipa zija zimene ndidzabweretsa pa mzinda uno.’ ” Tsono anthu aja adabwerera nakanena mau amenewo kwa mfumu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.